Job 21 (BOGWICC)
1 Pamenepo Yobu anayankha kuti, 2 “Mvetserani bwino mawu anga;ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu. 3 Ndiloleni ndiyankhulendipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze. 4 “Kodi ine ndikudandaulira munthu?Tsono ndilekerenji kupsa mtima? 5 Ndipenyeni ndipo mudabwe;mugwire dzanja pakamwa. 6 Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri;thupi langa limanjenjemera. 7 Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo,amakalamba ndi kusanduka amphamvu? 8 Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo,zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona. 9 Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha;mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe. 10 Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa;ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza. 11 Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa;makanda awo amavinavina pabwalo. 12 Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze;amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro. 13 Zaka zawo zimatha ali mu ulemererondipo amatsikira ku manda mwamtendere. 14 Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu. 15 Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire?Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo? 16 Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo,koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa. 17 “Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa?Nʼkangati kamene tsoka limawagwera?Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga? 18 Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo,ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu? 19 Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi. 20 Mulole kuti adzionere yekha chilango chake,kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse. 21 Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo,pamene chiwerengero cha masiku ake chatha? 22 “Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru,poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba? 23 Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse,ali pa mtendere ndi pa mpumulo, 24 thupi lake lili lonenepa,mafupa ake ali odzaza ndi mafuta. 25 Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima,wosalawapo chinthu chabwino chilichonse. 26 Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmandandipo onse amatuluka mphutsi. 27 “Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza,ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire. 28 Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti,matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’ 29 Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo?Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena? 30 Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka,kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu? 31 Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo?Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita? 32 Iye amanyamulidwa kupita ku mandandipo anthu amachezera pa manda ake. 33 Dothi la ku chigwa limamukomera;anthu onse amatsatira mtembo wake,ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho. 34 “Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewopalibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”
In Other Versions
Job 21 in the ANGEFD
Job 21 in the ANTPNG2D
Job 21 in the AS21
Job 21 in the BAGH
Job 21 in the BBPNG
Job 21 in the BBT1E
Job 21 in the BDS
Job 21 in the BEV
Job 21 in the BHAD
Job 21 in the BIB
Job 21 in the BLPT
Job 21 in the BNT
Job 21 in the BNTABOOT
Job 21 in the BNTLV
Job 21 in the BOATCB
Job 21 in the BOATCB2
Job 21 in the BOBCV
Job 21 in the BOCNT
Job 21 in the BOECS
Job 21 in the BOHCB
Job 21 in the BOHCV
Job 21 in the BOHLNT
Job 21 in the BOHNTLTAL
Job 21 in the BOICB
Job 21 in the BOILNTAP
Job 21 in the BOITCV
Job 21 in the BOKCV
Job 21 in the BOKCV2
Job 21 in the BOKHWOG
Job 21 in the BOKSSV
Job 21 in the BOLCB
Job 21 in the BOLCB2
Job 21 in the BOMCV
Job 21 in the BONAV
Job 21 in the BONCB
Job 21 in the BONLT
Job 21 in the BONUT2
Job 21 in the BOPLNT
Job 21 in the BOSCB
Job 21 in the BOSNC
Job 21 in the BOTLNT
Job 21 in the BOVCB
Job 21 in the BOYCB
Job 21 in the BPBB
Job 21 in the BPH
Job 21 in the BSB
Job 21 in the CCB
Job 21 in the CUV
Job 21 in the CUVS
Job 21 in the DBT
Job 21 in the DGDNT
Job 21 in the DHNT
Job 21 in the DNT
Job 21 in the ELBE
Job 21 in the EMTV
Job 21 in the ESV
Job 21 in the FBV
Job 21 in the FEB
Job 21 in the GGMNT
Job 21 in the GNT
Job 21 in the HARY
Job 21 in the HNT
Job 21 in the IRVA
Job 21 in the IRVB
Job 21 in the IRVG
Job 21 in the IRVH
Job 21 in the IRVK
Job 21 in the IRVM
Job 21 in the IRVM2
Job 21 in the IRVO
Job 21 in the IRVP
Job 21 in the IRVT
Job 21 in the IRVT2
Job 21 in the IRVU
Job 21 in the ISVN
Job 21 in the JSNT
Job 21 in the KAPI
Job 21 in the KBT1ETNIK
Job 21 in the KBV
Job 21 in the KJV
Job 21 in the KNFD
Job 21 in the LBA
Job 21 in the LBLA
Job 21 in the LNT
Job 21 in the LSV
Job 21 in the MAAL
Job 21 in the MBV
Job 21 in the MBV2
Job 21 in the MHNT
Job 21 in the MKNFD
Job 21 in the MNG
Job 21 in the MNT
Job 21 in the MNT2
Job 21 in the MRS1T
Job 21 in the NAA
Job 21 in the NASB
Job 21 in the NBLA
Job 21 in the NBS
Job 21 in the NBVTP
Job 21 in the NET2
Job 21 in the NIV11
Job 21 in the NNT
Job 21 in the NNT2
Job 21 in the NNT3
Job 21 in the PDDPT
Job 21 in the PFNT
Job 21 in the RMNT
Job 21 in the SBIAS
Job 21 in the SBIBS
Job 21 in the SBIBS2
Job 21 in the SBICS
Job 21 in the SBIDS
Job 21 in the SBIGS
Job 21 in the SBIHS
Job 21 in the SBIIS
Job 21 in the SBIIS2
Job 21 in the SBIIS3
Job 21 in the SBIKS
Job 21 in the SBIKS2
Job 21 in the SBIMS
Job 21 in the SBIOS
Job 21 in the SBIPS
Job 21 in the SBISS
Job 21 in the SBITS
Job 21 in the SBITS2
Job 21 in the SBITS3
Job 21 in the SBITS4
Job 21 in the SBIUS
Job 21 in the SBIVS
Job 21 in the SBT
Job 21 in the SBT1E
Job 21 in the SCHL
Job 21 in the SNT
Job 21 in the SUSU
Job 21 in the SUSU2
Job 21 in the SYNO
Job 21 in the TBIAOTANT
Job 21 in the TBT1E
Job 21 in the TBT1E2
Job 21 in the TFTIP
Job 21 in the TFTU
Job 21 in the TGNTATF3T
Job 21 in the THAI
Job 21 in the TNFD
Job 21 in the TNT
Job 21 in the TNTIK
Job 21 in the TNTIL
Job 21 in the TNTIN
Job 21 in the TNTIP
Job 21 in the TNTIZ
Job 21 in the TOMA
Job 21 in the TTENT
Job 21 in the UBG
Job 21 in the UGV
Job 21 in the UGV2
Job 21 in the UGV3
Job 21 in the VBL
Job 21 in the VDCC
Job 21 in the YALU
Job 21 in the YAPE
Job 21 in the YBVTP
Job 21 in the ZBP