Matthew 9 (BOGWICC)

1 Yesu analowa mʼbwato nawoloka, ndipo anabwera ku mudzi wa kwawo. 2 Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, “Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.” 3 Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.” 4 Ndipo podziwa maganizo awo Yesu anati, “Bwanji mukuganiza zoyipa mʼmitima mwanu? 5 Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’ 6 Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ ” 7 Ndipo munthuyo anayimirira napita kwawo. 8 Gulu la anthu litaona izi, linadzazidwa ndi mantha ndipo linalemekeza Mulungu amene anapereka ulamuliro kwa anthu. 9 Ndipo Yesu atachoka kumeneko, anaona munthu wina dzina lake Mateyu, atakhala mʼnyumba ya msonkho. Anati kwa iye, “Nditsate Ine.” Ndipo iye ananyamuka namutsata. 10 Ndipo pamene Iye ankadya mʼnyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anabwera nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11 Ndipo Afarisi poona izi, anati kwa ophunzira ake, “Nʼchifukwa chiyani Aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?” 12 Yesu atamva, anati, “Munthu wamoyo safuna singʼanga ayi, koma wodwala. 13 Koma pitani kaphunzireni tanthauzo la mawu awa: ‘Ndimafuna chifundo osati nsembe ayi.’ Pakuti sindinabwere kudzayitana olungama koma ochimwa.” 14 Ndipo ophunzira a Yohane anabwera namufunsa Iye kuti, “Bwanji ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?” 15 Yesu anayankha kuti, “Kodi oyitanidwa ku ukwati angamalire bwanji pamene mkwati ali naye pamodzi? Nthawi idzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa ndi pamene adzasala kudya.” 16 Ndipo palibe munthu amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale chifukwa chigambacho chidzachoka ndipo chibowocho chidzakula kuposa kale. 17 Kapena sathira vinyo watsopano mʼmatumba akale; akatero, matumba akalewo adzaphulika ndipo vinyoyo adzatayika, matumbawo adzawonongeka; satero ayi. Amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso ndipo zonse zimasungika. 18 Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo.” 19 Yesu ndi ophunzira ake ananyamuka napita naye pamodzi. 20 Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake. 21 Iyeyo anati mwa iye yekha, “Nditangokhudza kasonga ka mkanjo wake, ine ndidzachiritsidwa.” 22 Ndipo Yesu anatembenuka namuona mayiyo nati, “Limbani mtima mayi iwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthawi yomweyo mayiyo anachiritsidwa. 23 Yesu atalowa mʼnyumba ya mkulu wa sunagoge ndi kuona oyimba zitoliro ndi gulu la anthu ochita phokoso, 24 anati, “Tulukani, mtsikanayu sanafe koma ali mtulo.” Koma anamuseka Iye. 25 Atangowatulutsa anthuwo, analowa mʼnyumba ndipo anagwira dzanja la mtsikanayo ndipo anauka. 26 Mbiriyi inamveka mʼdera lonse. 27 Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!” 28 Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?”Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.” 29 Pomwepo anakhudza maso awo nati, “Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.” 30 Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, “Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi.” 31 Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse. 32 Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula. 33 Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, “Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli.” 34 Koma Afarisi anati, “Akutulutsa mizimu yoyipa ndi mphamvu ya mkulu wa ziwanda.” 35 Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo. 36 Ataona maguluwo, anagwidwa ndi chisoni chifukwa anali ozunzika ndi osowa chithandizo ngati nkhosa zopanda mʼbusa. 37 Pamenepo anati kwa ophunzira ake, “Zokolola ndi zambiri koma antchito ndi ochepa. 38 Nʼchifukwa chake, pemphani Ambuye mwini zokolola kuti atumize antchito ku munda wake.”

In Other Versions

Matthew 9 in the ANGEFD

Matthew 9 in the ANTPNG2D

Matthew 9 in the AS21

Matthew 9 in the BAGH

Matthew 9 in the BBPNG

Matthew 9 in the BBT1E

Matthew 9 in the BDS

Matthew 9 in the BEV

Matthew 9 in the BHAD

Matthew 9 in the BIB

Matthew 9 in the BLPT

Matthew 9 in the BNT

Matthew 9 in the BNTABOOT

Matthew 9 in the BNTLV

Matthew 9 in the BOATCB

Matthew 9 in the BOATCB2

Matthew 9 in the BOBCV

Matthew 9 in the BOCNT

Matthew 9 in the BOECS

Matthew 9 in the BOHCB

Matthew 9 in the BOHCV

Matthew 9 in the BOHLNT

Matthew 9 in the BOHNTLTAL

Matthew 9 in the BOICB

Matthew 9 in the BOILNTAP

Matthew 9 in the BOITCV

Matthew 9 in the BOKCV

Matthew 9 in the BOKCV2

Matthew 9 in the BOKHWOG

Matthew 9 in the BOKSSV

Matthew 9 in the BOLCB

Matthew 9 in the BOLCB2

Matthew 9 in the BOMCV

Matthew 9 in the BONAV

Matthew 9 in the BONCB

Matthew 9 in the BONLT

Matthew 9 in the BONUT2

Matthew 9 in the BOPLNT

Matthew 9 in the BOSCB

Matthew 9 in the BOSNC

Matthew 9 in the BOTLNT

Matthew 9 in the BOVCB

Matthew 9 in the BOYCB

Matthew 9 in the BPBB

Matthew 9 in the BPH

Matthew 9 in the BSB

Matthew 9 in the CCB

Matthew 9 in the CUV

Matthew 9 in the CUVS

Matthew 9 in the DBT

Matthew 9 in the DGDNT

Matthew 9 in the DHNT

Matthew 9 in the DNT

Matthew 9 in the ELBE

Matthew 9 in the EMTV

Matthew 9 in the ESV

Matthew 9 in the FBV

Matthew 9 in the FEB

Matthew 9 in the GGMNT

Matthew 9 in the GNT

Matthew 9 in the HARY

Matthew 9 in the HNT

Matthew 9 in the IRVA

Matthew 9 in the IRVB

Matthew 9 in the IRVG

Matthew 9 in the IRVH

Matthew 9 in the IRVK

Matthew 9 in the IRVM

Matthew 9 in the IRVM2

Matthew 9 in the IRVO

Matthew 9 in the IRVP

Matthew 9 in the IRVT

Matthew 9 in the IRVT2

Matthew 9 in the IRVU

Matthew 9 in the ISVN

Matthew 9 in the JSNT

Matthew 9 in the KAPI

Matthew 9 in the KBT1ETNIK

Matthew 9 in the KBV

Matthew 9 in the KJV

Matthew 9 in the KNFD

Matthew 9 in the LBA

Matthew 9 in the LBLA

Matthew 9 in the LNT

Matthew 9 in the LSV

Matthew 9 in the MAAL

Matthew 9 in the MBV

Matthew 9 in the MBV2

Matthew 9 in the MHNT

Matthew 9 in the MKNFD

Matthew 9 in the MNG

Matthew 9 in the MNT

Matthew 9 in the MNT2

Matthew 9 in the MRS1T

Matthew 9 in the NAA

Matthew 9 in the NASB

Matthew 9 in the NBLA

Matthew 9 in the NBS

Matthew 9 in the NBVTP

Matthew 9 in the NET2

Matthew 9 in the NIV11

Matthew 9 in the NNT

Matthew 9 in the NNT2

Matthew 9 in the NNT3

Matthew 9 in the PDDPT

Matthew 9 in the PFNT

Matthew 9 in the RMNT

Matthew 9 in the SBIAS

Matthew 9 in the SBIBS

Matthew 9 in the SBIBS2

Matthew 9 in the SBICS

Matthew 9 in the SBIDS

Matthew 9 in the SBIGS

Matthew 9 in the SBIHS

Matthew 9 in the SBIIS

Matthew 9 in the SBIIS2

Matthew 9 in the SBIIS3

Matthew 9 in the SBIKS

Matthew 9 in the SBIKS2

Matthew 9 in the SBIMS

Matthew 9 in the SBIOS

Matthew 9 in the SBIPS

Matthew 9 in the SBISS

Matthew 9 in the SBITS

Matthew 9 in the SBITS2

Matthew 9 in the SBITS3

Matthew 9 in the SBITS4

Matthew 9 in the SBIUS

Matthew 9 in the SBIVS

Matthew 9 in the SBT

Matthew 9 in the SBT1E

Matthew 9 in the SCHL

Matthew 9 in the SNT

Matthew 9 in the SUSU

Matthew 9 in the SUSU2

Matthew 9 in the SYNO

Matthew 9 in the TBIAOTANT

Matthew 9 in the TBT1E

Matthew 9 in the TBT1E2

Matthew 9 in the TFTIP

Matthew 9 in the TFTU

Matthew 9 in the TGNTATF3T

Matthew 9 in the THAI

Matthew 9 in the TNFD

Matthew 9 in the TNT

Matthew 9 in the TNTIK

Matthew 9 in the TNTIL

Matthew 9 in the TNTIN

Matthew 9 in the TNTIP

Matthew 9 in the TNTIZ

Matthew 9 in the TOMA

Matthew 9 in the TTENT

Matthew 9 in the UBG

Matthew 9 in the UGV

Matthew 9 in the UGV2

Matthew 9 in the UGV3

Matthew 9 in the VBL

Matthew 9 in the VDCC

Matthew 9 in the YALU

Matthew 9 in the YAPE

Matthew 9 in the YBVTP

Matthew 9 in the ZBP