Mark 2 (BOGWICC)

1 Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba. 2 Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu. 3 Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. 4 Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. 5 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo, “Mwana, machimo ako akhululukidwa.” 6 Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, 7 “Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?” 8 Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi? 9 Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ 10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo.” Anati kwa wofa ziwaloyo, 11 “Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu.” 12 Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!” 13 Yesu anatulukanso napita kumbali ya nyanja. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuliphunzitsa. 14 Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye. 15 Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira. 16 Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?” 17 Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti, “Anthu amene ali bwino safuna singʼanga koma odwala. Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa.” 18 Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?” 19 Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi. 20 Koma nthawi idzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya. 21 “Palibe amene amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale. Ngati atatero, chigamba chatsopanocho chidzazomola chovala chakalecho, kukulitsa chibowocho. 22 Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.” 23 Tsiku lina la Sabata, Yesu amadutsa pakati pa minda ya tirigu, ndipo ophunzira ake amayenda naye limodzi, nayamba kubudula ngala za tiriguyo. 24 Afarisi anati kwa Iye, “Taonani, chifukwa chiyani akuchita chosaloledwa ndi lamulo pa Sabata?” 25 Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali osowa ndi anamva njala? 26 Pa nthawi ya Abiatara mkulu wa ansembe, iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndi kudya buledi wopatulika amene amaloledwa kuti adye ndi ansembe okha. Ndipo anapereka wina kwa anzake.” 27 Pamenepo anawawuza kuti, “Sabata linapangidwira munthu, osati munthu kupangidwira Sabata. 28 Choncho Mwana wa Munthu ali Ambuye ngakhale wa Sabata.”

In Other Versions

Mark 2 in the ANGEFD

Mark 2 in the ANTPNG2D

Mark 2 in the AS21

Mark 2 in the BAGH

Mark 2 in the BBPNG

Mark 2 in the BBT1E

Mark 2 in the BDS

Mark 2 in the BEV

Mark 2 in the BHAD

Mark 2 in the BIB

Mark 2 in the BLPT

Mark 2 in the BNT

Mark 2 in the BNTABOOT

Mark 2 in the BNTLV

Mark 2 in the BOATCB

Mark 2 in the BOATCB2

Mark 2 in the BOBCV

Mark 2 in the BOCNT

Mark 2 in the BOECS

Mark 2 in the BOHCB

Mark 2 in the BOHCV

Mark 2 in the BOHLNT

Mark 2 in the BOHNTLTAL

Mark 2 in the BOICB

Mark 2 in the BOILNTAP

Mark 2 in the BOITCV

Mark 2 in the BOKCV

Mark 2 in the BOKCV2

Mark 2 in the BOKHWOG

Mark 2 in the BOKSSV

Mark 2 in the BOLCB

Mark 2 in the BOLCB2

Mark 2 in the BOMCV

Mark 2 in the BONAV

Mark 2 in the BONCB

Mark 2 in the BONLT

Mark 2 in the BONUT2

Mark 2 in the BOPLNT

Mark 2 in the BOSCB

Mark 2 in the BOSNC

Mark 2 in the BOTLNT

Mark 2 in the BOVCB

Mark 2 in the BOYCB

Mark 2 in the BPBB

Mark 2 in the BPH

Mark 2 in the BSB

Mark 2 in the CCB

Mark 2 in the CUV

Mark 2 in the CUVS

Mark 2 in the DBT

Mark 2 in the DGDNT

Mark 2 in the DHNT

Mark 2 in the DNT

Mark 2 in the ELBE

Mark 2 in the EMTV

Mark 2 in the ESV

Mark 2 in the FBV

Mark 2 in the FEB

Mark 2 in the GGMNT

Mark 2 in the GNT

Mark 2 in the HARY

Mark 2 in the HNT

Mark 2 in the IRVA

Mark 2 in the IRVB

Mark 2 in the IRVG

Mark 2 in the IRVH

Mark 2 in the IRVK

Mark 2 in the IRVM

Mark 2 in the IRVM2

Mark 2 in the IRVO

Mark 2 in the IRVP

Mark 2 in the IRVT

Mark 2 in the IRVT2

Mark 2 in the IRVU

Mark 2 in the ISVN

Mark 2 in the JSNT

Mark 2 in the KAPI

Mark 2 in the KBT1ETNIK

Mark 2 in the KBV

Mark 2 in the KJV

Mark 2 in the KNFD

Mark 2 in the LBA

Mark 2 in the LBLA

Mark 2 in the LNT

Mark 2 in the LSV

Mark 2 in the MAAL

Mark 2 in the MBV

Mark 2 in the MBV2

Mark 2 in the MHNT

Mark 2 in the MKNFD

Mark 2 in the MNG

Mark 2 in the MNT

Mark 2 in the MNT2

Mark 2 in the MRS1T

Mark 2 in the NAA

Mark 2 in the NASB

Mark 2 in the NBLA

Mark 2 in the NBS

Mark 2 in the NBVTP

Mark 2 in the NET2

Mark 2 in the NIV11

Mark 2 in the NNT

Mark 2 in the NNT2

Mark 2 in the NNT3

Mark 2 in the PDDPT

Mark 2 in the PFNT

Mark 2 in the RMNT

Mark 2 in the SBIAS

Mark 2 in the SBIBS

Mark 2 in the SBIBS2

Mark 2 in the SBICS

Mark 2 in the SBIDS

Mark 2 in the SBIGS

Mark 2 in the SBIHS

Mark 2 in the SBIIS

Mark 2 in the SBIIS2

Mark 2 in the SBIIS3

Mark 2 in the SBIKS

Mark 2 in the SBIKS2

Mark 2 in the SBIMS

Mark 2 in the SBIOS

Mark 2 in the SBIPS

Mark 2 in the SBISS

Mark 2 in the SBITS

Mark 2 in the SBITS2

Mark 2 in the SBITS3

Mark 2 in the SBITS4

Mark 2 in the SBIUS

Mark 2 in the SBIVS

Mark 2 in the SBT

Mark 2 in the SBT1E

Mark 2 in the SCHL

Mark 2 in the SNT

Mark 2 in the SUSU

Mark 2 in the SUSU2

Mark 2 in the SYNO

Mark 2 in the TBIAOTANT

Mark 2 in the TBT1E

Mark 2 in the TBT1E2

Mark 2 in the TFTIP

Mark 2 in the TFTU

Mark 2 in the TGNTATF3T

Mark 2 in the THAI

Mark 2 in the TNFD

Mark 2 in the TNT

Mark 2 in the TNTIK

Mark 2 in the TNTIL

Mark 2 in the TNTIN

Mark 2 in the TNTIP

Mark 2 in the TNTIZ

Mark 2 in the TOMA

Mark 2 in the TTENT

Mark 2 in the UBG

Mark 2 in the UGV

Mark 2 in the UGV2

Mark 2 in the UGV3

Mark 2 in the VBL

Mark 2 in the VDCC

Mark 2 in the YALU

Mark 2 in the YAPE

Mark 2 in the YBVTP

Mark 2 in the ZBP