Nehemiah 8 (BOGWICC)

1 Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli. 2 Choncho pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wansembe Ezara, anabwera ndi buku la malamulo ku msonkhano wa amuna, akazi ndi ana onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. 3 Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo. 4 Mlembi Ezara anayimirira pa nsanja ya mitengo imene anthu anamanga chifukwa cha msonkhanowu. Ku dzanja lake lamanja kunayimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya, ndipo kudzanja lake lamanzere kunali Pedaya, Misaeli, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndi Mesulamu. 5 Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira. 6 Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho. 7 Anthuwo atayimiriranso Alevi awa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetayi, Hodiya, Maaseya, Kerita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndi Pelaya anawathandiza kuti amvetse bwino malamulowo. 8 Iwo anawerenga buku la malamulo a Mulungu momveka bwino ndi kutanthauzira mawuwo kuti anthu amvetse bwino zowerengedwazo. 9 Tsono bwanamkubwa Nehemiya pamodzi ndi wansembe ndi mlembi Ezara komanso Alevi amene amaphunzitsa anthu anati kwa anthu onse, “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Anayankhula choncho popeza anthu onse ankalira atamva mawu a buku la malamulo lija. 10 Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.” 11 Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.” 12 Anthu onse anachoka kupita kukadya ndi kumwa. Chakudya china anatumiza kwa anzawo. Choncho panali chikondwerero chachikulu popeza tsopano anali atamvetsa bwino mawu a Mulungu amene anawawerengera ndi kuwafotokozerawo. 13 Mmawa mwake atsogoleri a mabanja pamodzi ndi ansembe ndi alevi anasonkhana kwa Ezara, mlembi wa malamulo kuti aphunzire mawu a malamulowo. 14 Tsono anapeza kuti zinalembedwa mʼbuku la malamulo kuti Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti Aisraeli azikhala mʼzithando pa nthawi yonse ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri. 15 Choncho analengeza ndi kufalitsa mʼmizinda yawo yonse ndi mu Yerusalemu kuti, “Pitani ku phiri mukadule nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wa kutchire, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa ndiponso za mitengo ina ya masamba, zomangira zithando monga zalembedweramu ndi kubwera nazo.” 16 Choncho anthu anapita kukatenga nthambi ndipo aliyense anadzimangira misasa pa denga ya nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, mʼbwalo la pa Chipata cha Madzi ndiponso mʼbwalo la pa Chipata cha Efereimu. 17 Gulu lonse la anthu limene linabwera ku ukapolo linamanga misasa ndipo linakhala mʼmenemo. Kuyambira nthawi ya Yoswa mwana wa Nuni mpaka tsiku limenelo nʼkuti Aisraeli asanachitepo zimenezi. Choncho panali chimwemwe chachikulu. 18 Tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, Ezara ankawerenga buku la malamulo a Mulungu. Anthu anachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panachitika msonkhano potsata buku la malamulo lija.

In Other Versions

Nehemiah 8 in the ANGEFD

Nehemiah 8 in the ANTPNG2D

Nehemiah 8 in the AS21

Nehemiah 8 in the BAGH

Nehemiah 8 in the BBPNG

Nehemiah 8 in the BBT1E

Nehemiah 8 in the BDS

Nehemiah 8 in the BEV

Nehemiah 8 in the BHAD

Nehemiah 8 in the BIB

Nehemiah 8 in the BLPT

Nehemiah 8 in the BNT

Nehemiah 8 in the BNTABOOT

Nehemiah 8 in the BNTLV

Nehemiah 8 in the BOATCB

Nehemiah 8 in the BOATCB2

Nehemiah 8 in the BOBCV

Nehemiah 8 in the BOCNT

Nehemiah 8 in the BOECS

Nehemiah 8 in the BOHCB

Nehemiah 8 in the BOHCV

Nehemiah 8 in the BOHLNT

Nehemiah 8 in the BOHNTLTAL

Nehemiah 8 in the BOICB

Nehemiah 8 in the BOILNTAP

Nehemiah 8 in the BOITCV

Nehemiah 8 in the BOKCV

Nehemiah 8 in the BOKCV2

Nehemiah 8 in the BOKHWOG

Nehemiah 8 in the BOKSSV

Nehemiah 8 in the BOLCB

Nehemiah 8 in the BOLCB2

Nehemiah 8 in the BOMCV

Nehemiah 8 in the BONAV

Nehemiah 8 in the BONCB

Nehemiah 8 in the BONLT

Nehemiah 8 in the BONUT2

Nehemiah 8 in the BOPLNT

Nehemiah 8 in the BOSCB

Nehemiah 8 in the BOSNC

Nehemiah 8 in the BOTLNT

Nehemiah 8 in the BOVCB

Nehemiah 8 in the BOYCB

Nehemiah 8 in the BPBB

Nehemiah 8 in the BPH

Nehemiah 8 in the BSB

Nehemiah 8 in the CCB

Nehemiah 8 in the CUV

Nehemiah 8 in the CUVS

Nehemiah 8 in the DBT

Nehemiah 8 in the DGDNT

Nehemiah 8 in the DHNT

Nehemiah 8 in the DNT

Nehemiah 8 in the ELBE

Nehemiah 8 in the EMTV

Nehemiah 8 in the ESV

Nehemiah 8 in the FBV

Nehemiah 8 in the FEB

Nehemiah 8 in the GGMNT

Nehemiah 8 in the GNT

Nehemiah 8 in the HARY

Nehemiah 8 in the HNT

Nehemiah 8 in the IRVA

Nehemiah 8 in the IRVB

Nehemiah 8 in the IRVG

Nehemiah 8 in the IRVH

Nehemiah 8 in the IRVK

Nehemiah 8 in the IRVM

Nehemiah 8 in the IRVM2

Nehemiah 8 in the IRVO

Nehemiah 8 in the IRVP

Nehemiah 8 in the IRVT

Nehemiah 8 in the IRVT2

Nehemiah 8 in the IRVU

Nehemiah 8 in the ISVN

Nehemiah 8 in the JSNT

Nehemiah 8 in the KAPI

Nehemiah 8 in the KBT1ETNIK

Nehemiah 8 in the KBV

Nehemiah 8 in the KJV

Nehemiah 8 in the KNFD

Nehemiah 8 in the LBA

Nehemiah 8 in the LBLA

Nehemiah 8 in the LNT

Nehemiah 8 in the LSV

Nehemiah 8 in the MAAL

Nehemiah 8 in the MBV

Nehemiah 8 in the MBV2

Nehemiah 8 in the MHNT

Nehemiah 8 in the MKNFD

Nehemiah 8 in the MNG

Nehemiah 8 in the MNT

Nehemiah 8 in the MNT2

Nehemiah 8 in the MRS1T

Nehemiah 8 in the NAA

Nehemiah 8 in the NASB

Nehemiah 8 in the NBLA

Nehemiah 8 in the NBS

Nehemiah 8 in the NBVTP

Nehemiah 8 in the NET2

Nehemiah 8 in the NIV11

Nehemiah 8 in the NNT

Nehemiah 8 in the NNT2

Nehemiah 8 in the NNT3

Nehemiah 8 in the PDDPT

Nehemiah 8 in the PFNT

Nehemiah 8 in the RMNT

Nehemiah 8 in the SBIAS

Nehemiah 8 in the SBIBS

Nehemiah 8 in the SBIBS2

Nehemiah 8 in the SBICS

Nehemiah 8 in the SBIDS

Nehemiah 8 in the SBIGS

Nehemiah 8 in the SBIHS

Nehemiah 8 in the SBIIS

Nehemiah 8 in the SBIIS2

Nehemiah 8 in the SBIIS3

Nehemiah 8 in the SBIKS

Nehemiah 8 in the SBIKS2

Nehemiah 8 in the SBIMS

Nehemiah 8 in the SBIOS

Nehemiah 8 in the SBIPS

Nehemiah 8 in the SBISS

Nehemiah 8 in the SBITS

Nehemiah 8 in the SBITS2

Nehemiah 8 in the SBITS3

Nehemiah 8 in the SBITS4

Nehemiah 8 in the SBIUS

Nehemiah 8 in the SBIVS

Nehemiah 8 in the SBT

Nehemiah 8 in the SBT1E

Nehemiah 8 in the SCHL

Nehemiah 8 in the SNT

Nehemiah 8 in the SUSU

Nehemiah 8 in the SUSU2

Nehemiah 8 in the SYNO

Nehemiah 8 in the TBIAOTANT

Nehemiah 8 in the TBT1E

Nehemiah 8 in the TBT1E2

Nehemiah 8 in the TFTIP

Nehemiah 8 in the TFTU

Nehemiah 8 in the TGNTATF3T

Nehemiah 8 in the THAI

Nehemiah 8 in the TNFD

Nehemiah 8 in the TNT

Nehemiah 8 in the TNTIK

Nehemiah 8 in the TNTIL

Nehemiah 8 in the TNTIN

Nehemiah 8 in the TNTIP

Nehemiah 8 in the TNTIZ

Nehemiah 8 in the TOMA

Nehemiah 8 in the TTENT

Nehemiah 8 in the UBG

Nehemiah 8 in the UGV

Nehemiah 8 in the UGV2

Nehemiah 8 in the UGV3

Nehemiah 8 in the VBL

Nehemiah 8 in the VDCC

Nehemiah 8 in the YALU

Nehemiah 8 in the YAPE

Nehemiah 8 in the YBVTP

Nehemiah 8 in the ZBP