Mark 14 (BOGWICC)

1 Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha. 2 Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.” 3 Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu. 4 Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? 5 Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali. 6 Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 7 Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 8 Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 9 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.” 10 Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu. 11 Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke. 12 Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?” 13 Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye. 14 Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’ 15 Iye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.” 16 Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska. 17 Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo. 18 Pamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.” 19 Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?” 20 Iye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine. 21 Mwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.” 22 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.” 23 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo. 24 Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri. 25 Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.” 26 Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi. 27 Yesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “ ‘Kantha Mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’ 28 Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.” 29 Petro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.” 30 Yesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.” 31 Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi. 32 Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.” 33 Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima. 34 Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.” 35 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire. 36 Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.” 37 Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi? 38 Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.” 39 Kenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi. 40 Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye. 41 Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. 42 Nyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!” 43 Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu. 44 Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.” 45 Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona. 46 Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga. 47 Kenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake. 48 Yesu anati, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira, kuti mubwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? 49 Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.” 50 Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha. 51 Mnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira, 52 anathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo. 53 Anamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi. 54 Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto. 55 Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse. 56 Ambiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane. 57 Kenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti, 58 “Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ” 59 Ngakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane. 60 Kenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?” 61 Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe.Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?” 62 Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.” 63 Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso? 64 Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?”Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa. 65 Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya. 66 Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera. 67 Ataona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa.Iye anati, “Iwenso unali pamodzi ndi Mnazareti, Yesu.” 68 Koma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata. 69 Pamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.” 70 Anakananso kachiwiri.Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.” 71 Iye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.” 72 Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.

In Other Versions

Mark 14 in the ANGEFD

Mark 14 in the ANTPNG2D

Mark 14 in the AS21

Mark 14 in the BAGH

Mark 14 in the BBPNG

Mark 14 in the BBT1E

Mark 14 in the BDS

Mark 14 in the BEV

Mark 14 in the BHAD

Mark 14 in the BIB

Mark 14 in the BLPT

Mark 14 in the BNT

Mark 14 in the BNTABOOT

Mark 14 in the BNTLV

Mark 14 in the BOATCB

Mark 14 in the BOATCB2

Mark 14 in the BOBCV

Mark 14 in the BOCNT

Mark 14 in the BOECS

Mark 14 in the BOHCB

Mark 14 in the BOHCV

Mark 14 in the BOHLNT

Mark 14 in the BOHNTLTAL

Mark 14 in the BOICB

Mark 14 in the BOILNTAP

Mark 14 in the BOITCV

Mark 14 in the BOKCV

Mark 14 in the BOKCV2

Mark 14 in the BOKHWOG

Mark 14 in the BOKSSV

Mark 14 in the BOLCB

Mark 14 in the BOLCB2

Mark 14 in the BOMCV

Mark 14 in the BONAV

Mark 14 in the BONCB

Mark 14 in the BONLT

Mark 14 in the BONUT2

Mark 14 in the BOPLNT

Mark 14 in the BOSCB

Mark 14 in the BOSNC

Mark 14 in the BOTLNT

Mark 14 in the BOVCB

Mark 14 in the BOYCB

Mark 14 in the BPBB

Mark 14 in the BPH

Mark 14 in the BSB

Mark 14 in the CCB

Mark 14 in the CUV

Mark 14 in the CUVS

Mark 14 in the DBT

Mark 14 in the DGDNT

Mark 14 in the DHNT

Mark 14 in the DNT

Mark 14 in the ELBE

Mark 14 in the EMTV

Mark 14 in the ESV

Mark 14 in the FBV

Mark 14 in the FEB

Mark 14 in the GGMNT

Mark 14 in the GNT

Mark 14 in the HARY

Mark 14 in the HNT

Mark 14 in the IRVA

Mark 14 in the IRVB

Mark 14 in the IRVG

Mark 14 in the IRVH

Mark 14 in the IRVK

Mark 14 in the IRVM

Mark 14 in the IRVM2

Mark 14 in the IRVO

Mark 14 in the IRVP

Mark 14 in the IRVT

Mark 14 in the IRVT2

Mark 14 in the IRVU

Mark 14 in the ISVN

Mark 14 in the JSNT

Mark 14 in the KAPI

Mark 14 in the KBT1ETNIK

Mark 14 in the KBV

Mark 14 in the KJV

Mark 14 in the KNFD

Mark 14 in the LBA

Mark 14 in the LBLA

Mark 14 in the LNT

Mark 14 in the LSV

Mark 14 in the MAAL

Mark 14 in the MBV

Mark 14 in the MBV2

Mark 14 in the MHNT

Mark 14 in the MKNFD

Mark 14 in the MNG

Mark 14 in the MNT

Mark 14 in the MNT2

Mark 14 in the MRS1T

Mark 14 in the NAA

Mark 14 in the NASB

Mark 14 in the NBLA

Mark 14 in the NBS

Mark 14 in the NBVTP

Mark 14 in the NET2

Mark 14 in the NIV11

Mark 14 in the NNT

Mark 14 in the NNT2

Mark 14 in the NNT3

Mark 14 in the PDDPT

Mark 14 in the PFNT

Mark 14 in the RMNT

Mark 14 in the SBIAS

Mark 14 in the SBIBS

Mark 14 in the SBIBS2

Mark 14 in the SBICS

Mark 14 in the SBIDS

Mark 14 in the SBIGS

Mark 14 in the SBIHS

Mark 14 in the SBIIS

Mark 14 in the SBIIS2

Mark 14 in the SBIIS3

Mark 14 in the SBIKS

Mark 14 in the SBIKS2

Mark 14 in the SBIMS

Mark 14 in the SBIOS

Mark 14 in the SBIPS

Mark 14 in the SBISS

Mark 14 in the SBITS

Mark 14 in the SBITS2

Mark 14 in the SBITS3

Mark 14 in the SBITS4

Mark 14 in the SBIUS

Mark 14 in the SBIVS

Mark 14 in the SBT

Mark 14 in the SBT1E

Mark 14 in the SCHL

Mark 14 in the SNT

Mark 14 in the SUSU

Mark 14 in the SUSU2

Mark 14 in the SYNO

Mark 14 in the TBIAOTANT

Mark 14 in the TBT1E

Mark 14 in the TBT1E2

Mark 14 in the TFTIP

Mark 14 in the TFTU

Mark 14 in the TGNTATF3T

Mark 14 in the THAI

Mark 14 in the TNFD

Mark 14 in the TNT

Mark 14 in the TNTIK

Mark 14 in the TNTIL

Mark 14 in the TNTIN

Mark 14 in the TNTIP

Mark 14 in the TNTIZ

Mark 14 in the TOMA

Mark 14 in the TTENT

Mark 14 in the UBG

Mark 14 in the UGV

Mark 14 in the UGV2

Mark 14 in the UGV3

Mark 14 in the VBL

Mark 14 in the VDCC

Mark 14 in the YALU

Mark 14 in the YAPE

Mark 14 in the YBVTP

Mark 14 in the ZBP