Isaiah 49 (BOGWICC)

1 Mverani Ine, inu anthu a pa zilumbatcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali:Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe,ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga. 2 Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa,anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake;Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwandipo anandibisa mʼchimake. 3 Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli.Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.” 4 Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchitondi kuwononga mphamvu zanga pachabe,koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova,ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.” 5 Yehova anandiwumba inemʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wakekuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iyendi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye,choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova,ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga. 6 Yehovayo tsono akuti,“Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga,kuti udzutse mafuko a Yakobondi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka.Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira,udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.” 7 Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula,Woyerayo wa Israeli akunena,amene mitundu ya anthu inamuda,amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti,“Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira.Akalonga nawonso adzagwada pansi.Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirikandi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.” 8 Yehova akuti,“Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha,ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza;ndinakusunga ndi kukusandutsakuti ukhale pangano kwa anthu,kuti dziko libwerere mwakalendi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso. 9 Ndidzawuza a mʼndende kuti atulukendi a mu mdima kuti aonekere poyera. “Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njirandi msipu pa mʼmalo owuma. 10 Iwo sadzamva njala kapena ludzu,kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza;chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolerandi kuwaperekeza ku akasupe a madzi. 11 Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo,ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza. 12 Taonani, anthu anga adzachokera kutali,ena kumpoto, ena kumadzulo,enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.” 13 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga;kondwera, iwe dziko lapansi;imbani nyimbo inu mapiri!Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika. 14 Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya,Ambuye wandiyiwala.” 15 “Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakuberendi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?Ngakhale iye angathe kuyiwala,Ine sindidzakuyiwala iwe! 16 Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;makoma ako ndimawaona nthawi zonse. 17 Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira,ndipo amene anakupasula akuchokapo. 18 Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼaneana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe.Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo,anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsachimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’ 19 “Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwandipo dziko lako ndi kusakazidwa,chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewerandipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali. 20 Ana obadwa nthawi yako yachisoniadzanena kuti,‘Malo ano atichepera,tipatse malo ena woti tikhalemo.’ 21 Tsono iwe udzadzifunsa kuti,‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa?Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena;ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa.Ndani anawalera ana amenewa?Ndinatsala ndekha,nanga awa, achokera kuti?’ ” 22 Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi,“Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere.Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere.Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawondipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo. 23 Mafumu adzakhala abambo wongokulerandipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera.Iwo adzagwetsa nkhopezawo pansi.Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova;iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.” 24 Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo,kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza? 25 Koma zimene Yehova akunena ndi izi,“Ankhondo adzawalanda amʼndende awo,ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo;ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu,ndipo ndidzapulumutsa ana anu. 26 Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe;adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo.Zikadzatero anthu onse adzadziwakuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu,Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”

In Other Versions

Isaiah 49 in the ANGEFD

Isaiah 49 in the ANTPNG2D

Isaiah 49 in the AS21

Isaiah 49 in the BAGH

Isaiah 49 in the BBPNG

Isaiah 49 in the BBT1E

Isaiah 49 in the BDS

Isaiah 49 in the BEV

Isaiah 49 in the BHAD

Isaiah 49 in the BIB

Isaiah 49 in the BLPT

Isaiah 49 in the BNT

Isaiah 49 in the BNTABOOT

Isaiah 49 in the BNTLV

Isaiah 49 in the BOATCB

Isaiah 49 in the BOATCB2

Isaiah 49 in the BOBCV

Isaiah 49 in the BOCNT

Isaiah 49 in the BOECS

Isaiah 49 in the BOHCB

Isaiah 49 in the BOHCV

Isaiah 49 in the BOHLNT

Isaiah 49 in the BOHNTLTAL

Isaiah 49 in the BOICB

Isaiah 49 in the BOILNTAP

Isaiah 49 in the BOITCV

Isaiah 49 in the BOKCV

Isaiah 49 in the BOKCV2

Isaiah 49 in the BOKHWOG

Isaiah 49 in the BOKSSV

Isaiah 49 in the BOLCB

Isaiah 49 in the BOLCB2

Isaiah 49 in the BOMCV

Isaiah 49 in the BONAV

Isaiah 49 in the BONCB

Isaiah 49 in the BONLT

Isaiah 49 in the BONUT2

Isaiah 49 in the BOPLNT

Isaiah 49 in the BOSCB

Isaiah 49 in the BOSNC

Isaiah 49 in the BOTLNT

Isaiah 49 in the BOVCB

Isaiah 49 in the BOYCB

Isaiah 49 in the BPBB

Isaiah 49 in the BPH

Isaiah 49 in the BSB

Isaiah 49 in the CCB

Isaiah 49 in the CUV

Isaiah 49 in the CUVS

Isaiah 49 in the DBT

Isaiah 49 in the DGDNT

Isaiah 49 in the DHNT

Isaiah 49 in the DNT

Isaiah 49 in the ELBE

Isaiah 49 in the EMTV

Isaiah 49 in the ESV

Isaiah 49 in the FBV

Isaiah 49 in the FEB

Isaiah 49 in the GGMNT

Isaiah 49 in the GNT

Isaiah 49 in the HARY

Isaiah 49 in the HNT

Isaiah 49 in the IRVA

Isaiah 49 in the IRVB

Isaiah 49 in the IRVG

Isaiah 49 in the IRVH

Isaiah 49 in the IRVK

Isaiah 49 in the IRVM

Isaiah 49 in the IRVM2

Isaiah 49 in the IRVO

Isaiah 49 in the IRVP

Isaiah 49 in the IRVT

Isaiah 49 in the IRVT2

Isaiah 49 in the IRVU

Isaiah 49 in the ISVN

Isaiah 49 in the JSNT

Isaiah 49 in the KAPI

Isaiah 49 in the KBT1ETNIK

Isaiah 49 in the KBV

Isaiah 49 in the KJV

Isaiah 49 in the KNFD

Isaiah 49 in the LBA

Isaiah 49 in the LBLA

Isaiah 49 in the LNT

Isaiah 49 in the LSV

Isaiah 49 in the MAAL

Isaiah 49 in the MBV

Isaiah 49 in the MBV2

Isaiah 49 in the MHNT

Isaiah 49 in the MKNFD

Isaiah 49 in the MNG

Isaiah 49 in the MNT

Isaiah 49 in the MNT2

Isaiah 49 in the MRS1T

Isaiah 49 in the NAA

Isaiah 49 in the NASB

Isaiah 49 in the NBLA

Isaiah 49 in the NBS

Isaiah 49 in the NBVTP

Isaiah 49 in the NET2

Isaiah 49 in the NIV11

Isaiah 49 in the NNT

Isaiah 49 in the NNT2

Isaiah 49 in the NNT3

Isaiah 49 in the PDDPT

Isaiah 49 in the PFNT

Isaiah 49 in the RMNT

Isaiah 49 in the SBIAS

Isaiah 49 in the SBIBS

Isaiah 49 in the SBIBS2

Isaiah 49 in the SBICS

Isaiah 49 in the SBIDS

Isaiah 49 in the SBIGS

Isaiah 49 in the SBIHS

Isaiah 49 in the SBIIS

Isaiah 49 in the SBIIS2

Isaiah 49 in the SBIIS3

Isaiah 49 in the SBIKS

Isaiah 49 in the SBIKS2

Isaiah 49 in the SBIMS

Isaiah 49 in the SBIOS

Isaiah 49 in the SBIPS

Isaiah 49 in the SBISS

Isaiah 49 in the SBITS

Isaiah 49 in the SBITS2

Isaiah 49 in the SBITS3

Isaiah 49 in the SBITS4

Isaiah 49 in the SBIUS

Isaiah 49 in the SBIVS

Isaiah 49 in the SBT

Isaiah 49 in the SBT1E

Isaiah 49 in the SCHL

Isaiah 49 in the SNT

Isaiah 49 in the SUSU

Isaiah 49 in the SUSU2

Isaiah 49 in the SYNO

Isaiah 49 in the TBIAOTANT

Isaiah 49 in the TBT1E

Isaiah 49 in the TBT1E2

Isaiah 49 in the TFTIP

Isaiah 49 in the TFTU

Isaiah 49 in the TGNTATF3T

Isaiah 49 in the THAI

Isaiah 49 in the TNFD

Isaiah 49 in the TNT

Isaiah 49 in the TNTIK

Isaiah 49 in the TNTIL

Isaiah 49 in the TNTIN

Isaiah 49 in the TNTIP

Isaiah 49 in the TNTIZ

Isaiah 49 in the TOMA

Isaiah 49 in the TTENT

Isaiah 49 in the UBG

Isaiah 49 in the UGV

Isaiah 49 in the UGV2

Isaiah 49 in the UGV3

Isaiah 49 in the VBL

Isaiah 49 in the VDCC

Isaiah 49 in the YALU

Isaiah 49 in the YAPE

Isaiah 49 in the YBVTP

Isaiah 49 in the ZBP