Matthew 11 (BOGWICC)
1 Ndipo Yesu atamaliza kulangiza ophunzira ake khumi ndi awiri aja, anachoka kumeneko kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira ku mizinda ya ku Galileya. 2 Yohane ali mʼndende anamva zimene Khristu ankachita, ndipo anatumiza ophunzira ake kukamufunsa Iye. 3 Anamufunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankanena kuti mudzabwerayu kapena tidikire wina?” 4 Yesu anayankha kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwamva ndi kuona. 5 Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. 6 Odala ndi munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.” 7 Pamene ophunzira a Yohane ankachoka, Yesu anayamba kuyankhula kwa gulu la anthu za Yohane kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kuti mukaone chiyani? Kodi bango logwedezeka ndi mphepo? 8 Nanga munkapita kukaona chiyani, munthu wovala zokongola? Ayi, wovala zokongola amakhala mʼnyumba za mafumu. 9 Nanga munkapita kukaona chiyani? Mneneri kodi? Inde ndikuwuzani kuti munkakaona woposa mneneri. 10 Uyu ndi amene malemba akunena za iye kuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu amene adzakonza njira yanu. 11 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pakati pa obadwa ndi mkazi sipanaoneke wina aliyense wamkulu woposa Yohane Mʼbatizi; komatu amene ndi wamngʼono kwambiri mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu koposa iye. 12 Kuyambira masiku a Yohane Mʼbatizi mpaka tsopano, ufumu wakumwamba ndi wolimbirana ndipo anthu amphamvu okha ndi amene akuwulanda. 13 Pakuti aneneri onse ndi malamulo ananenera kufikira nthawi ya Yohane. 14 Ndipo ngati inu mufuna kulandira izi, iyeyu ndi Eliya amene ankanena kuti adzabwera uja. 15 Iye amene ali ndi makutu amve. 16 “Kodi mʼbado uwu ndingawufanizire ndi chiyani? Uli ngati ana opezeka mʼmisika amene akuyitana anzawo nʼkumati: 17 “ ‘Tinakuyimbirani zitoliro, koma inu simunavine; ife tinayimba nyimbo zamaliro, koma inu simunalire.’ 18 Pakuti Yohane sanabwerere kudya kapena kumwa koma iwo ankanena kuti, ‘Iye anali ndi chiwanda.’ 19 Mwana wa Munthu anabwera ndi kumadya ndi kumwa koma iwo akuti, ‘Munthu wadyera, woledzera, bwenzi la amisonkho ndi bwenzi la ochimwa.’ Koma nzeru imatsimikizika kuti ndi yolondola mwa ntchito zake.” 20 Pamenepo Yesu anayamba kudzudzula mizinda imene zodabwitsa zake zambiri zinachitikamo, chifukwa chakuti sinatembenuke mtima. 21 “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betisaida! Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe zikanachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akanalapa kale atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 22 Koma ndikuwuzani inu kuti pa tsiku lachiweruzo mlandu wa Turo ndi Sidoni udzachepako kusiyana ndi wanu. 23 Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero. 24 Koma Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro mlandu wa Sodomu udzachepako kusiyana ndi wanu.” 25 Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono. 26 Inde, Atate, ichi chinali chokukomerani Inu. 27 “Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira. 28 “Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. 29 Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30 Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”
In Other Versions
Matthew 11 in the ANGEFD
Matthew 11 in the ANTPNG2D
Matthew 11 in the AS21
Matthew 11 in the BAGH
Matthew 11 in the BBPNG
Matthew 11 in the BBT1E
Matthew 11 in the BDS
Matthew 11 in the BEV
Matthew 11 in the BHAD
Matthew 11 in the BIB
Matthew 11 in the BLPT
Matthew 11 in the BNT
Matthew 11 in the BNTABOOT
Matthew 11 in the BNTLV
Matthew 11 in the BOATCB
Matthew 11 in the BOATCB2
Matthew 11 in the BOBCV
Matthew 11 in the BOCNT
Matthew 11 in the BOECS
Matthew 11 in the BOHCB
Matthew 11 in the BOHCV
Matthew 11 in the BOHLNT
Matthew 11 in the BOHNTLTAL
Matthew 11 in the BOICB
Matthew 11 in the BOILNTAP
Matthew 11 in the BOITCV
Matthew 11 in the BOKCV
Matthew 11 in the BOKCV2
Matthew 11 in the BOKHWOG
Matthew 11 in the BOKSSV
Matthew 11 in the BOLCB
Matthew 11 in the BOLCB2
Matthew 11 in the BOMCV
Matthew 11 in the BONAV
Matthew 11 in the BONCB
Matthew 11 in the BONLT
Matthew 11 in the BONUT2
Matthew 11 in the BOPLNT
Matthew 11 in the BOSCB
Matthew 11 in the BOSNC
Matthew 11 in the BOTLNT
Matthew 11 in the BOVCB
Matthew 11 in the BOYCB
Matthew 11 in the BPBB
Matthew 11 in the BPH
Matthew 11 in the BSB
Matthew 11 in the CCB
Matthew 11 in the CUV
Matthew 11 in the CUVS
Matthew 11 in the DBT
Matthew 11 in the DGDNT
Matthew 11 in the DHNT
Matthew 11 in the DNT
Matthew 11 in the ELBE
Matthew 11 in the EMTV
Matthew 11 in the ESV
Matthew 11 in the FBV
Matthew 11 in the FEB
Matthew 11 in the GGMNT
Matthew 11 in the GNT
Matthew 11 in the HARY
Matthew 11 in the HNT
Matthew 11 in the IRVA
Matthew 11 in the IRVB
Matthew 11 in the IRVG
Matthew 11 in the IRVH
Matthew 11 in the IRVK
Matthew 11 in the IRVM
Matthew 11 in the IRVM2
Matthew 11 in the IRVO
Matthew 11 in the IRVP
Matthew 11 in the IRVT
Matthew 11 in the IRVT2
Matthew 11 in the IRVU
Matthew 11 in the ISVN
Matthew 11 in the JSNT
Matthew 11 in the KAPI
Matthew 11 in the KBT1ETNIK
Matthew 11 in the KBV
Matthew 11 in the KJV
Matthew 11 in the KNFD
Matthew 11 in the LBA
Matthew 11 in the LBLA
Matthew 11 in the LNT
Matthew 11 in the LSV
Matthew 11 in the MAAL
Matthew 11 in the MBV
Matthew 11 in the MBV2
Matthew 11 in the MHNT
Matthew 11 in the MKNFD
Matthew 11 in the MNG
Matthew 11 in the MNT
Matthew 11 in the MNT2
Matthew 11 in the MRS1T
Matthew 11 in the NAA
Matthew 11 in the NASB
Matthew 11 in the NBLA
Matthew 11 in the NBS
Matthew 11 in the NBVTP
Matthew 11 in the NET2
Matthew 11 in the NIV11
Matthew 11 in the NNT
Matthew 11 in the NNT2
Matthew 11 in the NNT3
Matthew 11 in the PDDPT
Matthew 11 in the PFNT
Matthew 11 in the RMNT
Matthew 11 in the SBIAS
Matthew 11 in the SBIBS
Matthew 11 in the SBIBS2
Matthew 11 in the SBICS
Matthew 11 in the SBIDS
Matthew 11 in the SBIGS
Matthew 11 in the SBIHS
Matthew 11 in the SBIIS
Matthew 11 in the SBIIS2
Matthew 11 in the SBIIS3
Matthew 11 in the SBIKS
Matthew 11 in the SBIKS2
Matthew 11 in the SBIMS
Matthew 11 in the SBIOS
Matthew 11 in the SBIPS
Matthew 11 in the SBISS
Matthew 11 in the SBITS
Matthew 11 in the SBITS2
Matthew 11 in the SBITS3
Matthew 11 in the SBITS4
Matthew 11 in the SBIUS
Matthew 11 in the SBIVS
Matthew 11 in the SBT
Matthew 11 in the SBT1E
Matthew 11 in the SCHL
Matthew 11 in the SNT
Matthew 11 in the SUSU
Matthew 11 in the SUSU2
Matthew 11 in the SYNO
Matthew 11 in the TBIAOTANT
Matthew 11 in the TBT1E
Matthew 11 in the TBT1E2
Matthew 11 in the TFTIP
Matthew 11 in the TFTU
Matthew 11 in the TGNTATF3T
Matthew 11 in the THAI
Matthew 11 in the TNFD
Matthew 11 in the TNT
Matthew 11 in the TNTIK
Matthew 11 in the TNTIL
Matthew 11 in the TNTIN
Matthew 11 in the TNTIP
Matthew 11 in the TNTIZ
Matthew 11 in the TOMA
Matthew 11 in the TTENT
Matthew 11 in the UBG
Matthew 11 in the UGV
Matthew 11 in the UGV2
Matthew 11 in the UGV3
Matthew 11 in the VBL
Matthew 11 in the VDCC
Matthew 11 in the YALU
Matthew 11 in the YAPE
Matthew 11 in the YBVTP
Matthew 11 in the ZBP