Nehemiah 9 (BOGWICC)
1 Pa tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraeli anasonkhana pamodzi ndi kusala chakudya, kuvala ziguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. 2 Aisraeliwa anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anayimirira nayamba kuwulula machimo awo ndi zolakwa za makolo awo. 3 Anthuwo anayimirira pomwepo, ndipo anamva mawu a mʼbuku la malamulo a Yehova akuwerengedwa kwa maora enanso atatu ndipo anakhala maora ena atatu akuwulula machimo awo ndi kupembedza Yehova Mulungu wawo. 4 Pa makwerero okhalapo alevi anayimirirapo anthu awa: Yesuwa, Bani, Kadimieli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Iwowa ankapemphera mokweza mawu kwa Yehova Mulungu wawo. 5 Ndipo Alevi awa: Yesuwa, Kadimieli, Bani, Hasabaneya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu, amene ndi wamuyaya.”“Litamandike dzina lake laulemerero limene liposa madalitso ndi matamando onse. 6 Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani. 7 “Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumutulutsa mʼdziko la Uri wa ku Kaldeya ndi kumutcha dzina lake Abrahamu. 8 Inu munaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa inu, ndipo munapangana naye pangano lakuti mudzapereka kwa zidzukulu zake dziko la Akanaani Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Inu mwasunga lonjezo lanu chifukwa ndinu wolungama. 9 “Munaona kuzunzika kwa makolo athu ku Igupto. Munamva kufuwula kwawo pa Nyanja Yofiira. 10 Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa kutsutsana ndi Farao, pamaso pa Farao, nduna zake ndi anthu onse a mʼdziko lake, pakuti Inu munadziwa kuti anazunza makolo athu. Inu munadzipangira nokha dzina, monga zilili mpaka lero lino. 11 Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama. 12 Masana munkawunikira ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawunikira ndi chipilala cha moto njira yonse imene ankayendamo. 13 “Munatsika pa Phiri la Sinai, ndipo munawayankhula kuchokera kumwamba. Munawapatsa malangizo olungama, ziphunzitso zoona ndiponso malamulo abwino. 14 Inu munawadziwitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi loyera ndipo munawapatsa malamulo ndi ziphunzitso. 15 Pamene anali ndi njala munawapatsa buledi wochokera kumwamba. Pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe. Munawawuza kuti apite kukalanda dziko limene munalonjeza kuti mudzawapatsa.” 16 “Koma makolo athu anadzikuza ndi kuwumitsa khosi, ndipo iwo sanamvere malamulo anu. 17 Anakana kumvera ndipo sanakumbukire zodabwitsa zimene munachita pakati pawo. Koma iwo anawumitsa khosi, nakuwukirani podzisankhira okha mtsogoleri kuti awatsogolere kubwerera ku ukapolo ku dziko la Igupto. Koma ndinu Mulungu wokhululukira, wokoma mtima ndi wachifundo wosapsa mtima msanga ndi wachikondi chachikulu chosasinthika. Choncho Inu simunawasiye. 18 Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa. 19 “Koma Inu ndi chifundo chanu chachikulu, simunawasiye mʼchipululu. Chipilala cha mtambo sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo masana ndipo chipilala cha moto sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo usiku. 20 Inu munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti uwalangize. Inu simunawamane chakudya cha mana chija, ndipo munawapatsa madzi akumwa. 21 Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.” 22 “Inu munawapatsa mafumu ndi mayiko mʼmanja mwawo. Munawagawiranso mayiko achilendo akutali kwambiri. Munabwera nawo mʼdziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani kuti alowemo nʼkulitenga kukhala lawo. 23 Munachulukitsa ana awo aamuna ngati nyenyezi za mlengalenga. Ndipo munawabweretsa mʼdziko limene munawuza makolo awo kuti alilowe ndi kulitenga. 24 Choncho zidzukulu zawo zinapita ndi kukalandira dzikolo. Inu munagonjetsa pamaso pawo, Akanaani amene amakhala mʼdzikolo. Inde munapereka mʼmanja mwawo mafumu awo pamodzi ndi anthu a mʼdzikomo kuti achite nawo monga angafunire. 25 Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana. 26 “Komabe iwo anakhala osamvera ndipo anakuwukirani nafulatira malamulo anu. Anapha aneneri anu, amene anakawadandaulira kuti abwerere kwa Inu. Anachita chipongwe choopsa. 27 Pamene anazunzidwa anafuwulira kwa Inu, ndipo Inu munawamvera muli kumwambako. Ndipo mwa chifundo chanu chachikulu munkawapatsa atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo.” 28 “Koma akangokhala pa mtendere ankayambanso kuchita zoyipa pamaso panu. Choncho munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira kwa Inu, Inu munkawamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chochuluka, nthawi zonse munkawapulumutsa. 29 “Inu munkawachenjeza kuti abwerere ndi kuyamba kutsata malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula ndipo sankamvera malamulo anu. Iwo anachimwira malangizo anu amene munati ‘Amapatsa moyo kwa munthu wowamvera.’ Iwo ankakufulatirani, nawumitsa makosi awo osafuna kukumverani. 30 Munapirira nawo kwa zaka zambiri. Munkawachenjeza ndi Mzimu wanu kudzera mwa aneneri anu, koma iwo sankakumverani. Choncho munawapereka mʼmanja mwa anthu a mayiko ena. 31 Komabe mwachifundo chanu chachikulu simuwatheretu kapena kuwataya pakuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo. 32 “Nʼchifukwa chake, tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa kwambiri mumasunga pangano ndi chikondi chosasinthika. Musalole kuti mavuto onse amene atigwera ife, mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu ndi anthu ena onse kuyambira nthawi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero aoneke ochepa pamaso panu. 33 Koma Inu mwakhala wolungama pa zonse zimene zakhala zikutichitikira. Mwachita zokhulupirika, koma ife tachita zolakwa. 34 Ndipotu mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu ndi makolo athu sanatsatire mawu anu. Iwo sanalabadire za malamulo anu ngakhale mawu anu owachenjeza amene munawapatsa. 35 Ngakhale ankadzilamulira okha, nʼkumalandira zabwino zochuluka mʼdziko lalikulu ndi lachonde limene munawapatsa, koma iwo sanakutumikireni kapena kusiya ntchito zawo zoyipa. 36 “Tsono, taonani! Ife lero ndife akapolo, ndife akapolo mʼdziko limene munapereka kwa makolo athu kuti azidya zipatso zake ndi zabwino zake zonse. 37 Tsono chifukwa cha machimo athu, mafumu amene munawayika kuti azitilamulira angodzilemeretsa ndi chuma chambiri cha dzikoli. Iwo ali ndi mphamvu zolamulira matupi athu ndi ngʼombe zathu momwe afunira. Zedi, ife tili mʼmavuto aakulu.” 38 “Chifukwa cha zonsezi, ife tikuchita mgwirizano wokhazikika, pochita kulemba, ndipo atsogoleri athu, Alevi athu ndi ansembe athu asindikiza chidindo chawo pa mgwirizanowo.”