Jeremiah 19 (BOGWICC)
1 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukagule mʼphika wadothi kwa munthu wowumba. Utenge akuluakulu ena a anthuwa ndi ansembe 2 ndipo mupite ku Chigwa cha Hinomu chimene chili pafupi ndi pa chipata cha mapale. Pamenepo ukalengeze mawu amene ndikakuwuze. 3 Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka. 4 Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa. 5 Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira. 6 Nʼchifukwa chake taonani, masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzatchulanso malo ano kuti Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma Chophera anthu. 7 “ ‘Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Ndidzachititsa kuti adani awo awaphe ku nkhondo. Ndidzawakanthitsa kwa anthu amene akuwazonda. Mitembo yawo ndidzayipereka kwa mbalame za mlengalenga ndi zirombo za kutchire kuti ikhale chakudya chawo. 8 Mzinda uno ndidzawusakaza ndi kuwusandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyansa. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake. 9 Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’ 10 “Tsono iwe udzaphwanye mtsukowo anthu amene udzapite nawowo akuona, 11 ndipo ukawawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndidzaphwanya dziko lino ndi mzinda uno ngati momwe wowumba amaphwanyira mbiya yake ndipo sangathe kuyikonzanso. Adzayika anthu akufa ku Tofeti chifukwa padzasowa malo ena owayika. 12 Umu ndi mmene ndidzachitire ndi malo ano pamodzi ndi anthu okhalamo, akutero Yehova. Ndidzasandutsa mzindawu kukhala ngati Tofeti. 13 Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ” 14 Kenaka Yeremiya anabwerako ku Tofeti, kumene Yehova anamutuma kuti akanenere, nakayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Yehova ndi kuwawuza anthu kuti, 15 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ”
In Other Versions
Jeremiah 19 in the ANGEFD
Jeremiah 19 in the ANTPNG2D
Jeremiah 19 in the AS21
Jeremiah 19 in the BAGH
Jeremiah 19 in the BBPNG
Jeremiah 19 in the BBT1E
Jeremiah 19 in the BDS
Jeremiah 19 in the BEV
Jeremiah 19 in the BHAD
Jeremiah 19 in the BIB
Jeremiah 19 in the BLPT
Jeremiah 19 in the BNT
Jeremiah 19 in the BNTABOOT
Jeremiah 19 in the BNTLV
Jeremiah 19 in the BOATCB
Jeremiah 19 in the BOATCB2
Jeremiah 19 in the BOBCV
Jeremiah 19 in the BOCNT
Jeremiah 19 in the BOECS
Jeremiah 19 in the BOHCB
Jeremiah 19 in the BOHCV
Jeremiah 19 in the BOHLNT
Jeremiah 19 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 19 in the BOICB
Jeremiah 19 in the BOILNTAP
Jeremiah 19 in the BOITCV
Jeremiah 19 in the BOKCV
Jeremiah 19 in the BOKCV2
Jeremiah 19 in the BOKHWOG
Jeremiah 19 in the BOKSSV
Jeremiah 19 in the BOLCB
Jeremiah 19 in the BOLCB2
Jeremiah 19 in the BOMCV
Jeremiah 19 in the BONAV
Jeremiah 19 in the BONCB
Jeremiah 19 in the BONLT
Jeremiah 19 in the BONUT2
Jeremiah 19 in the BOPLNT
Jeremiah 19 in the BOSCB
Jeremiah 19 in the BOSNC
Jeremiah 19 in the BOTLNT
Jeremiah 19 in the BOVCB
Jeremiah 19 in the BOYCB
Jeremiah 19 in the BPBB
Jeremiah 19 in the BPH
Jeremiah 19 in the BSB
Jeremiah 19 in the CCB
Jeremiah 19 in the CUV
Jeremiah 19 in the CUVS
Jeremiah 19 in the DBT
Jeremiah 19 in the DGDNT
Jeremiah 19 in the DHNT
Jeremiah 19 in the DNT
Jeremiah 19 in the ELBE
Jeremiah 19 in the EMTV
Jeremiah 19 in the ESV
Jeremiah 19 in the FBV
Jeremiah 19 in the FEB
Jeremiah 19 in the GGMNT
Jeremiah 19 in the GNT
Jeremiah 19 in the HARY
Jeremiah 19 in the HNT
Jeremiah 19 in the IRVA
Jeremiah 19 in the IRVB
Jeremiah 19 in the IRVG
Jeremiah 19 in the IRVH
Jeremiah 19 in the IRVK
Jeremiah 19 in the IRVM
Jeremiah 19 in the IRVM2
Jeremiah 19 in the IRVO
Jeremiah 19 in the IRVP
Jeremiah 19 in the IRVT
Jeremiah 19 in the IRVT2
Jeremiah 19 in the IRVU
Jeremiah 19 in the ISVN
Jeremiah 19 in the JSNT
Jeremiah 19 in the KAPI
Jeremiah 19 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 19 in the KBV
Jeremiah 19 in the KJV
Jeremiah 19 in the KNFD
Jeremiah 19 in the LBA
Jeremiah 19 in the LBLA
Jeremiah 19 in the LNT
Jeremiah 19 in the LSV
Jeremiah 19 in the MAAL
Jeremiah 19 in the MBV
Jeremiah 19 in the MBV2
Jeremiah 19 in the MHNT
Jeremiah 19 in the MKNFD
Jeremiah 19 in the MNG
Jeremiah 19 in the MNT
Jeremiah 19 in the MNT2
Jeremiah 19 in the MRS1T
Jeremiah 19 in the NAA
Jeremiah 19 in the NASB
Jeremiah 19 in the NBLA
Jeremiah 19 in the NBS
Jeremiah 19 in the NBVTP
Jeremiah 19 in the NET2
Jeremiah 19 in the NIV11
Jeremiah 19 in the NNT
Jeremiah 19 in the NNT2
Jeremiah 19 in the NNT3
Jeremiah 19 in the PDDPT
Jeremiah 19 in the PFNT
Jeremiah 19 in the RMNT
Jeremiah 19 in the SBIAS
Jeremiah 19 in the SBIBS
Jeremiah 19 in the SBIBS2
Jeremiah 19 in the SBICS
Jeremiah 19 in the SBIDS
Jeremiah 19 in the SBIGS
Jeremiah 19 in the SBIHS
Jeremiah 19 in the SBIIS
Jeremiah 19 in the SBIIS2
Jeremiah 19 in the SBIIS3
Jeremiah 19 in the SBIKS
Jeremiah 19 in the SBIKS2
Jeremiah 19 in the SBIMS
Jeremiah 19 in the SBIOS
Jeremiah 19 in the SBIPS
Jeremiah 19 in the SBISS
Jeremiah 19 in the SBITS
Jeremiah 19 in the SBITS2
Jeremiah 19 in the SBITS3
Jeremiah 19 in the SBITS4
Jeremiah 19 in the SBIUS
Jeremiah 19 in the SBIVS
Jeremiah 19 in the SBT
Jeremiah 19 in the SBT1E
Jeremiah 19 in the SCHL
Jeremiah 19 in the SNT
Jeremiah 19 in the SUSU
Jeremiah 19 in the SUSU2
Jeremiah 19 in the SYNO
Jeremiah 19 in the TBIAOTANT
Jeremiah 19 in the TBT1E
Jeremiah 19 in the TBT1E2
Jeremiah 19 in the TFTIP
Jeremiah 19 in the TFTU
Jeremiah 19 in the TGNTATF3T
Jeremiah 19 in the THAI
Jeremiah 19 in the TNFD
Jeremiah 19 in the TNT
Jeremiah 19 in the TNTIK
Jeremiah 19 in the TNTIL
Jeremiah 19 in the TNTIN
Jeremiah 19 in the TNTIP
Jeremiah 19 in the TNTIZ
Jeremiah 19 in the TOMA
Jeremiah 19 in the TTENT
Jeremiah 19 in the UBG
Jeremiah 19 in the UGV
Jeremiah 19 in the UGV2
Jeremiah 19 in the UGV3
Jeremiah 19 in the VBL
Jeremiah 19 in the VDCC
Jeremiah 19 in the YALU
Jeremiah 19 in the YAPE
Jeremiah 19 in the YBVTP
Jeremiah 19 in the ZBP