Luke 17 (BOGWICC)

1 Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo. 2 Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa. 3 Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha. “Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni. 4 Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.” 5 Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!” 6 Yesu anayankha kuti, “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani. 7 “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu anali ndi wantchito wolima kapena woweta nkhosa, kodi angawuze wantchitoyo atabwera ku munda kuti, ‘Tsopano bwera kuno khala pansi kuti udye?’ 8 Kodi sangamuwuze kuti, ‘Konzere chakudya cha madzulo, iweyo ukonzeke ndipo undidikirire pamene ndikudya ndi kumwa; kenaka ukhoza kudya ndi kumwa?’ 9 Kodi iye angathokoze wantchitoyo chifukwa chochita chimene anawuzidwa kuchita? 10 Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munawuzidwa, muzinena kuti, ‘Ndife antchito osayenera; tangogwira ntchito yathu basi.’ ” 11 Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu. 12 Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali 13 ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!” 14 Iye atawaona, anati, “Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe.” Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa. 15 Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. 16 Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya. 17 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti? 18 Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?” 19 Pamenepo anati kwa iye, “Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.” 20 Ndipo Afarisi atamufunsa Iye kuti, ufumu wa Mulungu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso, 21 kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” 22 Kenaka Iye anati kwa ophunzira ake, “Masiku akubwera pamene inu mudzalakalaka mutaona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. 23 Anthu adzakuwuzani kuti, ‘Uyo ali apoyo!’ kapena ‘Uyu ali apa!’ Musawathamangire iwo. 24 Pakuti monga mphenzi ingʼanima ndi kuwala kuchokera mbali ina ya thambo kufikira inzake, koteronso adzakhala ali Mwana wa Munthu pa tsiku lake. 25 Koma poyamba ayenera kuzunzika mu zambiri ndi kukanidwa ndi mʼbado uno. 26 “Monga mmene zinkachitikira nthawi ya Nowa, momwemonso zidzachitikanso nthawi ya Mwana wa Munthu. 27 Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo. 28 “Zinalinso chimodzimodzi nthawi ya Loti. Anthu ankadya ndi kumwa, kugula ndi kugulitsa, kudzala ndi kumanga. 29 Koma tsiku limene Loti anachoka ku Sodomu, moto ndi sulufule zinavumbwa kuchokera kumwamba ndi kuwawononga onsewo. 30 “Zidzakhalanso choncho Mwana wa Munthu akadzaonekera. 31 Tsiku limenelo munthu amene ali pa denga la nyumba yake, ndi katundu wake ali mʼnyumbamo, asadzatsike kukatenga. Chimodzimodzinso, munthu amene adzakhale ali ku munda asadzabwerere kukatenga chilichonse. 32 Kumbukirani mkazi wa Loti! 33 Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga. 34 Ine ndikukuwuzani inu, usiku umenewo anthu awiri adzagona pa mphasa imodzi; wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa. 35 Amayi awiri adzakhala pamodzi akusinja; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa. 36 Amuna awiri adzakhala akulima mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.” 37 Iwo anafunsa kuti, “Ambuye, kodi zimenezi zidzachitikira kuti?”Iye anayankha kuti, “Kumene kuli mtembo, nʼkumene makwangwala amasonkhanako.”

In Other Versions

Luke 17 in the ANGEFD

Luke 17 in the ANTPNG2D

Luke 17 in the AS21

Luke 17 in the BAGH

Luke 17 in the BBPNG

Luke 17 in the BBT1E

Luke 17 in the BDS

Luke 17 in the BEV

Luke 17 in the BHAD

Luke 17 in the BIB

Luke 17 in the BLPT

Luke 17 in the BNT

Luke 17 in the BNTABOOT

Luke 17 in the BNTLV

Luke 17 in the BOATCB

Luke 17 in the BOATCB2

Luke 17 in the BOBCV

Luke 17 in the BOCNT

Luke 17 in the BOECS

Luke 17 in the BOHCB

Luke 17 in the BOHCV

Luke 17 in the BOHLNT

Luke 17 in the BOHNTLTAL

Luke 17 in the BOICB

Luke 17 in the BOILNTAP

Luke 17 in the BOITCV

Luke 17 in the BOKCV

Luke 17 in the BOKCV2

Luke 17 in the BOKHWOG

Luke 17 in the BOKSSV

Luke 17 in the BOLCB

Luke 17 in the BOLCB2

Luke 17 in the BOMCV

Luke 17 in the BONAV

Luke 17 in the BONCB

Luke 17 in the BONLT

Luke 17 in the BONUT2

Luke 17 in the BOPLNT

Luke 17 in the BOSCB

Luke 17 in the BOSNC

Luke 17 in the BOTLNT

Luke 17 in the BOVCB

Luke 17 in the BOYCB

Luke 17 in the BPBB

Luke 17 in the BPH

Luke 17 in the BSB

Luke 17 in the CCB

Luke 17 in the CUV

Luke 17 in the CUVS

Luke 17 in the DBT

Luke 17 in the DGDNT

Luke 17 in the DHNT

Luke 17 in the DNT

Luke 17 in the ELBE

Luke 17 in the EMTV

Luke 17 in the ESV

Luke 17 in the FBV

Luke 17 in the FEB

Luke 17 in the GGMNT

Luke 17 in the GNT

Luke 17 in the HARY

Luke 17 in the HNT

Luke 17 in the IRVA

Luke 17 in the IRVB

Luke 17 in the IRVG

Luke 17 in the IRVH

Luke 17 in the IRVK

Luke 17 in the IRVM

Luke 17 in the IRVM2

Luke 17 in the IRVO

Luke 17 in the IRVP

Luke 17 in the IRVT

Luke 17 in the IRVT2

Luke 17 in the IRVU

Luke 17 in the ISVN

Luke 17 in the JSNT

Luke 17 in the KAPI

Luke 17 in the KBT1ETNIK

Luke 17 in the KBV

Luke 17 in the KJV

Luke 17 in the KNFD

Luke 17 in the LBA

Luke 17 in the LBLA

Luke 17 in the LNT

Luke 17 in the LSV

Luke 17 in the MAAL

Luke 17 in the MBV

Luke 17 in the MBV2

Luke 17 in the MHNT

Luke 17 in the MKNFD

Luke 17 in the MNG

Luke 17 in the MNT

Luke 17 in the MNT2

Luke 17 in the MRS1T

Luke 17 in the NAA

Luke 17 in the NASB

Luke 17 in the NBLA

Luke 17 in the NBS

Luke 17 in the NBVTP

Luke 17 in the NET2

Luke 17 in the NIV11

Luke 17 in the NNT

Luke 17 in the NNT2

Luke 17 in the NNT3

Luke 17 in the PDDPT

Luke 17 in the PFNT

Luke 17 in the RMNT

Luke 17 in the SBIAS

Luke 17 in the SBIBS

Luke 17 in the SBIBS2

Luke 17 in the SBICS

Luke 17 in the SBIDS

Luke 17 in the SBIGS

Luke 17 in the SBIHS

Luke 17 in the SBIIS

Luke 17 in the SBIIS2

Luke 17 in the SBIIS3

Luke 17 in the SBIKS

Luke 17 in the SBIKS2

Luke 17 in the SBIMS

Luke 17 in the SBIOS

Luke 17 in the SBIPS

Luke 17 in the SBISS

Luke 17 in the SBITS

Luke 17 in the SBITS2

Luke 17 in the SBITS3

Luke 17 in the SBITS4

Luke 17 in the SBIUS

Luke 17 in the SBIVS

Luke 17 in the SBT

Luke 17 in the SBT1E

Luke 17 in the SCHL

Luke 17 in the SNT

Luke 17 in the SUSU

Luke 17 in the SUSU2

Luke 17 in the SYNO

Luke 17 in the TBIAOTANT

Luke 17 in the TBT1E

Luke 17 in the TBT1E2

Luke 17 in the TFTIP

Luke 17 in the TFTU

Luke 17 in the TGNTATF3T

Luke 17 in the THAI

Luke 17 in the TNFD

Luke 17 in the TNT

Luke 17 in the TNTIK

Luke 17 in the TNTIL

Luke 17 in the TNTIN

Luke 17 in the TNTIP

Luke 17 in the TNTIZ

Luke 17 in the TOMA

Luke 17 in the TTENT

Luke 17 in the UBG

Luke 17 in the UGV

Luke 17 in the UGV2

Luke 17 in the UGV3

Luke 17 in the VBL

Luke 17 in the VDCC

Luke 17 in the YALU

Luke 17 in the YAPE

Luke 17 in the YBVTP

Luke 17 in the ZBP