Matthew 6 (BOGWICC)

1 “Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba. 2 “Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. 3 Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, 4 kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho. 5 “Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 6 Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho. 7 Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu. 8 Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe. 9 “Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe, 10 Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba. 11 Mutipatse chakudya chathu chalero. 12 Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu. 13 Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’ 14 Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani. 15 Koma ngati inu simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu. 16 “Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 17 Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, 18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho. 19 “Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. 20 Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. 21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko. 22 “Diso ndi nyale ya thupi. Ngati maso ako ali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mʼkuwala. 23 Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji! 24 “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi. 25 “Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? 26 Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri? 27 Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake? 28 “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. 29 Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa. 30 Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa! 31 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ 32 Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi. 33 Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu. 34 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.

In Other Versions

Matthew 6 in the ANGEFD

Matthew 6 in the ANTPNG2D

Matthew 6 in the AS21

Matthew 6 in the BAGH

Matthew 6 in the BBPNG

Matthew 6 in the BBT1E

Matthew 6 in the BDS

Matthew 6 in the BEV

Matthew 6 in the BHAD

Matthew 6 in the BIB

Matthew 6 in the BLPT

Matthew 6 in the BNT

Matthew 6 in the BNTABOOT

Matthew 6 in the BNTLV

Matthew 6 in the BOATCB

Matthew 6 in the BOATCB2

Matthew 6 in the BOBCV

Matthew 6 in the BOCNT

Matthew 6 in the BOECS

Matthew 6 in the BOHCB

Matthew 6 in the BOHCV

Matthew 6 in the BOHLNT

Matthew 6 in the BOHNTLTAL

Matthew 6 in the BOICB

Matthew 6 in the BOILNTAP

Matthew 6 in the BOITCV

Matthew 6 in the BOKCV

Matthew 6 in the BOKCV2

Matthew 6 in the BOKHWOG

Matthew 6 in the BOKSSV

Matthew 6 in the BOLCB

Matthew 6 in the BOLCB2

Matthew 6 in the BOMCV

Matthew 6 in the BONAV

Matthew 6 in the BONCB

Matthew 6 in the BONLT

Matthew 6 in the BONUT2

Matthew 6 in the BOPLNT

Matthew 6 in the BOSCB

Matthew 6 in the BOSNC

Matthew 6 in the BOTLNT

Matthew 6 in the BOVCB

Matthew 6 in the BOYCB

Matthew 6 in the BPBB

Matthew 6 in the BPH

Matthew 6 in the BSB

Matthew 6 in the CCB

Matthew 6 in the CUV

Matthew 6 in the CUVS

Matthew 6 in the DBT

Matthew 6 in the DGDNT

Matthew 6 in the DHNT

Matthew 6 in the DNT

Matthew 6 in the ELBE

Matthew 6 in the EMTV

Matthew 6 in the ESV

Matthew 6 in the FBV

Matthew 6 in the FEB

Matthew 6 in the GGMNT

Matthew 6 in the GNT

Matthew 6 in the HARY

Matthew 6 in the HNT

Matthew 6 in the IRVA

Matthew 6 in the IRVB

Matthew 6 in the IRVG

Matthew 6 in the IRVH

Matthew 6 in the IRVK

Matthew 6 in the IRVM

Matthew 6 in the IRVM2

Matthew 6 in the IRVO

Matthew 6 in the IRVP

Matthew 6 in the IRVT

Matthew 6 in the IRVT2

Matthew 6 in the IRVU

Matthew 6 in the ISVN

Matthew 6 in the JSNT

Matthew 6 in the KAPI

Matthew 6 in the KBT1ETNIK

Matthew 6 in the KBV

Matthew 6 in the KJV

Matthew 6 in the KNFD

Matthew 6 in the LBA

Matthew 6 in the LBLA

Matthew 6 in the LNT

Matthew 6 in the LSV

Matthew 6 in the MAAL

Matthew 6 in the MBV

Matthew 6 in the MBV2

Matthew 6 in the MHNT

Matthew 6 in the MKNFD

Matthew 6 in the MNG

Matthew 6 in the MNT

Matthew 6 in the MNT2

Matthew 6 in the MRS1T

Matthew 6 in the NAA

Matthew 6 in the NASB

Matthew 6 in the NBLA

Matthew 6 in the NBS

Matthew 6 in the NBVTP

Matthew 6 in the NET2

Matthew 6 in the NIV11

Matthew 6 in the NNT

Matthew 6 in the NNT2

Matthew 6 in the NNT3

Matthew 6 in the PDDPT

Matthew 6 in the PFNT

Matthew 6 in the RMNT

Matthew 6 in the SBIAS

Matthew 6 in the SBIBS

Matthew 6 in the SBIBS2

Matthew 6 in the SBICS

Matthew 6 in the SBIDS

Matthew 6 in the SBIGS

Matthew 6 in the SBIHS

Matthew 6 in the SBIIS

Matthew 6 in the SBIIS2

Matthew 6 in the SBIIS3

Matthew 6 in the SBIKS

Matthew 6 in the SBIKS2

Matthew 6 in the SBIMS

Matthew 6 in the SBIOS

Matthew 6 in the SBIPS

Matthew 6 in the SBISS

Matthew 6 in the SBITS

Matthew 6 in the SBITS2

Matthew 6 in the SBITS3

Matthew 6 in the SBITS4

Matthew 6 in the SBIUS

Matthew 6 in the SBIVS

Matthew 6 in the SBT

Matthew 6 in the SBT1E

Matthew 6 in the SCHL

Matthew 6 in the SNT

Matthew 6 in the SUSU

Matthew 6 in the SUSU2

Matthew 6 in the SYNO

Matthew 6 in the TBIAOTANT

Matthew 6 in the TBT1E

Matthew 6 in the TBT1E2

Matthew 6 in the TFTIP

Matthew 6 in the TFTU

Matthew 6 in the TGNTATF3T

Matthew 6 in the THAI

Matthew 6 in the TNFD

Matthew 6 in the TNT

Matthew 6 in the TNTIK

Matthew 6 in the TNTIL

Matthew 6 in the TNTIN

Matthew 6 in the TNTIP

Matthew 6 in the TNTIZ

Matthew 6 in the TOMA

Matthew 6 in the TTENT

Matthew 6 in the UBG

Matthew 6 in the UGV

Matthew 6 in the UGV2

Matthew 6 in the UGV3

Matthew 6 in the VBL

Matthew 6 in the VDCC

Matthew 6 in the YALU

Matthew 6 in the YAPE

Matthew 6 in the YBVTP

Matthew 6 in the ZBP