Leviticus 15 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 2 “Yankhulani ndi Aisraeli ndipo muwawuze kuti, ‘Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zotulukazo ndi zonyansa ndithu. 3 Lamulo lokhudza kudziyipitsira ndi zotuluka ku maliseche a munthu nali: Malisechewo akamatulukabe mafinya, kaya aleka, munthuyo adzakhala wodetsedwa: 4 “ ‘Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonapo, ndiponso chinthu chilichonse chimene akhalepo chidzakhala chodetsedwa. 5 Aliyense wokhudza bedi la munthuyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 6 Aliyense wokhala pa chinthu chimene munthu wotulutsa mafinyayo anakhalapo, achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 7 “ ‘Aliyense wokhudza thupi la munthu amene akutulutsa mafinyayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 8 “ ‘Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu munthu wina amene ndi woyeretsedwa, munthu ameneyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 9 “ ‘Chilichonse chimene munthuyo akhalira akakwera pa kavalo chidzakhala chodetsedwa. 10 Ndipo aliyense wokhudza chimene anakhalira munthuyo adzakhala wodetsedwanso mpaka madzulo. Aliyense wonyamula chinthucho achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 11 “ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akakhudza munthu aliyense asanasambe mʼmanja, wokhudzidwayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 12 “ ‘Mʼphika wadothi umene munthu wotulutsa mafinyayo wakhudza awuphwanye, ndipo chiwiya chilichonse chamtengo achitsuke ndi madzi. 13 “ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, awerenge masiku asanu ndi awiri akuyeretsedwa kwake kenaka achape zovala zake ndi kusamba pa kasupe, ndipo adzayeretsedwa. 14 Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri kapena mawunda a nkhunda awiri ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova pa khomo pa tenti ya msonkhano ndipo azipereke kwa wansembe. 15 Wansembe apereke zimenezo: imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wotulutsa mafinya uja pamaso pa Yehova. 16 “ ‘Mwamuna akataya pansi mbewu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 17 Chovala chilichonse kapena chikopa chilichonse pomwe pagwera mbewu yaumunayo achichape, komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo. 18 Mwamuna akagona ndi mkazi wake nataya mbewu yake yaumuna, onse awiriwo asambe. Komabe adzakhala odetsedwa mpaka madzulo. 19 “ ‘Mkazi akakhala wosamba ndipo ikakhala kuti ndi nthawi yake yeniyeni yosamba, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Aliyense amene adzamukhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 20 “ ‘Chilichonse chimene mkaziyo agonera pa nthawi yake yosamba chidzakhala chodetsedwa, ndipo chilichonse chimene adzakhalira chidzakhalanso chodetsedwa. 21 Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Aliyense wokhudza chimene wakhalapo achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 23 Kaya ndi bedi kapena chinthu china chilichonse chimene anakhalapo, ngati munthu wina akhudza chinthucho, munthuyo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 24 “ ‘Mwamuna aliyense akagona naye ndipo magazi osamba kwake ndi kumukhudza, munthuyo adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri, ndipo bedi limene wagonapo lidzakhalanso lodetsedwa. 25 “ ‘Mkazi akataya magazi masiku ambiri, wosakhala pa nthawi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira nthawi yake yosamba, mkaziyo adzakhala wodetsedwa nthawi yonse imene akutaya magazi, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba. 26 Bedi lililonse limene mkaziyo adzagonapo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, ndiponso chilichonse chimene wakhalira chidzakhala chodetsedwa monga mmene chimakhalira chodetsedwa pa nthawi yake yosamba. 27 Aliyense amene adzakhudza zinthu zimenezo adzakhala wodetsedwa ndipo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28 “ ‘Nthawi yosamba ikatha, mkaziyo awerenge masiku asanu ndi awiri, ndipo masikuwo akatha adzakhala woyeretsedwa. 29 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiwa ziwiri kapena mawunda awiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pa khomo la Tenti ya Msonkhano. 30 Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Yehova chifukwa cha matenda ake wosamba aja. 31 “ ‘Choncho muwayeretsa ana a Israeli nʼkudetsedwa kwawo kuti angafe pochita tchimo lowadetsa limene polichita limadetsa malo anga wokhalamo amene ali pakati pawo.’ ” 32 Amenewa ndi malamulo a munthu amene akutuluka mafinya kumaliseche kwake, komanso a munthu aliyense amene wadetsedwa ndi mbewu yaumuna, 33 mkazi wodwala chifukwa cha msambo komanso a mwamuna kapena mkazi amene akutulutsa mafinya kumaliseche kwake ndi mwamuna wogona ndi mkazi amene akusamba.

In Other Versions

Leviticus 15 in the ANGEFD

Leviticus 15 in the ANTPNG2D

Leviticus 15 in the AS21

Leviticus 15 in the BAGH

Leviticus 15 in the BBPNG

Leviticus 15 in the BBT1E

Leviticus 15 in the BDS

Leviticus 15 in the BEV

Leviticus 15 in the BHAD

Leviticus 15 in the BIB

Leviticus 15 in the BLPT

Leviticus 15 in the BNT

Leviticus 15 in the BNTABOOT

Leviticus 15 in the BNTLV

Leviticus 15 in the BOATCB

Leviticus 15 in the BOATCB2

Leviticus 15 in the BOBCV

Leviticus 15 in the BOCNT

Leviticus 15 in the BOECS

Leviticus 15 in the BOHCB

Leviticus 15 in the BOHCV

Leviticus 15 in the BOHLNT

Leviticus 15 in the BOHNTLTAL

Leviticus 15 in the BOICB

Leviticus 15 in the BOILNTAP

Leviticus 15 in the BOITCV

Leviticus 15 in the BOKCV

Leviticus 15 in the BOKCV2

Leviticus 15 in the BOKHWOG

Leviticus 15 in the BOKSSV

Leviticus 15 in the BOLCB

Leviticus 15 in the BOLCB2

Leviticus 15 in the BOMCV

Leviticus 15 in the BONAV

Leviticus 15 in the BONCB

Leviticus 15 in the BONLT

Leviticus 15 in the BONUT2

Leviticus 15 in the BOPLNT

Leviticus 15 in the BOSCB

Leviticus 15 in the BOSNC

Leviticus 15 in the BOTLNT

Leviticus 15 in the BOVCB

Leviticus 15 in the BOYCB

Leviticus 15 in the BPBB

Leviticus 15 in the BPH

Leviticus 15 in the BSB

Leviticus 15 in the CCB

Leviticus 15 in the CUV

Leviticus 15 in the CUVS

Leviticus 15 in the DBT

Leviticus 15 in the DGDNT

Leviticus 15 in the DHNT

Leviticus 15 in the DNT

Leviticus 15 in the ELBE

Leviticus 15 in the EMTV

Leviticus 15 in the ESV

Leviticus 15 in the FBV

Leviticus 15 in the FEB

Leviticus 15 in the GGMNT

Leviticus 15 in the GNT

Leviticus 15 in the HARY

Leviticus 15 in the HNT

Leviticus 15 in the IRVA

Leviticus 15 in the IRVB

Leviticus 15 in the IRVG

Leviticus 15 in the IRVH

Leviticus 15 in the IRVK

Leviticus 15 in the IRVM

Leviticus 15 in the IRVM2

Leviticus 15 in the IRVO

Leviticus 15 in the IRVP

Leviticus 15 in the IRVT

Leviticus 15 in the IRVT2

Leviticus 15 in the IRVU

Leviticus 15 in the ISVN

Leviticus 15 in the JSNT

Leviticus 15 in the KAPI

Leviticus 15 in the KBT1ETNIK

Leviticus 15 in the KBV

Leviticus 15 in the KJV

Leviticus 15 in the KNFD

Leviticus 15 in the LBA

Leviticus 15 in the LBLA

Leviticus 15 in the LNT

Leviticus 15 in the LSV

Leviticus 15 in the MAAL

Leviticus 15 in the MBV

Leviticus 15 in the MBV2

Leviticus 15 in the MHNT

Leviticus 15 in the MKNFD

Leviticus 15 in the MNG

Leviticus 15 in the MNT

Leviticus 15 in the MNT2

Leviticus 15 in the MRS1T

Leviticus 15 in the NAA

Leviticus 15 in the NASB

Leviticus 15 in the NBLA

Leviticus 15 in the NBS

Leviticus 15 in the NBVTP

Leviticus 15 in the NET2

Leviticus 15 in the NIV11

Leviticus 15 in the NNT

Leviticus 15 in the NNT2

Leviticus 15 in the NNT3

Leviticus 15 in the PDDPT

Leviticus 15 in the PFNT

Leviticus 15 in the RMNT

Leviticus 15 in the SBIAS

Leviticus 15 in the SBIBS

Leviticus 15 in the SBIBS2

Leviticus 15 in the SBICS

Leviticus 15 in the SBIDS

Leviticus 15 in the SBIGS

Leviticus 15 in the SBIHS

Leviticus 15 in the SBIIS

Leviticus 15 in the SBIIS2

Leviticus 15 in the SBIIS3

Leviticus 15 in the SBIKS

Leviticus 15 in the SBIKS2

Leviticus 15 in the SBIMS

Leviticus 15 in the SBIOS

Leviticus 15 in the SBIPS

Leviticus 15 in the SBISS

Leviticus 15 in the SBITS

Leviticus 15 in the SBITS2

Leviticus 15 in the SBITS3

Leviticus 15 in the SBITS4

Leviticus 15 in the SBIUS

Leviticus 15 in the SBIVS

Leviticus 15 in the SBT

Leviticus 15 in the SBT1E

Leviticus 15 in the SCHL

Leviticus 15 in the SNT

Leviticus 15 in the SUSU

Leviticus 15 in the SUSU2

Leviticus 15 in the SYNO

Leviticus 15 in the TBIAOTANT

Leviticus 15 in the TBT1E

Leviticus 15 in the TBT1E2

Leviticus 15 in the TFTIP

Leviticus 15 in the TFTU

Leviticus 15 in the TGNTATF3T

Leviticus 15 in the THAI

Leviticus 15 in the TNFD

Leviticus 15 in the TNT

Leviticus 15 in the TNTIK

Leviticus 15 in the TNTIL

Leviticus 15 in the TNTIN

Leviticus 15 in the TNTIP

Leviticus 15 in the TNTIZ

Leviticus 15 in the TOMA

Leviticus 15 in the TTENT

Leviticus 15 in the UBG

Leviticus 15 in the UGV

Leviticus 15 in the UGV2

Leviticus 15 in the UGV3

Leviticus 15 in the VBL

Leviticus 15 in the VDCC

Leviticus 15 in the YALU

Leviticus 15 in the YAPE

Leviticus 15 in the YBVTP

Leviticus 15 in the ZBP