Numbers 6 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi afuna kuchita lonjezo lapadera, lonjezo lodzipatula yekha kwa Yehova ngati Mnaziri, 3 sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma. 4 Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’ 5 “ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’ 6 Pa nthawi yonse imene munthuyo wadzipatula yekha kwa Yehova asayandikire mtembo. 7 Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake. 8 Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova. 9 “Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri. 10 Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano. 11 Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake. 12 Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake. 13 “Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 14 Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano, 15 ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta. 16 “Wansembe apereke zimenezi pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe ya uchimo ndi nsembe yopsereza. 17 Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa. 18 “Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano. 19 “Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija. 20 Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo. 21 “Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.” 22 Yehova anawuza Mose kuti, 23 “Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti, 24 “ ‘Yehova akudalitsendi kukusunga; 25 Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,nakuchitira chisomo; 26 Yehova akweze nkhope yake pa iwe,nakupatse mtendere.’ ” 27 Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi.

In Other Versions

Numbers 6 in the ANGEFD

Numbers 6 in the ANTPNG2D

Numbers 6 in the AS21

Numbers 6 in the BAGH

Numbers 6 in the BBPNG

Numbers 6 in the BBT1E

Numbers 6 in the BDS

Numbers 6 in the BEV

Numbers 6 in the BHAD

Numbers 6 in the BIB

Numbers 6 in the BLPT

Numbers 6 in the BNT

Numbers 6 in the BNTABOOT

Numbers 6 in the BNTLV

Numbers 6 in the BOATCB

Numbers 6 in the BOATCB2

Numbers 6 in the BOBCV

Numbers 6 in the BOCNT

Numbers 6 in the BOECS

Numbers 6 in the BOHCB

Numbers 6 in the BOHCV

Numbers 6 in the BOHLNT

Numbers 6 in the BOHNTLTAL

Numbers 6 in the BOICB

Numbers 6 in the BOILNTAP

Numbers 6 in the BOITCV

Numbers 6 in the BOKCV

Numbers 6 in the BOKCV2

Numbers 6 in the BOKHWOG

Numbers 6 in the BOKSSV

Numbers 6 in the BOLCB

Numbers 6 in the BOLCB2

Numbers 6 in the BOMCV

Numbers 6 in the BONAV

Numbers 6 in the BONCB

Numbers 6 in the BONLT

Numbers 6 in the BONUT2

Numbers 6 in the BOPLNT

Numbers 6 in the BOSCB

Numbers 6 in the BOSNC

Numbers 6 in the BOTLNT

Numbers 6 in the BOVCB

Numbers 6 in the BOYCB

Numbers 6 in the BPBB

Numbers 6 in the BPH

Numbers 6 in the BSB

Numbers 6 in the CCB

Numbers 6 in the CUV

Numbers 6 in the CUVS

Numbers 6 in the DBT

Numbers 6 in the DGDNT

Numbers 6 in the DHNT

Numbers 6 in the DNT

Numbers 6 in the ELBE

Numbers 6 in the EMTV

Numbers 6 in the ESV

Numbers 6 in the FBV

Numbers 6 in the FEB

Numbers 6 in the GGMNT

Numbers 6 in the GNT

Numbers 6 in the HARY

Numbers 6 in the HNT

Numbers 6 in the IRVA

Numbers 6 in the IRVB

Numbers 6 in the IRVG

Numbers 6 in the IRVH

Numbers 6 in the IRVK

Numbers 6 in the IRVM

Numbers 6 in the IRVM2

Numbers 6 in the IRVO

Numbers 6 in the IRVP

Numbers 6 in the IRVT

Numbers 6 in the IRVT2

Numbers 6 in the IRVU

Numbers 6 in the ISVN

Numbers 6 in the JSNT

Numbers 6 in the KAPI

Numbers 6 in the KBT1ETNIK

Numbers 6 in the KBV

Numbers 6 in the KJV

Numbers 6 in the KNFD

Numbers 6 in the LBA

Numbers 6 in the LBLA

Numbers 6 in the LNT

Numbers 6 in the LSV

Numbers 6 in the MAAL

Numbers 6 in the MBV

Numbers 6 in the MBV2

Numbers 6 in the MHNT

Numbers 6 in the MKNFD

Numbers 6 in the MNG

Numbers 6 in the MNT

Numbers 6 in the MNT2

Numbers 6 in the MRS1T

Numbers 6 in the NAA

Numbers 6 in the NASB

Numbers 6 in the NBLA

Numbers 6 in the NBS

Numbers 6 in the NBVTP

Numbers 6 in the NET2

Numbers 6 in the NIV11

Numbers 6 in the NNT

Numbers 6 in the NNT2

Numbers 6 in the NNT3

Numbers 6 in the PDDPT

Numbers 6 in the PFNT

Numbers 6 in the RMNT

Numbers 6 in the SBIAS

Numbers 6 in the SBIBS

Numbers 6 in the SBIBS2

Numbers 6 in the SBICS

Numbers 6 in the SBIDS

Numbers 6 in the SBIGS

Numbers 6 in the SBIHS

Numbers 6 in the SBIIS

Numbers 6 in the SBIIS2

Numbers 6 in the SBIIS3

Numbers 6 in the SBIKS

Numbers 6 in the SBIKS2

Numbers 6 in the SBIMS

Numbers 6 in the SBIOS

Numbers 6 in the SBIPS

Numbers 6 in the SBISS

Numbers 6 in the SBITS

Numbers 6 in the SBITS2

Numbers 6 in the SBITS3

Numbers 6 in the SBITS4

Numbers 6 in the SBIUS

Numbers 6 in the SBIVS

Numbers 6 in the SBT

Numbers 6 in the SBT1E

Numbers 6 in the SCHL

Numbers 6 in the SNT

Numbers 6 in the SUSU

Numbers 6 in the SUSU2

Numbers 6 in the SYNO

Numbers 6 in the TBIAOTANT

Numbers 6 in the TBT1E

Numbers 6 in the TBT1E2

Numbers 6 in the TFTIP

Numbers 6 in the TFTU

Numbers 6 in the TGNTATF3T

Numbers 6 in the THAI

Numbers 6 in the TNFD

Numbers 6 in the TNT

Numbers 6 in the TNTIK

Numbers 6 in the TNTIL

Numbers 6 in the TNTIN

Numbers 6 in the TNTIP

Numbers 6 in the TNTIZ

Numbers 6 in the TOMA

Numbers 6 in the TTENT

Numbers 6 in the UBG

Numbers 6 in the UGV

Numbers 6 in the UGV2

Numbers 6 in the UGV3

Numbers 6 in the VBL

Numbers 6 in the VDCC

Numbers 6 in the YALU

Numbers 6 in the YAPE

Numbers 6 in the YBVTP

Numbers 6 in the ZBP