Jeremiah 26 (BOGWICC)

1 Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda atayamba kulamulira, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2 “Kayime mʼbwalo la Nyumba ya Yehova. Ndipo ukayankhule kwa anthu onse okhala mʼmizinda ya ku Yuda amene amabwera kudzapembedza ku Nyumba ya Yehova. Ukawawuze zonse zomwe ndakulamula; usakasiyeko ndi mawu amodzi omwe. 3 Mwina mwake adzamvera, ndipo aliyense adzatembenuka kuleka njira yake yoyipa. Ndiye ine ndidzaleka osapatsa chilango chimene ndinakonzekera kuti ndiwalange nacho chifukwa cha ntchito zawo zoyipa. 4 Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani, 5 ndipo ngati simumvera mawu a atumiki anga, aneneri amene ndakhala ndikukutumizirani, ngakhale kuti simunawamvere, 6 ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ” 7 Ansembe, aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya akuyankhula mawu amenewa mʼNyumba ya Yehova. 8 Yeremiya atangotsiriza kuwawuza anthu aja zonse zimene Yehova anamulamula kuti ayankhule, ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse anamugwira ndipo anati, “Uyenera kuphedwa! 9 Chifukwa chiyani walosera mʼdzina la Yehova kuti Nyumba ino idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala wopanda anthu ngati chipululu?” Anthu onse anamuzungulira Yeremiya mʼNyumba ya Yehova. 10 Koma nduna za ku Yuda zitamva zomwe zinachitikazi, zinanyamuka kuchokera ku nyumba yaufumu kupita ku Nyumba ya Yehova, nakakhala pamalo pawo, pa Chipata Chatsopano cha Nyumba ya Yehova. 11 Pamenepo ansembe ndi aneneri anawuza ndunazo pamodzi ndi anthu onse kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa chifukwa amalosera zoyipira mzinda uno. Inu mwadzimvera nokha zimenezi!” 12 Ndipo Yeremiya anawuza nduna zija ndi anthu onse kuti, “Yehova anandituma kunenera mawu onse amene mwawamva otsutsa Nyumba ino ndi mzinda uno. 13 Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu ndipo mverani Yehova Mulungu wanu. Mukatero ndiye kuti Yehova adzaleka osakupatsani chilango chimene ankati akupatseni. 14 Kunena za ine, ndili mʼmanja mwanu; mundichite chilichonse chimene mukuganiza kuti ndi chabwino ndi choyenera. 15 Komatu dziwani kuti ngati mundipha, inu pamodzi ndi mzinda uno ndi onse amene amakhala muno, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi Yehova anandituma kuti ndidzayankhule mawu onsewa inu mukumva.” 16 Pamenepo ndunazo pamodzi ndi anthu onse anawuza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthu uyu sayenera kuphedwa! Pakuti wayankhula kwa ife mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.” 17 Akuluakulu ena a mʼdzikomo anayimirira ndi kuwuza gulu lonse la anthu kuti, 18 “Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti,“ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,Yerusalemu adzasanduka bwinja,ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’ 19 Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!” 20 (Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya. 21 Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto. 22 Komabe Mfumu Yehoyakimu anatuma Elinatani mwana wa Akibori pamodzi ndi anthu ena, ku Igupto. 23 Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba). 24 Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye anateteza Yeremiya, motero sanamupereke kwa anthu kuti amuphe.

In Other Versions

Jeremiah 26 in the ANGEFD

Jeremiah 26 in the ANTPNG2D

Jeremiah 26 in the AS21

Jeremiah 26 in the BAGH

Jeremiah 26 in the BBPNG

Jeremiah 26 in the BBT1E

Jeremiah 26 in the BDS

Jeremiah 26 in the BEV

Jeremiah 26 in the BHAD

Jeremiah 26 in the BIB

Jeremiah 26 in the BLPT

Jeremiah 26 in the BNT

Jeremiah 26 in the BNTABOOT

Jeremiah 26 in the BNTLV

Jeremiah 26 in the BOATCB

Jeremiah 26 in the BOATCB2

Jeremiah 26 in the BOBCV

Jeremiah 26 in the BOCNT

Jeremiah 26 in the BOECS

Jeremiah 26 in the BOHCB

Jeremiah 26 in the BOHCV

Jeremiah 26 in the BOHLNT

Jeremiah 26 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 26 in the BOICB

Jeremiah 26 in the BOILNTAP

Jeremiah 26 in the BOITCV

Jeremiah 26 in the BOKCV

Jeremiah 26 in the BOKCV2

Jeremiah 26 in the BOKHWOG

Jeremiah 26 in the BOKSSV

Jeremiah 26 in the BOLCB

Jeremiah 26 in the BOLCB2

Jeremiah 26 in the BOMCV

Jeremiah 26 in the BONAV

Jeremiah 26 in the BONCB

Jeremiah 26 in the BONLT

Jeremiah 26 in the BONUT2

Jeremiah 26 in the BOPLNT

Jeremiah 26 in the BOSCB

Jeremiah 26 in the BOSNC

Jeremiah 26 in the BOTLNT

Jeremiah 26 in the BOVCB

Jeremiah 26 in the BOYCB

Jeremiah 26 in the BPBB

Jeremiah 26 in the BPH

Jeremiah 26 in the BSB

Jeremiah 26 in the CCB

Jeremiah 26 in the CUV

Jeremiah 26 in the CUVS

Jeremiah 26 in the DBT

Jeremiah 26 in the DGDNT

Jeremiah 26 in the DHNT

Jeremiah 26 in the DNT

Jeremiah 26 in the ELBE

Jeremiah 26 in the EMTV

Jeremiah 26 in the ESV

Jeremiah 26 in the FBV

Jeremiah 26 in the FEB

Jeremiah 26 in the GGMNT

Jeremiah 26 in the GNT

Jeremiah 26 in the HARY

Jeremiah 26 in the HNT

Jeremiah 26 in the IRVA

Jeremiah 26 in the IRVB

Jeremiah 26 in the IRVG

Jeremiah 26 in the IRVH

Jeremiah 26 in the IRVK

Jeremiah 26 in the IRVM

Jeremiah 26 in the IRVM2

Jeremiah 26 in the IRVO

Jeremiah 26 in the IRVP

Jeremiah 26 in the IRVT

Jeremiah 26 in the IRVT2

Jeremiah 26 in the IRVU

Jeremiah 26 in the ISVN

Jeremiah 26 in the JSNT

Jeremiah 26 in the KAPI

Jeremiah 26 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 26 in the KBV

Jeremiah 26 in the KJV

Jeremiah 26 in the KNFD

Jeremiah 26 in the LBA

Jeremiah 26 in the LBLA

Jeremiah 26 in the LNT

Jeremiah 26 in the LSV

Jeremiah 26 in the MAAL

Jeremiah 26 in the MBV

Jeremiah 26 in the MBV2

Jeremiah 26 in the MHNT

Jeremiah 26 in the MKNFD

Jeremiah 26 in the MNG

Jeremiah 26 in the MNT

Jeremiah 26 in the MNT2

Jeremiah 26 in the MRS1T

Jeremiah 26 in the NAA

Jeremiah 26 in the NASB

Jeremiah 26 in the NBLA

Jeremiah 26 in the NBS

Jeremiah 26 in the NBVTP

Jeremiah 26 in the NET2

Jeremiah 26 in the NIV11

Jeremiah 26 in the NNT

Jeremiah 26 in the NNT2

Jeremiah 26 in the NNT3

Jeremiah 26 in the PDDPT

Jeremiah 26 in the PFNT

Jeremiah 26 in the RMNT

Jeremiah 26 in the SBIAS

Jeremiah 26 in the SBIBS

Jeremiah 26 in the SBIBS2

Jeremiah 26 in the SBICS

Jeremiah 26 in the SBIDS

Jeremiah 26 in the SBIGS

Jeremiah 26 in the SBIHS

Jeremiah 26 in the SBIIS

Jeremiah 26 in the SBIIS2

Jeremiah 26 in the SBIIS3

Jeremiah 26 in the SBIKS

Jeremiah 26 in the SBIKS2

Jeremiah 26 in the SBIMS

Jeremiah 26 in the SBIOS

Jeremiah 26 in the SBIPS

Jeremiah 26 in the SBISS

Jeremiah 26 in the SBITS

Jeremiah 26 in the SBITS2

Jeremiah 26 in the SBITS3

Jeremiah 26 in the SBITS4

Jeremiah 26 in the SBIUS

Jeremiah 26 in the SBIVS

Jeremiah 26 in the SBT

Jeremiah 26 in the SBT1E

Jeremiah 26 in the SCHL

Jeremiah 26 in the SNT

Jeremiah 26 in the SUSU

Jeremiah 26 in the SUSU2

Jeremiah 26 in the SYNO

Jeremiah 26 in the TBIAOTANT

Jeremiah 26 in the TBT1E

Jeremiah 26 in the TBT1E2

Jeremiah 26 in the TFTIP

Jeremiah 26 in the TFTU

Jeremiah 26 in the TGNTATF3T

Jeremiah 26 in the THAI

Jeremiah 26 in the TNFD

Jeremiah 26 in the TNT

Jeremiah 26 in the TNTIK

Jeremiah 26 in the TNTIL

Jeremiah 26 in the TNTIN

Jeremiah 26 in the TNTIP

Jeremiah 26 in the TNTIZ

Jeremiah 26 in the TOMA

Jeremiah 26 in the TTENT

Jeremiah 26 in the UBG

Jeremiah 26 in the UGV

Jeremiah 26 in the UGV2

Jeremiah 26 in the UGV3

Jeremiah 26 in the VBL

Jeremiah 26 in the VDCC

Jeremiah 26 in the YALU

Jeremiah 26 in the YAPE

Jeremiah 26 in the YBVTP

Jeremiah 26 in the ZBP