Joshua 18 (BOGWICC)

1 Atagonjetsa dziko lonse Aisraeli anasonkhana ku Silo ndipo anayimikako tenti ya msonkhano. 2 Koma pa nthawiyo nʼkuti mafuko asanu ndi awiri a Aisraeli asanalandire cholowa chawo. 3 Ndipo Yoswa anati kwa Aisraeli, “Kodi mudikira mpaka liti kuti mulowe ndi kulanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani? 4 Sankhani amuna atatu kuchokera ku fuko lililonse ndipo ine ndidzawatuma kuti akayendere dzikolo ndi kukalilembera bwino kuti ndiligawe kukhala lawo. Akatero, abwererenso kwa ine. 5 Aligawe dzikolo mʼzigawo zisanu ndi ziwiri; fuko la Yuda lidzakhale ndi dziko lake la kummwera ndi nyumba ya Yosefe ikhalebe mʼdziko lawo la kumpoto. 6 Mudzalembe mawu ofotokoza za zigawo zisanu ndi ziwiri za dzikolo, ndi kubwera nawo kwa ine. Tsono ineyo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 7 Alevi asakhale ndi dziko pakati panu, chifukwa gawo lawo ndi kutumikira Yehova pa ntchito ya unsembe. Ndipo Gadi, Rubeni ndi theka la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo kummawa kwa Yorodani. Mose mtumiki wa Yehova ndiye anawapatsa.” 8 Anthuwo akupita kukalembera dzikolo, Yoswa anawalangiza kuti, “Pitani mukayendere ndi kulembera dzikolo. Kenaka mukabwere kwa ine, ndidzakuchitirani maere kuno ku Silo pamaso pa Yehova.” 9 Ndipo anthu anachoka ndi kukayendera dziko lonse. Iwo analemba bwinobwino mʼbuku za dzikolo, mzinda ndi mzinda. Analigawa magawo asanu ndi awiri, ndipo anabwerera kwa Yoswa ku misasa ya ku Silo. 10 Pambuyo pake Yoswa anawachitira maere ku Silo pamaso pa Yehova, ndipo fuko lililonse la Israeli analigawira dziko lake. 11 Maere anagwera mabanja a fuko la Benjamini. Dziko limene anapatsidwa linali pakati pa fuko la Yuda ndi fuko la Yosefe: 12 Mbali ya kumpoto malire awo anayambira ku Yorodani nalowera chakumpoto kwa matsitso a ku Yeriko kulowera cha kumadzulo kwa dziko la ku mapiri ndi kukafika ku chipululu cha Beti-Aveni. 13 Kuchokera kumeneko malirewo analoza ku Luzi nadutsa mʼmbali mwa mapiri kummwera kwa Luzi (ndiye Beteli) ndipo anatsika mpaka ku Ataroti Adari, ku mapiri a kummwera kwa Beti-Horoni wa Kumunsi. 14 Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo. 15 Malire a kummwera anayambira mʼmphepete mwenimweni mwa Kiriati Yearimu napita kumadzulo mpaka kukafika ku akasupe a Nefitowa. 16 Malire anatsikira mʼmphepete mwa phiri loyangʼanana ndi chigwa cha Beni Hinomu, kumpoto kwa chigwa cha Refaimu. Anapitirira kutsikira ku chigwa cha Hinomu kummwera kwa chitunda cha Ayebusi mpaka ku Eni Rogeli. 17 Kenaka anakhotera kumpoto kupita ku Eni-Semesi, kupitirira mpaka ku Geliloti amene amayangʼanana ndi pokwera pa Adumimu. Kenaka malire anatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. 18 Anabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Beti Araba ndi kutsikabe mpaka ku chigwa cha Yorodani. 19 Anabzolanso cha kumpoto kwa chitunda cha Beti-Hogila kukafika cha kumpoto ku gombe la Nyanja ya Mchere kumene mtsinje wa Yorodani umathirirako, cha kummwera kwenikweni. Awa anali malire a kummwera. 20 Yorodani ndiye anali malire a mbali ya kummawa.Awa anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira. 21 Mabanja a fuko la Benjamini anali ndi mizinda iyi;Yeriko, Beti-Hogila, Emeki Kezizi, 22 Beti-Araba, Zemaraimu, Beteli 23 Avimu, Para, Ofiri, 24 Kefari-Amoni, Ofini ndi Geba, mizinda khumi ndi awiri ndi midzi yake 25 Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti, 26 Mizipa, Kefira, Moza 27 Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28 Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake.Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.

In Other Versions

Joshua 18 in the ANGEFD

Joshua 18 in the ANTPNG2D

Joshua 18 in the AS21

Joshua 18 in the BAGH

Joshua 18 in the BBPNG

Joshua 18 in the BBT1E

Joshua 18 in the BDS

Joshua 18 in the BEV

Joshua 18 in the BHAD

Joshua 18 in the BIB

Joshua 18 in the BLPT

Joshua 18 in the BNT

Joshua 18 in the BNTABOOT

Joshua 18 in the BNTLV

Joshua 18 in the BOATCB

Joshua 18 in the BOATCB2

Joshua 18 in the BOBCV

Joshua 18 in the BOCNT

Joshua 18 in the BOECS

Joshua 18 in the BOHCB

Joshua 18 in the BOHCV

Joshua 18 in the BOHLNT

Joshua 18 in the BOHNTLTAL

Joshua 18 in the BOICB

Joshua 18 in the BOILNTAP

Joshua 18 in the BOITCV

Joshua 18 in the BOKCV

Joshua 18 in the BOKCV2

Joshua 18 in the BOKHWOG

Joshua 18 in the BOKSSV

Joshua 18 in the BOLCB

Joshua 18 in the BOLCB2

Joshua 18 in the BOMCV

Joshua 18 in the BONAV

Joshua 18 in the BONCB

Joshua 18 in the BONLT

Joshua 18 in the BONUT2

Joshua 18 in the BOPLNT

Joshua 18 in the BOSCB

Joshua 18 in the BOSNC

Joshua 18 in the BOTLNT

Joshua 18 in the BOVCB

Joshua 18 in the BOYCB

Joshua 18 in the BPBB

Joshua 18 in the BPH

Joshua 18 in the BSB

Joshua 18 in the CCB

Joshua 18 in the CUV

Joshua 18 in the CUVS

Joshua 18 in the DBT

Joshua 18 in the DGDNT

Joshua 18 in the DHNT

Joshua 18 in the DNT

Joshua 18 in the ELBE

Joshua 18 in the EMTV

Joshua 18 in the ESV

Joshua 18 in the FBV

Joshua 18 in the FEB

Joshua 18 in the GGMNT

Joshua 18 in the GNT

Joshua 18 in the HARY

Joshua 18 in the HNT

Joshua 18 in the IRVA

Joshua 18 in the IRVB

Joshua 18 in the IRVG

Joshua 18 in the IRVH

Joshua 18 in the IRVK

Joshua 18 in the IRVM

Joshua 18 in the IRVM2

Joshua 18 in the IRVO

Joshua 18 in the IRVP

Joshua 18 in the IRVT

Joshua 18 in the IRVT2

Joshua 18 in the IRVU

Joshua 18 in the ISVN

Joshua 18 in the JSNT

Joshua 18 in the KAPI

Joshua 18 in the KBT1ETNIK

Joshua 18 in the KBV

Joshua 18 in the KJV

Joshua 18 in the KNFD

Joshua 18 in the LBA

Joshua 18 in the LBLA

Joshua 18 in the LNT

Joshua 18 in the LSV

Joshua 18 in the MAAL

Joshua 18 in the MBV

Joshua 18 in the MBV2

Joshua 18 in the MHNT

Joshua 18 in the MKNFD

Joshua 18 in the MNG

Joshua 18 in the MNT

Joshua 18 in the MNT2

Joshua 18 in the MRS1T

Joshua 18 in the NAA

Joshua 18 in the NASB

Joshua 18 in the NBLA

Joshua 18 in the NBS

Joshua 18 in the NBVTP

Joshua 18 in the NET2

Joshua 18 in the NIV11

Joshua 18 in the NNT

Joshua 18 in the NNT2

Joshua 18 in the NNT3

Joshua 18 in the PDDPT

Joshua 18 in the PFNT

Joshua 18 in the RMNT

Joshua 18 in the SBIAS

Joshua 18 in the SBIBS

Joshua 18 in the SBIBS2

Joshua 18 in the SBICS

Joshua 18 in the SBIDS

Joshua 18 in the SBIGS

Joshua 18 in the SBIHS

Joshua 18 in the SBIIS

Joshua 18 in the SBIIS2

Joshua 18 in the SBIIS3

Joshua 18 in the SBIKS

Joshua 18 in the SBIKS2

Joshua 18 in the SBIMS

Joshua 18 in the SBIOS

Joshua 18 in the SBIPS

Joshua 18 in the SBISS

Joshua 18 in the SBITS

Joshua 18 in the SBITS2

Joshua 18 in the SBITS3

Joshua 18 in the SBITS4

Joshua 18 in the SBIUS

Joshua 18 in the SBIVS

Joshua 18 in the SBT

Joshua 18 in the SBT1E

Joshua 18 in the SCHL

Joshua 18 in the SNT

Joshua 18 in the SUSU

Joshua 18 in the SUSU2

Joshua 18 in the SYNO

Joshua 18 in the TBIAOTANT

Joshua 18 in the TBT1E

Joshua 18 in the TBT1E2

Joshua 18 in the TFTIP

Joshua 18 in the TFTU

Joshua 18 in the TGNTATF3T

Joshua 18 in the THAI

Joshua 18 in the TNFD

Joshua 18 in the TNT

Joshua 18 in the TNTIK

Joshua 18 in the TNTIL

Joshua 18 in the TNTIN

Joshua 18 in the TNTIP

Joshua 18 in the TNTIZ

Joshua 18 in the TOMA

Joshua 18 in the TTENT

Joshua 18 in the UBG

Joshua 18 in the UGV

Joshua 18 in the UGV2

Joshua 18 in the UGV3

Joshua 18 in the VBL

Joshua 18 in the VDCC

Joshua 18 in the YALU

Joshua 18 in the YAPE

Joshua 18 in the YBVTP

Joshua 18 in the ZBP