John 9 (BOGWICC)

1 Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. 2 Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?” 3 Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. 4 Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. 5 Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.” 6 Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. 7 Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya. 8 Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?” 9 Ena ananena kuti anali yemweyo.Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.”Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.” 10 Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?” 11 Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.” 12 Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?”Iye anati, “Ine sindikudziwa.” 13 Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi. 14 Tsono linali la Sabata tsiku limene Yesu anakanda dothi ndi kutsekula maso a munthuyu. 15 Choncho Afarisi anamufunsanso iye momwe analandirira kuona kwake. Munthuyo anayankha kuti, “Iye anapaka matope mʼmaso anga, ndipo ine ndinakasamba, ndipo ndikuona.” 16 Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.”Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika. 17 Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?”Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.” 18 Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake. 19 Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu ndi mwana wanu? Kodi iyeyu ndi amene mukunena kuti anabadwa wosaona? Nanga zikutheka bwanji kuti akuona?” 20 Makolo anayankha kuti, “Ife tikudziwa kuti ndi mwana wathu, ndipo tikudziwa kuti anabadwa wosaona. 21 Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.” 22 Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge. 23 Ichi ndi chifukwa chake makolo ake anati, “Mufunseni iye ndi wamkulu.” 24 Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.” 25 Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!” 26 Kenaka anamufunsa kuti, “Kodi Iye anachita chiyani kwa iwe? Iye anatsekula motani maso ako?” 27 Iye anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kale ndipo inu simunamvetsetse. Chifukwa chiyani mukufuna mumvenso? Mukufuna kuti inu mukhale ophunzira akenso?” 28 Pamenepo anamunyoza ndipo anati, “Iwe ndiye ophunzira wa munthuyu! Ife ndife ophunzira a Mose! 29 Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.” 30 Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga. 31 Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake. 32 Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona. 33 Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.” 34 Pamenepo anayankha kuti, “Iwe unabadwa mu uchimo kotheratu; bwanji ukuyesa kutiphunzitsa ife!” Ndipo anamutulutsa kunja. 35 Yesu anamva kuti anamutulutsa kunja ndipo pamene anamupeza anati, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?” 36 Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi, Ambuye, ameneyo ndi ndani? Ndiwuzeni kuti ndimukhulupirire Iye?” 37 Yesu anati, “Iwe wamuona tsopano. Zoonadi ndiye amene akuyankhula nawe.” 38 Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye. 39 Yesu anati, “Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone.” 40 Afarisi ena amene anali pafupi naye anamva akunena izi ndipo anafunsa kuti, “Chiyani? Kodi ndife osaonanso?” 41 Yesu anati, “Mukanakhala osaona, simukanachimwa; koma tsopano popeza mukuti mumaona, ndinu ochimwabe.”

In Other Versions

John 9 in the ANGEFD

John 9 in the ANTPNG2D

John 9 in the AS21

John 9 in the BAGH

John 9 in the BBPNG

John 9 in the BBT1E

John 9 in the BDS

John 9 in the BEV

John 9 in the BHAD

John 9 in the BIB

John 9 in the BLPT

John 9 in the BNT

John 9 in the BNTABOOT

John 9 in the BNTLV

John 9 in the BOATCB

John 9 in the BOATCB2

John 9 in the BOBCV

John 9 in the BOCNT

John 9 in the BOECS

John 9 in the BOHCB

John 9 in the BOHCV

John 9 in the BOHLNT

John 9 in the BOHNTLTAL

John 9 in the BOICB

John 9 in the BOILNTAP

John 9 in the BOITCV

John 9 in the BOKCV

John 9 in the BOKCV2

John 9 in the BOKHWOG

John 9 in the BOKSSV

John 9 in the BOLCB

John 9 in the BOLCB2

John 9 in the BOMCV

John 9 in the BONAV

John 9 in the BONCB

John 9 in the BONLT

John 9 in the BONUT2

John 9 in the BOPLNT

John 9 in the BOSCB

John 9 in the BOSNC

John 9 in the BOTLNT

John 9 in the BOVCB

John 9 in the BOYCB

John 9 in the BPBB

John 9 in the BPH

John 9 in the BSB

John 9 in the CCB

John 9 in the CUV

John 9 in the CUVS

John 9 in the DBT

John 9 in the DGDNT

John 9 in the DHNT

John 9 in the DNT

John 9 in the ELBE

John 9 in the EMTV

John 9 in the ESV

John 9 in the FBV

John 9 in the FEB

John 9 in the GGMNT

John 9 in the GNT

John 9 in the HARY

John 9 in the HNT

John 9 in the IRVA

John 9 in the IRVB

John 9 in the IRVG

John 9 in the IRVH

John 9 in the IRVK

John 9 in the IRVM

John 9 in the IRVM2

John 9 in the IRVO

John 9 in the IRVP

John 9 in the IRVT

John 9 in the IRVT2

John 9 in the IRVU

John 9 in the ISVN

John 9 in the JSNT

John 9 in the KAPI

John 9 in the KBT1ETNIK

John 9 in the KBV

John 9 in the KJV

John 9 in the KNFD

John 9 in the LBA

John 9 in the LBLA

John 9 in the LNT

John 9 in the LSV

John 9 in the MAAL

John 9 in the MBV

John 9 in the MBV2

John 9 in the MHNT

John 9 in the MKNFD

John 9 in the MNG

John 9 in the MNT

John 9 in the MNT2

John 9 in the MRS1T

John 9 in the NAA

John 9 in the NASB

John 9 in the NBLA

John 9 in the NBS

John 9 in the NBVTP

John 9 in the NET2

John 9 in the NIV11

John 9 in the NNT

John 9 in the NNT2

John 9 in the NNT3

John 9 in the PDDPT

John 9 in the PFNT

John 9 in the RMNT

John 9 in the SBIAS

John 9 in the SBIBS

John 9 in the SBIBS2

John 9 in the SBICS

John 9 in the SBIDS

John 9 in the SBIGS

John 9 in the SBIHS

John 9 in the SBIIS

John 9 in the SBIIS2

John 9 in the SBIIS3

John 9 in the SBIKS

John 9 in the SBIKS2

John 9 in the SBIMS

John 9 in the SBIOS

John 9 in the SBIPS

John 9 in the SBISS

John 9 in the SBITS

John 9 in the SBITS2

John 9 in the SBITS3

John 9 in the SBITS4

John 9 in the SBIUS

John 9 in the SBIVS

John 9 in the SBT

John 9 in the SBT1E

John 9 in the SCHL

John 9 in the SNT

John 9 in the SUSU

John 9 in the SUSU2

John 9 in the SYNO

John 9 in the TBIAOTANT

John 9 in the TBT1E

John 9 in the TBT1E2

John 9 in the TFTIP

John 9 in the TFTU

John 9 in the TGNTATF3T

John 9 in the THAI

John 9 in the TNFD

John 9 in the TNT

John 9 in the TNTIK

John 9 in the TNTIL

John 9 in the TNTIN

John 9 in the TNTIP

John 9 in the TNTIZ

John 9 in the TOMA

John 9 in the TTENT

John 9 in the UBG

John 9 in the UGV

John 9 in the UGV2

John 9 in the UGV3

John 9 in the VBL

John 9 in the VDCC

John 9 in the YALU

John 9 in the YAPE

John 9 in the YBVTP

John 9 in the ZBP