Matthew 1 (BOGWICC)

1 Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu: 2 Abrahamu anabereka Isake,Isake anabereka Yakobo,Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake. 3 Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara.Perezi anabereka Hezironi,Hezironi anabereka Aramu. 4 Aramu anabereka Aminadabu,Aminadabu anabereka Naasoni,Naasoni anabereka Salimoni. 5 Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe,Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute,Obedi anabereka Yese. 6 Yese anabereka Mfumu Davide. Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya. 7 Solomoni anabereka Rehabiamu,Rehabiamu anabereka Abiya,Abiya anabereka Asa, 8 Asa anabereka Yehosafati,Yehosafati anabereka Yoramu,Yoramu anabereka Uziya. 9 Uziya anabereka Yotamu,Yotamu anabereka Ahazi,Ahazi anabereka Hezekiya. 10 Hezekiya anabereka Manase,Manase anabereka Amoni,Amoni anabereka Yosiya. 11 Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni. 12 Ali ku ukapolo ku Babuloni,Yekoniya anabereka Salatieli,Salatieli anabereka Zerubabeli. 13 Zerubabeli anabereka Abiudi,Abiudi anabereka Eliakimu,Eliakimu anabereka Azoro. 14 Azoro anabereka Zadoki,Zadoki anabereka Akimu,Akimu anabereka Eliudi. 15 Eliudi anabereka Eliezara,Eliezara anabereka Matani,Matani anabereka Yakobo. 16 Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu. 17 Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi. 18 Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. 19 Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera. 20 Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. 21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.” 22 Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, 23 “Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.” 24 Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake. 25 Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.

In Other Versions

Matthew 1 in the ANGEFD

Matthew 1 in the ANTPNG2D

Matthew 1 in the AS21

Matthew 1 in the BAGH

Matthew 1 in the BBPNG

Matthew 1 in the BBT1E

Matthew 1 in the BDS

Matthew 1 in the BEV

Matthew 1 in the BHAD

Matthew 1 in the BIB

Matthew 1 in the BLPT

Matthew 1 in the BNT

Matthew 1 in the BNTABOOT

Matthew 1 in the BNTLV

Matthew 1 in the BOATCB

Matthew 1 in the BOATCB2

Matthew 1 in the BOBCV

Matthew 1 in the BOCNT

Matthew 1 in the BOECS

Matthew 1 in the BOHCB

Matthew 1 in the BOHCV

Matthew 1 in the BOHLNT

Matthew 1 in the BOHNTLTAL

Matthew 1 in the BOICB

Matthew 1 in the BOILNTAP

Matthew 1 in the BOITCV

Matthew 1 in the BOKCV

Matthew 1 in the BOKCV2

Matthew 1 in the BOKHWOG

Matthew 1 in the BOKSSV

Matthew 1 in the BOLCB

Matthew 1 in the BOLCB2

Matthew 1 in the BOMCV

Matthew 1 in the BONAV

Matthew 1 in the BONCB

Matthew 1 in the BONLT

Matthew 1 in the BONUT2

Matthew 1 in the BOPLNT

Matthew 1 in the BOSCB

Matthew 1 in the BOSNC

Matthew 1 in the BOTLNT

Matthew 1 in the BOVCB

Matthew 1 in the BOYCB

Matthew 1 in the BPBB

Matthew 1 in the BPH

Matthew 1 in the BSB

Matthew 1 in the CCB

Matthew 1 in the CUV

Matthew 1 in the CUVS

Matthew 1 in the DBT

Matthew 1 in the DGDNT

Matthew 1 in the DHNT

Matthew 1 in the DNT

Matthew 1 in the ELBE

Matthew 1 in the EMTV

Matthew 1 in the ESV

Matthew 1 in the FBV

Matthew 1 in the FEB

Matthew 1 in the GGMNT

Matthew 1 in the GNT

Matthew 1 in the HARY

Matthew 1 in the HNT

Matthew 1 in the IRVA

Matthew 1 in the IRVB

Matthew 1 in the IRVG

Matthew 1 in the IRVH

Matthew 1 in the IRVK

Matthew 1 in the IRVM

Matthew 1 in the IRVM2

Matthew 1 in the IRVO

Matthew 1 in the IRVP

Matthew 1 in the IRVT

Matthew 1 in the IRVT2

Matthew 1 in the IRVU

Matthew 1 in the ISVN

Matthew 1 in the JSNT

Matthew 1 in the KAPI

Matthew 1 in the KBT1ETNIK

Matthew 1 in the KBV

Matthew 1 in the KJV

Matthew 1 in the KNFD

Matthew 1 in the LBA

Matthew 1 in the LBLA

Matthew 1 in the LNT

Matthew 1 in the LSV

Matthew 1 in the MAAL

Matthew 1 in the MBV

Matthew 1 in the MBV2

Matthew 1 in the MHNT

Matthew 1 in the MKNFD

Matthew 1 in the MNG

Matthew 1 in the MNT

Matthew 1 in the MNT2

Matthew 1 in the MRS1T

Matthew 1 in the NAA

Matthew 1 in the NASB

Matthew 1 in the NBLA

Matthew 1 in the NBS

Matthew 1 in the NBVTP

Matthew 1 in the NET2

Matthew 1 in the NIV11

Matthew 1 in the NNT

Matthew 1 in the NNT2

Matthew 1 in the NNT3

Matthew 1 in the PDDPT

Matthew 1 in the PFNT

Matthew 1 in the RMNT

Matthew 1 in the SBIAS

Matthew 1 in the SBIBS

Matthew 1 in the SBIBS2

Matthew 1 in the SBICS

Matthew 1 in the SBIDS

Matthew 1 in the SBIGS

Matthew 1 in the SBIHS

Matthew 1 in the SBIIS

Matthew 1 in the SBIIS2

Matthew 1 in the SBIIS3

Matthew 1 in the SBIKS

Matthew 1 in the SBIKS2

Matthew 1 in the SBIMS

Matthew 1 in the SBIOS

Matthew 1 in the SBIPS

Matthew 1 in the SBISS

Matthew 1 in the SBITS

Matthew 1 in the SBITS2

Matthew 1 in the SBITS3

Matthew 1 in the SBITS4

Matthew 1 in the SBIUS

Matthew 1 in the SBIVS

Matthew 1 in the SBT

Matthew 1 in the SBT1E

Matthew 1 in the SCHL

Matthew 1 in the SNT

Matthew 1 in the SUSU

Matthew 1 in the SUSU2

Matthew 1 in the SYNO

Matthew 1 in the TBIAOTANT

Matthew 1 in the TBT1E

Matthew 1 in the TBT1E2

Matthew 1 in the TFTIP

Matthew 1 in the TFTU

Matthew 1 in the TGNTATF3T

Matthew 1 in the THAI

Matthew 1 in the TNFD

Matthew 1 in the TNT

Matthew 1 in the TNTIK

Matthew 1 in the TNTIL

Matthew 1 in the TNTIN

Matthew 1 in the TNTIP

Matthew 1 in the TNTIZ

Matthew 1 in the TOMA

Matthew 1 in the TTENT

Matthew 1 in the UBG

Matthew 1 in the UGV

Matthew 1 in the UGV2

Matthew 1 in the UGV3

Matthew 1 in the VBL

Matthew 1 in the VDCC

Matthew 1 in the YALU

Matthew 1 in the YAPE

Matthew 1 in the YBVTP

Matthew 1 in the ZBP