Luke 24 (BOGWICC)

1 Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda. 2 Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika 3 ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. 4 Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. 5 Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? 6 Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: 7 ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ” 8 Ndipo anakumbukira mawu ake. 9 Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse. 10 Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi. 11 Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru. 12 Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo. 13 Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu. 14 Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo. 15 Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi; 16 koma iwo sanamuzindikire. 17 Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?”Iwo anayima ndi nkhope zakugwa. 18 Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?” 19 Iye anafunsa kuti, “Zinthu zotani?”Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse. 20 Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye; 21 koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi. 22 Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa 23 koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo. 24 Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.” 25 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena! 26 Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?” 27 Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini. 28 Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira. 29 Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo. 30 Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira. 31 Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo. 32 Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?” 33 Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi 34 ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.” 35 Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi. 36 Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.” 37 Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa. 38 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu? 39 Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.” 40 Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. 41 Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” 42 Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika. 43 Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona. 44 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.” 45 Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba. 46 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu. 47 Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu. 48 Inu ndinu mboni za zimenezi. 49 Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.” 50 Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa. 51 Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba. 52 Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. 53 Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.

In Other Versions

Luke 24 in the ANGEFD

Luke 24 in the ANTPNG2D

Luke 24 in the AS21

Luke 24 in the BAGH

Luke 24 in the BBPNG

Luke 24 in the BBT1E

Luke 24 in the BDS

Luke 24 in the BEV

Luke 24 in the BHAD

Luke 24 in the BIB

Luke 24 in the BLPT

Luke 24 in the BNT

Luke 24 in the BNTABOOT

Luke 24 in the BNTLV

Luke 24 in the BOATCB

Luke 24 in the BOATCB2

Luke 24 in the BOBCV

Luke 24 in the BOCNT

Luke 24 in the BOECS

Luke 24 in the BOHCB

Luke 24 in the BOHCV

Luke 24 in the BOHLNT

Luke 24 in the BOHNTLTAL

Luke 24 in the BOICB

Luke 24 in the BOILNTAP

Luke 24 in the BOITCV

Luke 24 in the BOKCV

Luke 24 in the BOKCV2

Luke 24 in the BOKHWOG

Luke 24 in the BOKSSV

Luke 24 in the BOLCB

Luke 24 in the BOLCB2

Luke 24 in the BOMCV

Luke 24 in the BONAV

Luke 24 in the BONCB

Luke 24 in the BONLT

Luke 24 in the BONUT2

Luke 24 in the BOPLNT

Luke 24 in the BOSCB

Luke 24 in the BOSNC

Luke 24 in the BOTLNT

Luke 24 in the BOVCB

Luke 24 in the BOYCB

Luke 24 in the BPBB

Luke 24 in the BPH

Luke 24 in the BSB

Luke 24 in the CCB

Luke 24 in the CUV

Luke 24 in the CUVS

Luke 24 in the DBT

Luke 24 in the DGDNT

Luke 24 in the DHNT

Luke 24 in the DNT

Luke 24 in the ELBE

Luke 24 in the EMTV

Luke 24 in the ESV

Luke 24 in the FBV

Luke 24 in the FEB

Luke 24 in the GGMNT

Luke 24 in the GNT

Luke 24 in the HARY

Luke 24 in the HNT

Luke 24 in the IRVA

Luke 24 in the IRVB

Luke 24 in the IRVG

Luke 24 in the IRVH

Luke 24 in the IRVK

Luke 24 in the IRVM

Luke 24 in the IRVM2

Luke 24 in the IRVO

Luke 24 in the IRVP

Luke 24 in the IRVT

Luke 24 in the IRVT2

Luke 24 in the IRVU

Luke 24 in the ISVN

Luke 24 in the JSNT

Luke 24 in the KAPI

Luke 24 in the KBT1ETNIK

Luke 24 in the KBV

Luke 24 in the KJV

Luke 24 in the KNFD

Luke 24 in the LBA

Luke 24 in the LBLA

Luke 24 in the LNT

Luke 24 in the LSV

Luke 24 in the MAAL

Luke 24 in the MBV

Luke 24 in the MBV2

Luke 24 in the MHNT

Luke 24 in the MKNFD

Luke 24 in the MNG

Luke 24 in the MNT

Luke 24 in the MNT2

Luke 24 in the MRS1T

Luke 24 in the NAA

Luke 24 in the NASB

Luke 24 in the NBLA

Luke 24 in the NBS

Luke 24 in the NBVTP

Luke 24 in the NET2

Luke 24 in the NIV11

Luke 24 in the NNT

Luke 24 in the NNT2

Luke 24 in the NNT3

Luke 24 in the PDDPT

Luke 24 in the PFNT

Luke 24 in the RMNT

Luke 24 in the SBIAS

Luke 24 in the SBIBS

Luke 24 in the SBIBS2

Luke 24 in the SBICS

Luke 24 in the SBIDS

Luke 24 in the SBIGS

Luke 24 in the SBIHS

Luke 24 in the SBIIS

Luke 24 in the SBIIS2

Luke 24 in the SBIIS3

Luke 24 in the SBIKS

Luke 24 in the SBIKS2

Luke 24 in the SBIMS

Luke 24 in the SBIOS

Luke 24 in the SBIPS

Luke 24 in the SBISS

Luke 24 in the SBITS

Luke 24 in the SBITS2

Luke 24 in the SBITS3

Luke 24 in the SBITS4

Luke 24 in the SBIUS

Luke 24 in the SBIVS

Luke 24 in the SBT

Luke 24 in the SBT1E

Luke 24 in the SCHL

Luke 24 in the SNT

Luke 24 in the SUSU

Luke 24 in the SUSU2

Luke 24 in the SYNO

Luke 24 in the TBIAOTANT

Luke 24 in the TBT1E

Luke 24 in the TBT1E2

Luke 24 in the TFTIP

Luke 24 in the TFTU

Luke 24 in the TGNTATF3T

Luke 24 in the THAI

Luke 24 in the TNFD

Luke 24 in the TNT

Luke 24 in the TNTIK

Luke 24 in the TNTIL

Luke 24 in the TNTIN

Luke 24 in the TNTIP

Luke 24 in the TNTIZ

Luke 24 in the TOMA

Luke 24 in the TTENT

Luke 24 in the UBG

Luke 24 in the UGV

Luke 24 in the UGV2

Luke 24 in the UGV3

Luke 24 in the VBL

Luke 24 in the VDCC

Luke 24 in the YALU

Luke 24 in the YAPE

Luke 24 in the YBVTP

Luke 24 in the ZBP