Jeremiah 6 (BOGWICC)
1 “Thawani, inu anthu a ku Benjamini!Tulukani mu Yerusalemu!Lizani lipenga ku Tekowa!Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu. 2 Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo? 3 Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo;adzamanga matenti awo mowuzinga,ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.” 4 Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo!Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano.Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka,ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika. 5 Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku unondi kuwononga malinga ake!” 6 Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Dulani mitengondipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;wadzaza ndi kuponderezana. 7 Monga momwe chitsime chimatulutsira madzindi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse. 8 Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokerendi kusandutsa dziko lako kukhala bwinjamopanda munthu wokhalamo.” 9 Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti,“Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli,monga momwe amachitira populula mphesa.Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathemonga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.” 10 Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?Makutu awo ndi otsekekakotero kuti sangathe kumva.Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;sasangalatsidwa nawo. 11 Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova. Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewundi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka. 12 Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.Ndidzatambasula dzanja langa kukanthaanthu okhala mʼdzikomo,”akutero Yehova. 13 “Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,onse amachita zachinyengo. 14 Amapoletsa zilonda za anthu angapamwamba pokha.Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’pamene palibe mtendere. 15 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo?Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe;sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe.Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,”akutero Yehova. 16 Yehova akuti,“Imani pa mphambano ndipo mupenye;kumeneko ndiye kuli njira zakale,funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’ 17 Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanirenindipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’ 18 Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,chimene chidzawachitikire anthuwo. 19 Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,ndikubweretsa masautso pa anthu awa.Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.Iwowa sanamvere mawu angandipo anakana lamulo langa. 20 Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;nsembe zanu sizindikondweretsa.” 21 Choncho Yehova akuti,“Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.” 22 Yehova akunena kuti,“Taonani, gulu lankhondo likubwerakuchokera kumpoto;mtundu wa anthu amphamvu wanyamukakuchokera kumathero a dziko lapansi. 23 Atenga mauta ndi mikondo;ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.Akwera pa akavalo awondipo akonzekera ngati anthu ankhondo,kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.” 24 A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,ndipo manja anthu alefukiratu.Nkhawa yatigwira,ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira. 25 Musapite ku mindakapena kuyenda mʼmisewu,pakuti mdani ali ndi lupanga,ndipo ponseponse anthu akuchita mantha. 26 Inu anthu anga, valani zigudulindipo gubudukani pa phulusa;lirani mwamphamvungati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,pakuti mwadzidzidzi wowonongayoadzabwera kudzatipha. 27 “Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo.Uwayese anthu angamonga ungayesere chitsulokuti uwone makhalidwe awo. 28 Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukirandipo akunka nanena zamiseche.Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.Onse amangochita zoyipa zokhazokha. 29 Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;mtovu watha kusungunuka ndi moto.Koma ntchito yosungunulayo sikupindulachifukwa zoyipa sizikuchokapo. 30 Iwo ali ngati siliva wotayidwa,chifukwa Yehova wawakana.”