Isaiah 44 (BOGWICC)
1 Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,Israeli, amene ndinakusankha. 2 Yehovaamene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,Yesuruni, amene ndinakusankha. 3 Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu. 4 Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwinondi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda. 5 Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli. 6 “Yehova Mfumundi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha. 7 Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule.Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwezimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale,ndi ziti zimene zidzachitike;inde, muloleni alosere zimene zikubwera. 8 Musanjenjemere, musachite mantha.Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe?Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.” 9 Onse amene amapanga mafano ngachabe,ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu.Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona;ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi. 10 Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano,limene silingamupindulire? 11 Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi;amisiri a mafano ndi anthu chabe.Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu;onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi. 12 Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulondipo amachiyika pa makala amoto;ndi dzanja lake lamphamvuamachisula pochimenya ndi nyundo.Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu;iye samwa madzi, ndipo amalefuka. 13 Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwendipo amajambula chithunzi ndi cholembera;amasema bwinobwino ndi chipangizo chakendipo amachiwongola bwino ndi chida chake.Amachipanga ngati munthu,munthu wake wokongolakuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo. 14 Amagwetsa mitengo ya mkungudza,mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundunʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango,ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula. 15 Mitengoyo munthu amachitako nkhuni;nthambi zina amasonkhera moto wowotha,amakolezera moto wophikira buledindi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza;iye amapanga fano ndi kumaligwadira. 16 Chigawo china cha mtengowo amasonkhera motowowotcherapo nyama imeneamadya, nakhuta.Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti,“Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.” 17 Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo;amaligwadira ndi kulipembedza.Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti,“Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.” 18 Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse;maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona,ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa. 19 Palibe amene amayima nʼkulingalira.Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti,chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto;pa makala ake ndinaphikira buledi,ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya.Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi.Kodi ndidzagwadira mtengo? 20 Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa;motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti,“Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?” 21 Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izipopeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli.Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga;iwe Israeli, sindidzakuyiwala. 22 Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo,ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa.Bwerera kwa Ine,popeza ndakupulumutsa.” 23 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi;fuwula, iwe dziko lapansi.Imbani nyimbo, inu mapiri,inu nkhalango ndi mitengo yonse,chifukwa Yehova wawombola Yakobo,waonetsa ulemerero wake mwa Israeli. 24 Yehova Mpulumutsi wanu, ameneanakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti: “Ine ndine Yehova,amene anapanga zinthu zonse,ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo,ndinayala ndekha dziko lapansi. 25 Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga,ndipo ndimapusitsa owombeza mawula.Ndimasokoneza anthu a nzeru,ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa. 26 Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki akendi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake. “Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu.Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso.Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso. 27 Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako. 28 Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna;iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ”