John 18 (BOGWICC)
1 Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo. 2 Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko. 3 Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida. 4 Yesu, podziwa zonse zimene zimati zichitike kwa Iye, anatuluka ndi kuwafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndani?” 5 Iwo anayankha kuti, “Yesu wa ku Nazareti.”Yesu anati, “Ndine.” (Ndipo Yudasi womuperekayo anali atayima nawo pamenepo). 6 Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi. 7 Iye anawafunsanso kuti, “Kodi mukumufuna ndani?”Ndipo iwo anati, “Yesu wa ku Nazareti.” 8 Yesu anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kuti Ndine. Ngati inu mukufuna Ine, asiyeni anthu awa apite.” 9 Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.” 10 Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi). 11 Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?” 12 Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga. 13 Poyamba anapita naye kwa Anasi amene anali mkamwini wa Kayafa, mkulu wa ansembe chaka chimenecho. 14 Kayafa anali amene analangiza Ayuda kuti kukanakhala kwabwino ngati munthu mmodzi akanafera anthu. 15 Simoni Petro ndi ophunzira wina ankamutsatira Yesu chifukwa ophunzira uyu amadziwika kwa mkulu wa ansembe. Iye analowa ndi Yesu mʼbwalo la mkulu wa ansembe 16 koma Petro anadikira kunja pa khomo. Ophunzira winayo amene amadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka ndi kuyankhula ndi mtsikana amene anali mlonda wa pa khomo ndi kumulowetsa Petro. 17 Mtsikanayo anafunsa Petro kuti, “Kodi iwe sindiwe mmodzi wa ophunzira a Munthu uyu?”Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.” 18 Popeza kunkazizira, anyamata antchito ndi akuluakulu ena anasonkha moto wamakala namawotha atayimirira mozungulira. Petro nayenso anayimirira pamodzi ndi iwo namawotha nawo motowo. 19 Pa nthawi imeneyi, mkulu wa ansembe anamufunsa Yesu za ophunzira ake ndi chiphunzitso chake. 20 Yesu anayankha kuti, “Ine ndinayankhula poyera ku dziko lapansi. Nthawi zonse ndimaphunzitsa mʼsunagoge kapena mʼNyumba ya Mulungu kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi. Ine sindimanena kanthu mseri. 21 Nʼchifukwa chiyani mukundifunsa Ine? Afunseni amene amamva. Zoonadi akudziwa zimene Ine ndinanena.” 22 Yesu atanena izi, mmodzi wa akuluakulu amene anali pafupi anamumenya kumaso. Iye anafunsa kuti, “Mayankhidwe awa ndi woti ndi kuyankha mkulu wa ansembe?” 23 Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndanena kanthu kolakwika, chitirani umboni chimene ndalakwa. Koma ngati ndanena zoona, nʼchifukwa chiyani mwandimenya?” 24 Kenaka Anasi anamutumiza Iye, ali womangidwabe, kwa Kayafa, mkulu wa ansembe. 25 Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?”Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.” 26 Mmodzi wa antchito a mkulu wa ansembe, mʼbale wa munthu amene anadulidwa khutu ndi Petro anamutsutsa iye kuti, “Kodi sindinakuone iwe pamodzi ndi Iye mʼmunda muja?” 27 Petro anakananso, ndipo pa nthawi yomweyo tambala analira. 28 Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska. 29 Choncho Pilato anatuluka napita kwa iwo ndipo anati, “Kodi ndi milandu yanji imene mukumuzenga munthu uyu?” 30 Iwo anayankha kuti, “Ngati Iye akanakhala kuti si wolakwa, ife sitikanamupereka kwa inu.” 31 Pilato anati, “Mutengeni inu eni ake ndi kumuweruza Iye monga mwa malamulo anu.”Ayuda anatsutsa nati, “Koma tilibe ulamuliro wakupha aliyense.” 32 Izi zinachitika kuti mawu a Yesu amene anayankhula kusonyeza mtundu wa imfa imene Iye anati adzafe nayo akwaniritsidwe. 33 Kenaka Pilato anapita mʼkati mwa nyumba yaufumu nayitanitsa Yesu, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi iwe ndi mfumu ya Ayuda?” 34 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amenewo ndi maganizo anu wokha? Kapena kuti ena anakuwuzani za Ine?” 35 Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?” 36 Yesu anati, “Ufumu wanga si wa dziko lapansi lino. Ukanakhala wa pansi pano, antchito anga akanachita nkhondo kulepheretsa Ayuda kundigwira. Koma tsopano ufumu wanga ndi wochokera kumalo ena.” 37 Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!”Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.” 38 Pilato anafunsa kuti, “Kodi choonadi nʼchiyani?” Ndi mawu awa iye anapitanso kwa Ayuda ndipo anati, “Ine sindikupeza mlandu mwa Iye. 39 Koma ndi mwambo wanu kuti pa nthawi ya Paska, ine ndikumasulireni wamʼndende mmodzi. Kodi mufuna ndikumasulireni ‘Mfumu ya Ayuda?’ ” 40 Iwo anafuwula nati, “Ameneyu ayi! Mutipatse ife Baraba!” Barabayo anali wachifwamba.