Isaiah 7 (BOGWICC)

1 Pamene Ahazi mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya anali mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, koma sanathe kuwugonjetsa. 2 Tsono nyumba ya Davide inawuzidwa kuti, “Dziko la Siriya lagwirizana ndi Efereimu.” Choncho mfumu Ahazi ndi anthu ake ananjenjemera, monga momwe mitengo ya mʼnkhalango imagwedezekera ndi mphepo. 3 Pamenepo Yehova anawuza Yesaya kuti, “Tuluka, iwe ndi mwana wako Seariyasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu wopita ku Munda wa mmisiri wochapa nsalu. 4 Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. 5 Mfumu ya Siriya, Efereimu ndi mwana wa Remaliya apangana kuti akuchitire choyipa. Akunena kuti, 6 ‘Tiyeni tikalimbane ndi Yuda. Tiyeni tiliwononge ndi kuligawa; tiligawane pakati pathu, ndipo tilonge ufumu mwana wa Tabeeli kumeneko.’ 7 Komabe zimene akunena Ambuye Yehova ndi izi:“ ‘Zimenezo sizidzatheka,sizidzachitika konse, 8 pakuti Siriya amadalira Damasiko,ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi.Zisanathe zaka 65Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu. 9 Dziko la Efereimu limadalira Samariyandipo Samariya amadalira mwana wa Remaliya basi.Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu,ndithu simudzalimba konse.’ ” 10 Yehova anayankhulanso ndi Ahazi, 11 “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.” 12 Koma Ahazi anati, “Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova.” 13 Apo Yesaya anati, “Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga? 14 Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli. 15 Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino. 16 Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja. 17 Yehova adzabweretsa pa inu, pa anthu anu ndiponso pa nyumba ya bambo wanu masiku a mavuto woti sanakhalepo kuyambira tsiku limene Efereimu anapatukana ndi Yuda. Yehova adzabweretsa mfumu ya ku Asiriya.” 18 Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya. 19 Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika mu zigwa zozama, mʼmingʼalu ya matanthwe ndi mʼzitsamba zonse zaminga ndiponso ponse pamene pali malo omwetsera ziweto. 20 Tsiku limenelo Ambuye adzalemba ganyu ometa ochokera kutsidya kwa Mtsinje, ndiye mfumu ya ku Asiriya, kudzameta tsitsi lanu la ku mutu ndi la mʼmiyendo ndi ndevu zomwe. 21 Tsiku limenelo adzangosunga ngʼombe yayikazi yayingʼono ndi mbuzi ziwiri. 22 Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene ziwetozi zidzapereka, munthuyo azidzadya chambiko. Aliyense amene adzatsalire mʼdzikomo azidzadya chambiko ndi uchi. 23 Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga. 24 Anthu adzapita kumeneko kukachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti mʼdziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga. 25 Ndipo mʼmapiri monse mʼmene kale munkalimidwa ndi khasu, simudzapitamo kuopa mkandankhuku ndi minga; malowo adzasanduka odyetserako ngʼombe ndi nkhosa.

In Other Versions

Isaiah 7 in the ANGEFD

Isaiah 7 in the ANTPNG2D

Isaiah 7 in the AS21

Isaiah 7 in the BAGH

Isaiah 7 in the BBPNG

Isaiah 7 in the BBT1E

Isaiah 7 in the BDS

Isaiah 7 in the BEV

Isaiah 7 in the BHAD

Isaiah 7 in the BIB

Isaiah 7 in the BLPT

Isaiah 7 in the BNT

Isaiah 7 in the BNTABOOT

Isaiah 7 in the BNTLV

Isaiah 7 in the BOATCB

Isaiah 7 in the BOATCB2

Isaiah 7 in the BOBCV

Isaiah 7 in the BOCNT

Isaiah 7 in the BOECS

Isaiah 7 in the BOHCB

Isaiah 7 in the BOHCV

Isaiah 7 in the BOHLNT

Isaiah 7 in the BOHNTLTAL

Isaiah 7 in the BOICB

Isaiah 7 in the BOILNTAP

Isaiah 7 in the BOITCV

Isaiah 7 in the BOKCV

Isaiah 7 in the BOKCV2

Isaiah 7 in the BOKHWOG

Isaiah 7 in the BOKSSV

Isaiah 7 in the BOLCB

Isaiah 7 in the BOLCB2

Isaiah 7 in the BOMCV

Isaiah 7 in the BONAV

Isaiah 7 in the BONCB

Isaiah 7 in the BONLT

Isaiah 7 in the BONUT2

Isaiah 7 in the BOPLNT

Isaiah 7 in the BOSCB

Isaiah 7 in the BOSNC

Isaiah 7 in the BOTLNT

Isaiah 7 in the BOVCB

Isaiah 7 in the BOYCB

Isaiah 7 in the BPBB

Isaiah 7 in the BPH

Isaiah 7 in the BSB

Isaiah 7 in the CCB

Isaiah 7 in the CUV

Isaiah 7 in the CUVS

Isaiah 7 in the DBT

Isaiah 7 in the DGDNT

Isaiah 7 in the DHNT

Isaiah 7 in the DNT

Isaiah 7 in the ELBE

Isaiah 7 in the EMTV

Isaiah 7 in the ESV

Isaiah 7 in the FBV

Isaiah 7 in the FEB

Isaiah 7 in the GGMNT

Isaiah 7 in the GNT

Isaiah 7 in the HARY

Isaiah 7 in the HNT

Isaiah 7 in the IRVA

Isaiah 7 in the IRVB

Isaiah 7 in the IRVG

Isaiah 7 in the IRVH

Isaiah 7 in the IRVK

Isaiah 7 in the IRVM

Isaiah 7 in the IRVM2

Isaiah 7 in the IRVO

Isaiah 7 in the IRVP

Isaiah 7 in the IRVT

Isaiah 7 in the IRVT2

Isaiah 7 in the IRVU

Isaiah 7 in the ISVN

Isaiah 7 in the JSNT

Isaiah 7 in the KAPI

Isaiah 7 in the KBT1ETNIK

Isaiah 7 in the KBV

Isaiah 7 in the KJV

Isaiah 7 in the KNFD

Isaiah 7 in the LBA

Isaiah 7 in the LBLA

Isaiah 7 in the LNT

Isaiah 7 in the LSV

Isaiah 7 in the MAAL

Isaiah 7 in the MBV

Isaiah 7 in the MBV2

Isaiah 7 in the MHNT

Isaiah 7 in the MKNFD

Isaiah 7 in the MNG

Isaiah 7 in the MNT

Isaiah 7 in the MNT2

Isaiah 7 in the MRS1T

Isaiah 7 in the NAA

Isaiah 7 in the NASB

Isaiah 7 in the NBLA

Isaiah 7 in the NBS

Isaiah 7 in the NBVTP

Isaiah 7 in the NET2

Isaiah 7 in the NIV11

Isaiah 7 in the NNT

Isaiah 7 in the NNT2

Isaiah 7 in the NNT3

Isaiah 7 in the PDDPT

Isaiah 7 in the PFNT

Isaiah 7 in the RMNT

Isaiah 7 in the SBIAS

Isaiah 7 in the SBIBS

Isaiah 7 in the SBIBS2

Isaiah 7 in the SBICS

Isaiah 7 in the SBIDS

Isaiah 7 in the SBIGS

Isaiah 7 in the SBIHS

Isaiah 7 in the SBIIS

Isaiah 7 in the SBIIS2

Isaiah 7 in the SBIIS3

Isaiah 7 in the SBIKS

Isaiah 7 in the SBIKS2

Isaiah 7 in the SBIMS

Isaiah 7 in the SBIOS

Isaiah 7 in the SBIPS

Isaiah 7 in the SBISS

Isaiah 7 in the SBITS

Isaiah 7 in the SBITS2

Isaiah 7 in the SBITS3

Isaiah 7 in the SBITS4

Isaiah 7 in the SBIUS

Isaiah 7 in the SBIVS

Isaiah 7 in the SBT

Isaiah 7 in the SBT1E

Isaiah 7 in the SCHL

Isaiah 7 in the SNT

Isaiah 7 in the SUSU

Isaiah 7 in the SUSU2

Isaiah 7 in the SYNO

Isaiah 7 in the TBIAOTANT

Isaiah 7 in the TBT1E

Isaiah 7 in the TBT1E2

Isaiah 7 in the TFTIP

Isaiah 7 in the TFTU

Isaiah 7 in the TGNTATF3T

Isaiah 7 in the THAI

Isaiah 7 in the TNFD

Isaiah 7 in the TNT

Isaiah 7 in the TNTIK

Isaiah 7 in the TNTIL

Isaiah 7 in the TNTIN

Isaiah 7 in the TNTIP

Isaiah 7 in the TNTIZ

Isaiah 7 in the TOMA

Isaiah 7 in the TTENT

Isaiah 7 in the UBG

Isaiah 7 in the UGV

Isaiah 7 in the UGV2

Isaiah 7 in the UGV3

Isaiah 7 in the VBL

Isaiah 7 in the VDCC

Isaiah 7 in the YALU

Isaiah 7 in the YAPE

Isaiah 7 in the YBVTP

Isaiah 7 in the ZBP