Jeremiah 48 (BOGWICC)

1 Ponena za Mowabu: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa.Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa;linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa. 2 Palibenso amene akutamanda Mowabu;ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa:‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete;ankhondo adzakupirikitsani. 3 Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu.Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’ 4 Mowabu wawonongeka;ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri. 5 Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti,akulira kwambiri pamene akupita.Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumvekapa njira yotsikira ku Horonaimu. 6 Thawani! Dzipulumutseni;khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu. 7 Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu,nanunso mudzatengedwa ukapolo,ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo,pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake. 8 Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse,ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke.Chigwa chidzasanduka bwinjandipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwamonga Yehova wayankhulira. 9 Mtsineni khutu Mowabuchifukwa adzasakazika;mizinda yake idzasanduka mabwinja,wopanda munthu wokhalamo. 10 “Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika!Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu! 11 “Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake,ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina;iye sanatengedwepo ukapolo.Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kujandipo fungo lake silinasinthe. 12 Nʼchifukwa chake masiku akubwera,”akutero Yehova,“pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsukondipo adzamukhutula;adzakhuthula vinyo yense mitsuko yakepambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo. 13 Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi,monga momwe Aisraeli anachitira manyazindi Beteli amene ankamukhutulira. 14 “Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali.Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’ 15 Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake;anyamata ake okongola apita kukaphedwa,”ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. 16 Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi;masautso ake akubwera posachedwa. 17 Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira,inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake;nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija,taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!” 18 “Tsikani pa ulemerero wanundipo khalani pansi powuma,inu anthu okhala ku Diboni,pakuti wowononga Mowabuwabwera kudzamenyana nanu,wasakaza mizinda yanu yotetezedwa. 19 Inu amene mumakhala ku Aroeri,imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera.Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka,afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’ ” 20 Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika.Lirani mwachisoni ndipo fuwulani!Lengezani ku mtsinje wa Arinonikuti Mowabu wawonongedwa. 21 Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri,ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati, 22 Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu, 23 Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni, 24 Keriyoti ndi Bozirandi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe. 25 Mphamvu za Mowabu zawonongeka;mkono wake wathyoka,”akutero Yehova. 26 “Muledzeretseni Mowabu,chifukwa anadzikuza powukira Yehova.Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake;mulekeni akhale chinthu chomachiseka. 27 Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka?Kodi Israeli anapezeka pakati pa akubakuti nthawi zonse poyankhula za iye,iwe uzimupukusira mutu momunyoza? 28 Inu amene mumakhala ku Mowabu,siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe.Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chakepa khomo la phanga. 29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu,kunyada kwake nʼkwakukulu.Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula.Ali ndi mtima wodzikweza. 30 Ine ndikuzidziwa ntchito zake,akutero Yehova.Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu. 31 Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu,ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu,ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi. 32 Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri.Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesaimene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja;zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri.Wowononga wasakazazipatso zake zachilimwe ndi mpesa. 33 Chimwemwe ndi chisangalalo zathaku minda ya zipatso ya ku Mowabu.Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa;palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa.Ngakhale kufuwula kulipo,koma sikufuwula kwa chimwemwe. 34 “A ku Hesiboni ndi Eleali akulirandipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi,kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya.Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa. 35 Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabukupereka nsembe mʼmalo awo opembedzerandi kufukiza lubani kwa milungu yawo,”akutero Yehova. 36 “Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro.Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitolirochifukwa chuma chimene anachipata chatha. 37 Aliyense wameta mutu wakendi ndevu zake;manja a munthu aliyense ndi ochekacheka,ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake. 38 Pa madenga onse a ku Mowabundiponso mʼmisewu yakeanthu akungolira,pakuti ndaphwanya Mowabungati mtsuko wopanda ntchito,”akutero Yehova. 39 “Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira!Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi.Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka,chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.” 40 Yehova akuti,“Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhangachimene chatambalitsa mapiko ake. 41 Mizinda idzagwidwandipo malinga adzalandidwa.Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabuidzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira. 42 Mowabu sudzakhala mtundu wa anthuchifukwa unadzikuza powukira Yehova. 43 Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikirainu anthu a ku Mowabu,”akutero Yehova. 44 “Aliyense wothawa zoopsaadzagwera mʼdzenje,aliyense wotuluka mʼdzenjeadzakodwa mu msampha.Ndigwetsa zimenezi pa Mowabupa nthawi ya chilango chake,”akutero Yehova. 45 “Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesibonichifukwa chotopa.Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni.Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,dziko la anthu onyada. 46 Tsoka kwa iwe Mowabu!Anthu opembedza Kemosi awonongeka.Ana ako aamuna ndi aakaziatengedwa ukapolo. 47 “Komabe masiku akutsogolondidzabwezeranso Mowabu chuma chake,”akutero Yehova.Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.

In Other Versions

Jeremiah 48 in the ANGEFD

Jeremiah 48 in the ANTPNG2D

Jeremiah 48 in the AS21

Jeremiah 48 in the BAGH

Jeremiah 48 in the BBPNG

Jeremiah 48 in the BBT1E

Jeremiah 48 in the BDS

Jeremiah 48 in the BEV

Jeremiah 48 in the BHAD

Jeremiah 48 in the BIB

Jeremiah 48 in the BLPT

Jeremiah 48 in the BNT

Jeremiah 48 in the BNTABOOT

Jeremiah 48 in the BNTLV

Jeremiah 48 in the BOATCB

Jeremiah 48 in the BOATCB2

Jeremiah 48 in the BOBCV

Jeremiah 48 in the BOCNT

Jeremiah 48 in the BOECS

Jeremiah 48 in the BOHCB

Jeremiah 48 in the BOHCV

Jeremiah 48 in the BOHLNT

Jeremiah 48 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 48 in the BOICB

Jeremiah 48 in the BOILNTAP

Jeremiah 48 in the BOITCV

Jeremiah 48 in the BOKCV

Jeremiah 48 in the BOKCV2

Jeremiah 48 in the BOKHWOG

Jeremiah 48 in the BOKSSV

Jeremiah 48 in the BOLCB

Jeremiah 48 in the BOLCB2

Jeremiah 48 in the BOMCV

Jeremiah 48 in the BONAV

Jeremiah 48 in the BONCB

Jeremiah 48 in the BONLT

Jeremiah 48 in the BONUT2

Jeremiah 48 in the BOPLNT

Jeremiah 48 in the BOSCB

Jeremiah 48 in the BOSNC

Jeremiah 48 in the BOTLNT

Jeremiah 48 in the BOVCB

Jeremiah 48 in the BOYCB

Jeremiah 48 in the BPBB

Jeremiah 48 in the BPH

Jeremiah 48 in the BSB

Jeremiah 48 in the CCB

Jeremiah 48 in the CUV

Jeremiah 48 in the CUVS

Jeremiah 48 in the DBT

Jeremiah 48 in the DGDNT

Jeremiah 48 in the DHNT

Jeremiah 48 in the DNT

Jeremiah 48 in the ELBE

Jeremiah 48 in the EMTV

Jeremiah 48 in the ESV

Jeremiah 48 in the FBV

Jeremiah 48 in the FEB

Jeremiah 48 in the GGMNT

Jeremiah 48 in the GNT

Jeremiah 48 in the HARY

Jeremiah 48 in the HNT

Jeremiah 48 in the IRVA

Jeremiah 48 in the IRVB

Jeremiah 48 in the IRVG

Jeremiah 48 in the IRVH

Jeremiah 48 in the IRVK

Jeremiah 48 in the IRVM

Jeremiah 48 in the IRVM2

Jeremiah 48 in the IRVO

Jeremiah 48 in the IRVP

Jeremiah 48 in the IRVT

Jeremiah 48 in the IRVT2

Jeremiah 48 in the IRVU

Jeremiah 48 in the ISVN

Jeremiah 48 in the JSNT

Jeremiah 48 in the KAPI

Jeremiah 48 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 48 in the KBV

Jeremiah 48 in the KJV

Jeremiah 48 in the KNFD

Jeremiah 48 in the LBA

Jeremiah 48 in the LBLA

Jeremiah 48 in the LNT

Jeremiah 48 in the LSV

Jeremiah 48 in the MAAL

Jeremiah 48 in the MBV

Jeremiah 48 in the MBV2

Jeremiah 48 in the MHNT

Jeremiah 48 in the MKNFD

Jeremiah 48 in the MNG

Jeremiah 48 in the MNT

Jeremiah 48 in the MNT2

Jeremiah 48 in the MRS1T

Jeremiah 48 in the NAA

Jeremiah 48 in the NASB

Jeremiah 48 in the NBLA

Jeremiah 48 in the NBS

Jeremiah 48 in the NBVTP

Jeremiah 48 in the NET2

Jeremiah 48 in the NIV11

Jeremiah 48 in the NNT

Jeremiah 48 in the NNT2

Jeremiah 48 in the NNT3

Jeremiah 48 in the PDDPT

Jeremiah 48 in the PFNT

Jeremiah 48 in the RMNT

Jeremiah 48 in the SBIAS

Jeremiah 48 in the SBIBS

Jeremiah 48 in the SBIBS2

Jeremiah 48 in the SBICS

Jeremiah 48 in the SBIDS

Jeremiah 48 in the SBIGS

Jeremiah 48 in the SBIHS

Jeremiah 48 in the SBIIS

Jeremiah 48 in the SBIIS2

Jeremiah 48 in the SBIIS3

Jeremiah 48 in the SBIKS

Jeremiah 48 in the SBIKS2

Jeremiah 48 in the SBIMS

Jeremiah 48 in the SBIOS

Jeremiah 48 in the SBIPS

Jeremiah 48 in the SBISS

Jeremiah 48 in the SBITS

Jeremiah 48 in the SBITS2

Jeremiah 48 in the SBITS3

Jeremiah 48 in the SBITS4

Jeremiah 48 in the SBIUS

Jeremiah 48 in the SBIVS

Jeremiah 48 in the SBT

Jeremiah 48 in the SBT1E

Jeremiah 48 in the SCHL

Jeremiah 48 in the SNT

Jeremiah 48 in the SUSU

Jeremiah 48 in the SUSU2

Jeremiah 48 in the SYNO

Jeremiah 48 in the TBIAOTANT

Jeremiah 48 in the TBT1E

Jeremiah 48 in the TBT1E2

Jeremiah 48 in the TFTIP

Jeremiah 48 in the TFTU

Jeremiah 48 in the TGNTATF3T

Jeremiah 48 in the THAI

Jeremiah 48 in the TNFD

Jeremiah 48 in the TNT

Jeremiah 48 in the TNTIK

Jeremiah 48 in the TNTIL

Jeremiah 48 in the TNTIN

Jeremiah 48 in the TNTIP

Jeremiah 48 in the TNTIZ

Jeremiah 48 in the TOMA

Jeremiah 48 in the TTENT

Jeremiah 48 in the UBG

Jeremiah 48 in the UGV

Jeremiah 48 in the UGV2

Jeremiah 48 in the UGV3

Jeremiah 48 in the VBL

Jeremiah 48 in the VDCC

Jeremiah 48 in the YALU

Jeremiah 48 in the YAPE

Jeremiah 48 in the YBVTP

Jeremiah 48 in the ZBP