Leviticus 10 (BOGWICC)
1 Ana a Aaroni, Nadabu ndi Abihu, aliyense anatenga chofukizira lubani chake nayikamo makala a moto ndi kuthiramo lubani. Iwo anapereka pamaso pa Yehova moto wachilendo, moto umene Yehova sanawalamule. 2 Choncho moto unatuluka pamaso pa Yehova ndi kuwapsereza, ndipo anafa pamaso pa Yehova. 3 Pamenepo Mose anawuza Aaroni kuti, “Pajatu Yehova ananena kuti,“ ‘Kwa iwo amene amandiyandikirandidzaonetsa ulemerero wanga;pamaso pa anthu onsendidzalemekezedwa.’ ”Aaroni anakhala chete wosayankhula. 4 Mose anayitana Misaeli ndi Elizafani, ana a Uzieli, abambo angʼono a Aaroni, ndipo anawawuza kuti, “Bwerani kuno mudzachotse abale anuwa pa malo wopatulika ndi kuwatulutsira kunja kwa msasa.” 5 Choncho anabwera atavala minjiro yawo ndipo anawatenga ndi kuwatulutsa kunja kwa msasawo monga momwe Mose analamulira. 6 Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto. 7 Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano, mungafe, chifukwa munadzozedwa ndi mafuta a Yehova kukhala ansembe.” Choncho iwo anachita monga Mose ananenera. 8 Pambuyo pake Yehova anayankhula ndi Aaroni nati, 9 “Iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa pamene mukulowa mu tenti ya msonkhano kuti mungafe. Ili ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. 10 Muzisiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba, pakati pa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyeretsedwa, 11 ndipo muyenera kuphunzitsa Aisraeli onse malamulo amene Yehova wakupatsani kudzera mwa Mose.” 12 Mose anawuza Aaroni ndi ana ake otsalawo, Eliezara ndi Itamara kuti, “Tengani zopereka zachakudya zopanda yisiti zimene zatsala pa nsembe zopsereza za kwa Yehova ndipo muzidye pafupi ndi guwa pakuti ndi zopatulika kwambiri. 13 Muzidye pa malo wopatulika chifukwa zimenezi ndi gawo lako ndi la ana ako pa zopereka zopsereza kwa Yehova. Izitu ndi zimene Yehova anandilamulira. 14 Koma iwe pamodzi ndi ana ako aamuna ndi aakazi muzidya chidale chimene chinaweyulidwa ndi ntchafu zimene zinaperekedwa nsembe. Muzidye pamalo woyeretsedwa. Zimenezi zaperekedwa kwa iwe ndi ana ako monga gawo lanu pa zopereka zachiyanjano zimene apereka Aisraeli. 15 Ntchafu imene inaperekedwayo ndi chidale chomwe chinaweyulidwacho abwere nazo pamodzi ndi nsembe ya mafuta ya Yehova yotentha pa moto, ndipo uziweyule kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala zako ndi ana ako nthawi zonse monga walamulira Yehova.” 16 Pambuyo pake Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yopepesera machimo koma anapeza kuti anayitentha kale. Apa Mose anakalipira Eliezara ndi Itamara, ana a Aaroni otsala aja nati, 17 “Chifukwa chiyani simunadyere pamalo wopatulika nsembe yopepesera machimo ija? Kodi imene ija siyopatulika? Kodi Yehova sanapereke nyamayo kwa inu kuti muchotse machimo a mpingo wonse powachitira mwambo wa nsembe yopepesera machimo pamaso pa Yehova? 18 Pakuti magazi ake sanalowe nawo ku Malo Wopatulika, mukanadya nyama ya mbuziyo pa malo wopatulikawo monga Yehova analamulira.” 19 Aaroni anamuyankha Mose kuti, “Lero anthu apereka nsembe yawo yopepesera machimo ndiponso nsembe yawo yopsereza pamaso pa Yehova komabe zinthu zoterezi zandichitikira. Kodi Yehova akanakondwa ndikanadya nsembe yopepesera machimo lero?” 20 Pamene Mose anamva zimenezi, anakhutira.
In Other Versions
Leviticus 10 in the ANGEFD
Leviticus 10 in the ANTPNG2D
Leviticus 10 in the AS21
Leviticus 10 in the BAGH
Leviticus 10 in the BBPNG
Leviticus 10 in the BBT1E
Leviticus 10 in the BDS
Leviticus 10 in the BEV
Leviticus 10 in the BHAD
Leviticus 10 in the BIB
Leviticus 10 in the BLPT
Leviticus 10 in the BNT
Leviticus 10 in the BNTABOOT
Leviticus 10 in the BNTLV
Leviticus 10 in the BOATCB
Leviticus 10 in the BOATCB2
Leviticus 10 in the BOBCV
Leviticus 10 in the BOCNT
Leviticus 10 in the BOECS
Leviticus 10 in the BOHCB
Leviticus 10 in the BOHCV
Leviticus 10 in the BOHLNT
Leviticus 10 in the BOHNTLTAL
Leviticus 10 in the BOICB
Leviticus 10 in the BOILNTAP
Leviticus 10 in the BOITCV
Leviticus 10 in the BOKCV
Leviticus 10 in the BOKCV2
Leviticus 10 in the BOKHWOG
Leviticus 10 in the BOKSSV
Leviticus 10 in the BOLCB
Leviticus 10 in the BOLCB2
Leviticus 10 in the BOMCV
Leviticus 10 in the BONAV
Leviticus 10 in the BONCB
Leviticus 10 in the BONLT
Leviticus 10 in the BONUT2
Leviticus 10 in the BOPLNT
Leviticus 10 in the BOSCB
Leviticus 10 in the BOSNC
Leviticus 10 in the BOTLNT
Leviticus 10 in the BOVCB
Leviticus 10 in the BOYCB
Leviticus 10 in the BPBB
Leviticus 10 in the BPH
Leviticus 10 in the BSB
Leviticus 10 in the CCB
Leviticus 10 in the CUV
Leviticus 10 in the CUVS
Leviticus 10 in the DBT
Leviticus 10 in the DGDNT
Leviticus 10 in the DHNT
Leviticus 10 in the DNT
Leviticus 10 in the ELBE
Leviticus 10 in the EMTV
Leviticus 10 in the ESV
Leviticus 10 in the FBV
Leviticus 10 in the FEB
Leviticus 10 in the GGMNT
Leviticus 10 in the GNT
Leviticus 10 in the HARY
Leviticus 10 in the HNT
Leviticus 10 in the IRVA
Leviticus 10 in the IRVB
Leviticus 10 in the IRVG
Leviticus 10 in the IRVH
Leviticus 10 in the IRVK
Leviticus 10 in the IRVM
Leviticus 10 in the IRVM2
Leviticus 10 in the IRVO
Leviticus 10 in the IRVP
Leviticus 10 in the IRVT
Leviticus 10 in the IRVT2
Leviticus 10 in the IRVU
Leviticus 10 in the ISVN
Leviticus 10 in the JSNT
Leviticus 10 in the KAPI
Leviticus 10 in the KBT1ETNIK
Leviticus 10 in the KBV
Leviticus 10 in the KJV
Leviticus 10 in the KNFD
Leviticus 10 in the LBA
Leviticus 10 in the LBLA
Leviticus 10 in the LNT
Leviticus 10 in the LSV
Leviticus 10 in the MAAL
Leviticus 10 in the MBV
Leviticus 10 in the MBV2
Leviticus 10 in the MHNT
Leviticus 10 in the MKNFD
Leviticus 10 in the MNG
Leviticus 10 in the MNT
Leviticus 10 in the MNT2
Leviticus 10 in the MRS1T
Leviticus 10 in the NAA
Leviticus 10 in the NASB
Leviticus 10 in the NBLA
Leviticus 10 in the NBS
Leviticus 10 in the NBVTP
Leviticus 10 in the NET2
Leviticus 10 in the NIV11
Leviticus 10 in the NNT
Leviticus 10 in the NNT2
Leviticus 10 in the NNT3
Leviticus 10 in the PDDPT
Leviticus 10 in the PFNT
Leviticus 10 in the RMNT
Leviticus 10 in the SBIAS
Leviticus 10 in the SBIBS
Leviticus 10 in the SBIBS2
Leviticus 10 in the SBICS
Leviticus 10 in the SBIDS
Leviticus 10 in the SBIGS
Leviticus 10 in the SBIHS
Leviticus 10 in the SBIIS
Leviticus 10 in the SBIIS2
Leviticus 10 in the SBIIS3
Leviticus 10 in the SBIKS
Leviticus 10 in the SBIKS2
Leviticus 10 in the SBIMS
Leviticus 10 in the SBIOS
Leviticus 10 in the SBIPS
Leviticus 10 in the SBISS
Leviticus 10 in the SBITS
Leviticus 10 in the SBITS2
Leviticus 10 in the SBITS3
Leviticus 10 in the SBITS4
Leviticus 10 in the SBIUS
Leviticus 10 in the SBIVS
Leviticus 10 in the SBT
Leviticus 10 in the SBT1E
Leviticus 10 in the SCHL
Leviticus 10 in the SNT
Leviticus 10 in the SUSU
Leviticus 10 in the SUSU2
Leviticus 10 in the SYNO
Leviticus 10 in the TBIAOTANT
Leviticus 10 in the TBT1E
Leviticus 10 in the TBT1E2
Leviticus 10 in the TFTIP
Leviticus 10 in the TFTU
Leviticus 10 in the TGNTATF3T
Leviticus 10 in the THAI
Leviticus 10 in the TNFD
Leviticus 10 in the TNT
Leviticus 10 in the TNTIK
Leviticus 10 in the TNTIL
Leviticus 10 in the TNTIN
Leviticus 10 in the TNTIP
Leviticus 10 in the TNTIZ
Leviticus 10 in the TOMA
Leviticus 10 in the TTENT
Leviticus 10 in the UBG
Leviticus 10 in the UGV
Leviticus 10 in the UGV2
Leviticus 10 in the UGV3
Leviticus 10 in the VBL
Leviticus 10 in the VDCC
Leviticus 10 in the YALU
Leviticus 10 in the YAPE
Leviticus 10 in the YBVTP
Leviticus 10 in the ZBP