Jeremiah 2 (BOGWICC)

1 Yehova anandiwuza kuti, 2 “Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti,“ ‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako,mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi,mmene unkanditsata mʼchipululu muja;mʼdziko losadzalamo kanthu. 3 Israeli anali wopatulika wa Yehova,anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola;onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwandipo mavuto anawagwera,’ ”akutero Yehova. 4 Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo,inu mafuko onse a Israeli. 5 Yehova akuti,“Kodi makolo anu anandipeza nʼcholakwa chanji,kuti andithawe?Iwo anatsata milungu yachabechabe,nawonso nʼkusanduka achabechabe. 6 Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti,amene anatitulutsa mʼdziko la Iguptonatitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowumandi lokumbikakumbika,mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima,dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’ 7 Ndinakufikitsani ku dziko lachondekuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina.Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langandi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa. 8 Ansembe nawonso sanafunse kuti,‘Yehova ali kuti?’Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe;atsogoleri anandiwukira.Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala,ndi kutsatira mafano achabechabe. 9 “Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,”akutero Yehova.“Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu. 10 Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone,tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino;ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe: 11 Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene unasinthapo milungu yake?(Ngakhale kuti si milungu nʼkomwe).Koma anthu anga asinthitsa Mulungu wawo waulemererondi mafano achabechabe. 12 Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi,ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,”akutero Yehova. 13 “Popeza anthu anga achita machimo awiri:Andisiya Inekasupe wa madzi a moyo,ndi kukadzikumbira zitsime zawo,zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi. 14 Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi.Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere? 15 Adani ake abangulirandi kumuopseza ngati mikango.Dziko lake analisandutsa bwinja;mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo. 16 Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesiakuphwanyani mitu. 17 Zimenezitu zakuchitikiranichifukwa munasiya Yehova Mulungu wanupamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu? 18 Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto,kukamwa madzi a mu Sihori?Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya,kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate? 19 Kuyipa kwanuko kudzakulangani;kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani.Tsono ganizirani bwino,popeza ndi chinthu choyipakundisiya Ine Yehova Mulungu wanu;ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu.Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse. 20 “Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanundi kudula msinga zanu;munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere.Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitalindiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 21 Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika;unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika.Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesawachabechabe wonga wa kutchire? 22 Ngakhale utasamba ndi sodakapena kusambira sopo wambiri,kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,”akutero Ambuye Yehova. 23 “Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse;sindinatsatire Abaala’?Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja;zindikira bwino zomwe wachita.Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiroyomangothamanga uku ndi uku, 24 wakhala ngati mbidzi yozolowera mʼchipululu,yonka ninunkhiza pa nthawi yachisika.Ndani angayiretse chilakolako chakecho?Mphongo iliyonse yoyikhumba sidzavutika.Pa nthawi yachisika chakecho mphongoyo idzayipeza. 25 Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazindi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu.Koma unati, ‘Zamkutu!Ine ndimakonda milungu yachilendo,ndipo ndidzayitsatira.’ 26 “Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa,moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi;Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo,ansembe ndi aneneri awo. 27 Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’Iwo andifulatira Ine,ndipo safuna kundiyangʼana;Koma akakhala pa mavuto amati,‘Bwerani mudzatipulumutse!’ 28 Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha?Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsanipamene muli pamavuto!Inu anthu a ku Yuda,milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu. 29 “Kodi mukundizengeranji mlandu?Nonse mwandiwukira,”akutero Yehova. 30 “Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu;iwo sanaphunzirepo kanthu.Monga mkango wolusa,lupanga lanu lapha aneneri anu. 31 “Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova:“Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israelikapena ngati dziko la mdima wandiweyani?Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda;sitidzabweranso kwa Inu’? 32 Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake,kapena kuyiwala zovala zake za ukwati?Komatu anthu anga andiyiwalamasiku osawerengeka. 33 Mumadziwa bwino njira zopezera zibwenzi!Choncho ngakhale akazi oyipa omwe mumawaphunzitsa njira zanu. 34 Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapomagazi a anthu osauka osalakwa.Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba.Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi, 35 inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa,sadzatikwiyira.’Ndidzakuyimbani mlanduchifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’ 36 Chifukwa chiyanimukunkabe nimusinthasintha njira zanu?Aigupto adzakukhumudwitsanimonga momwe Asiriya anakuchititsani manyazi. 37 Mudzachokanso kumenekomanja ali kunkhongo.Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira,choncho sadzakuthandizani konse.

In Other Versions

Jeremiah 2 in the ANGEFD

Jeremiah 2 in the ANTPNG2D

Jeremiah 2 in the AS21

Jeremiah 2 in the BAGH

Jeremiah 2 in the BBPNG

Jeremiah 2 in the BBT1E

Jeremiah 2 in the BDS

Jeremiah 2 in the BEV

Jeremiah 2 in the BHAD

Jeremiah 2 in the BIB

Jeremiah 2 in the BLPT

Jeremiah 2 in the BNT

Jeremiah 2 in the BNTABOOT

Jeremiah 2 in the BNTLV

Jeremiah 2 in the BOATCB

Jeremiah 2 in the BOATCB2

Jeremiah 2 in the BOBCV

Jeremiah 2 in the BOCNT

Jeremiah 2 in the BOECS

Jeremiah 2 in the BOHCB

Jeremiah 2 in the BOHCV

Jeremiah 2 in the BOHLNT

Jeremiah 2 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 2 in the BOICB

Jeremiah 2 in the BOILNTAP

Jeremiah 2 in the BOITCV

Jeremiah 2 in the BOKCV

Jeremiah 2 in the BOKCV2

Jeremiah 2 in the BOKHWOG

Jeremiah 2 in the BOKSSV

Jeremiah 2 in the BOLCB

Jeremiah 2 in the BOLCB2

Jeremiah 2 in the BOMCV

Jeremiah 2 in the BONAV

Jeremiah 2 in the BONCB

Jeremiah 2 in the BONLT

Jeremiah 2 in the BONUT2

Jeremiah 2 in the BOPLNT

Jeremiah 2 in the BOSCB

Jeremiah 2 in the BOSNC

Jeremiah 2 in the BOTLNT

Jeremiah 2 in the BOVCB

Jeremiah 2 in the BOYCB

Jeremiah 2 in the BPBB

Jeremiah 2 in the BPH

Jeremiah 2 in the BSB

Jeremiah 2 in the CCB

Jeremiah 2 in the CUV

Jeremiah 2 in the CUVS

Jeremiah 2 in the DBT

Jeremiah 2 in the DGDNT

Jeremiah 2 in the DHNT

Jeremiah 2 in the DNT

Jeremiah 2 in the ELBE

Jeremiah 2 in the EMTV

Jeremiah 2 in the ESV

Jeremiah 2 in the FBV

Jeremiah 2 in the FEB

Jeremiah 2 in the GGMNT

Jeremiah 2 in the GNT

Jeremiah 2 in the HARY

Jeremiah 2 in the HNT

Jeremiah 2 in the IRVA

Jeremiah 2 in the IRVB

Jeremiah 2 in the IRVG

Jeremiah 2 in the IRVH

Jeremiah 2 in the IRVK

Jeremiah 2 in the IRVM

Jeremiah 2 in the IRVM2

Jeremiah 2 in the IRVO

Jeremiah 2 in the IRVP

Jeremiah 2 in the IRVT

Jeremiah 2 in the IRVT2

Jeremiah 2 in the IRVU

Jeremiah 2 in the ISVN

Jeremiah 2 in the JSNT

Jeremiah 2 in the KAPI

Jeremiah 2 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 2 in the KBV

Jeremiah 2 in the KJV

Jeremiah 2 in the KNFD

Jeremiah 2 in the LBA

Jeremiah 2 in the LBLA

Jeremiah 2 in the LNT

Jeremiah 2 in the LSV

Jeremiah 2 in the MAAL

Jeremiah 2 in the MBV

Jeremiah 2 in the MBV2

Jeremiah 2 in the MHNT

Jeremiah 2 in the MKNFD

Jeremiah 2 in the MNG

Jeremiah 2 in the MNT

Jeremiah 2 in the MNT2

Jeremiah 2 in the MRS1T

Jeremiah 2 in the NAA

Jeremiah 2 in the NASB

Jeremiah 2 in the NBLA

Jeremiah 2 in the NBS

Jeremiah 2 in the NBVTP

Jeremiah 2 in the NET2

Jeremiah 2 in the NIV11

Jeremiah 2 in the NNT

Jeremiah 2 in the NNT2

Jeremiah 2 in the NNT3

Jeremiah 2 in the PDDPT

Jeremiah 2 in the PFNT

Jeremiah 2 in the RMNT

Jeremiah 2 in the SBIAS

Jeremiah 2 in the SBIBS

Jeremiah 2 in the SBIBS2

Jeremiah 2 in the SBICS

Jeremiah 2 in the SBIDS

Jeremiah 2 in the SBIGS

Jeremiah 2 in the SBIHS

Jeremiah 2 in the SBIIS

Jeremiah 2 in the SBIIS2

Jeremiah 2 in the SBIIS3

Jeremiah 2 in the SBIKS

Jeremiah 2 in the SBIKS2

Jeremiah 2 in the SBIMS

Jeremiah 2 in the SBIOS

Jeremiah 2 in the SBIPS

Jeremiah 2 in the SBISS

Jeremiah 2 in the SBITS

Jeremiah 2 in the SBITS2

Jeremiah 2 in the SBITS3

Jeremiah 2 in the SBITS4

Jeremiah 2 in the SBIUS

Jeremiah 2 in the SBIVS

Jeremiah 2 in the SBT

Jeremiah 2 in the SBT1E

Jeremiah 2 in the SCHL

Jeremiah 2 in the SNT

Jeremiah 2 in the SUSU

Jeremiah 2 in the SUSU2

Jeremiah 2 in the SYNO

Jeremiah 2 in the TBIAOTANT

Jeremiah 2 in the TBT1E

Jeremiah 2 in the TBT1E2

Jeremiah 2 in the TFTIP

Jeremiah 2 in the TFTU

Jeremiah 2 in the TGNTATF3T

Jeremiah 2 in the THAI

Jeremiah 2 in the TNFD

Jeremiah 2 in the TNT

Jeremiah 2 in the TNTIK

Jeremiah 2 in the TNTIL

Jeremiah 2 in the TNTIN

Jeremiah 2 in the TNTIP

Jeremiah 2 in the TNTIZ

Jeremiah 2 in the TOMA

Jeremiah 2 in the TTENT

Jeremiah 2 in the UBG

Jeremiah 2 in the UGV

Jeremiah 2 in the UGV2

Jeremiah 2 in the UGV3

Jeremiah 2 in the VBL

Jeremiah 2 in the VDCC

Jeremiah 2 in the YALU

Jeremiah 2 in the YAPE

Jeremiah 2 in the YBVTP

Jeremiah 2 in the ZBP