Isaiah 43 (BOGWICC)
1 Koma tsopano, Yehovaamene anakulenga, iwe Yakobo,amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,“Usaope, pakuti ndakuwombola;Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga. 2 Pamene ukuwoloka nyanja,ndidzakhala nawe;ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,sidzakukokolola.Pamene ukudutsa pa moto,sudzapsa;lawi la moto silidzakutentha. 3 Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe. 4 Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,ndipo chifukwa ndimakukonda,ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako. 5 Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo. 6 Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali,ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi; 7 onsewo amadziwika ndi dzina langa;ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga,ndinawawumba, inde ndinawapanga.” 8 Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya,anthu amene ali nawo makutu koma sakumva. 9 Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi,anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu.Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi?Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale?Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona,kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.” 10 Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga,ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha,kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha.Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina,ngakhale pambuyo pangasipadzakhalaponso wina.” 11 Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova,ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha. 12 Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa;ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu.Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova. 13 “Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse.Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga,ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.” 14 Yehova akuti,Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti,“Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babulonindi kukupulumutsani.Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. 15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja,Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.” 16 Yehovaanapanga njira pa nyanja,anapanga njira pakati pa madzi amphamvu. 17 Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo,gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu,ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukansoanazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti, 18 “Iwalani zinthu zakale;ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale. 19 Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano!Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona?Ine ndikulambula msewu mʼchipululundi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma. 20 Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzizinandilemekeza.Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowumakuti ndiwapatse madzi anthu angaosankhidwa. 21 Anthu amene ndinadziwumbira ndekhakuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine. 22 “Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo,munatopa nane, Inu Aisraeli. 23 Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza,kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu.Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudyakapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza. 24 Simunandigulire bango lonunkhirakapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu.Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anundipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu. 25 “Ine, Inetu, ndi amene ndimafafanizazolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini,ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu. 26 Mundikumbutse zakale,ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi;fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa. 27 Kholo lanu loyamba linachimwa;ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira. 28 Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero,ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwendi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”