James 1 (BOGWICC)
1 Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu,kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana.Landirani moni. 2 Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. 3 Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. 4 Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse. 5 Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. 6 Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. 7 Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. 8 Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita. 9 Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. 10 Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. 11 Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake. 12 Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda. 13 Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. 14 Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. 15 Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa. 16 Musanyengedwe abale anga okondedwa. 17 Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. 18 Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba. 19 Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. 20 Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. 21 Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani. 22 Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. 23 Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. 24 Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera. 25 Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita. 26 Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe. 27 Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.
In Other Versions
James 1 in the ANGEFD
James 1 in the ANTPNG2D
James 1 in the AS21
James 1 in the BAGH
James 1 in the BBPNG
James 1 in the BBT1E
James 1 in the BDS
James 1 in the BEV
James 1 in the BHAD
James 1 in the BIB
James 1 in the BLPT
James 1 in the BNT
James 1 in the BNTABOOT
James 1 in the BNTLV
James 1 in the BOATCB
James 1 in the BOATCB2
James 1 in the BOBCV
James 1 in the BOCNT
James 1 in the BOECS
James 1 in the BOHCB
James 1 in the BOHCV
James 1 in the BOHLNT
James 1 in the BOHNTLTAL
James 1 in the BOICB
James 1 in the BOILNTAP
James 1 in the BOITCV
James 1 in the BOKCV
James 1 in the BOKCV2
James 1 in the BOKHWOG
James 1 in the BOKSSV
James 1 in the BOLCB
James 1 in the BOLCB2
James 1 in the BOMCV
James 1 in the BONAV
James 1 in the BONCB
James 1 in the BONLT
James 1 in the BONUT2
James 1 in the BOPLNT
James 1 in the BOSCB
James 1 in the BOSNC
James 1 in the BOTLNT
James 1 in the BOVCB
James 1 in the BOYCB
James 1 in the BPBB
James 1 in the BPH
James 1 in the BSB
James 1 in the CCB
James 1 in the CUV
James 1 in the CUVS
James 1 in the DBT
James 1 in the DGDNT
James 1 in the DHNT
James 1 in the DNT
James 1 in the ELBE
James 1 in the EMTV
James 1 in the ESV
James 1 in the FBV
James 1 in the FEB
James 1 in the GGMNT
James 1 in the GNT
James 1 in the HARY
James 1 in the HNT
James 1 in the IRVA
James 1 in the IRVB
James 1 in the IRVG
James 1 in the IRVH
James 1 in the IRVK
James 1 in the IRVM
James 1 in the IRVM2
James 1 in the IRVO
James 1 in the IRVP
James 1 in the IRVT
James 1 in the IRVT2
James 1 in the IRVU
James 1 in the ISVN
James 1 in the JSNT
James 1 in the KAPI
James 1 in the KBT1ETNIK
James 1 in the KBV
James 1 in the KJV
James 1 in the KNFD
James 1 in the LBA
James 1 in the LBLA
James 1 in the LNT
James 1 in the LSV
James 1 in the MAAL
James 1 in the MBV
James 1 in the MBV2
James 1 in the MHNT
James 1 in the MKNFD
James 1 in the MNG
James 1 in the MNT
James 1 in the MNT2
James 1 in the MRS1T
James 1 in the NAA
James 1 in the NASB
James 1 in the NBLA
James 1 in the NBS
James 1 in the NBVTP
James 1 in the NET2
James 1 in the NIV11
James 1 in the NNT
James 1 in the NNT2
James 1 in the NNT3
James 1 in the PDDPT
James 1 in the PFNT
James 1 in the RMNT
James 1 in the SBIAS
James 1 in the SBIBS
James 1 in the SBIBS2
James 1 in the SBICS
James 1 in the SBIDS
James 1 in the SBIGS
James 1 in the SBIHS
James 1 in the SBIIS
James 1 in the SBIIS2
James 1 in the SBIIS3
James 1 in the SBIKS
James 1 in the SBIKS2
James 1 in the SBIMS
James 1 in the SBIOS
James 1 in the SBIPS
James 1 in the SBISS
James 1 in the SBITS
James 1 in the SBITS2
James 1 in the SBITS3
James 1 in the SBITS4
James 1 in the SBIUS
James 1 in the SBIVS
James 1 in the SBT
James 1 in the SBT1E
James 1 in the SCHL
James 1 in the SNT
James 1 in the SUSU
James 1 in the SUSU2
James 1 in the SYNO
James 1 in the TBIAOTANT
James 1 in the TBT1E
James 1 in the TBT1E2
James 1 in the TFTIP
James 1 in the TFTU
James 1 in the TGNTATF3T
James 1 in the THAI
James 1 in the TNFD
James 1 in the TNT
James 1 in the TNTIK
James 1 in the TNTIL
James 1 in the TNTIN
James 1 in the TNTIP
James 1 in the TNTIZ
James 1 in the TOMA
James 1 in the TTENT
James 1 in the UBG
James 1 in the UGV
James 1 in the UGV2
James 1 in the UGV3
James 1 in the VBL
James 1 in the VDCC
James 1 in the YALU
James 1 in the YAPE
James 1 in the YBVTP
James 1 in the ZBP