Philippians 2 (BOGWICC)
1 Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, 2 tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso. 3 Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. 4 Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena. 5 Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu: 6 Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu,sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa. 7 Koma anadzichepetsa kotheratunakhala ndi khalidwe ngati la kapolondi kukhala munthu ngati anthu ena onse. 8 Ndipo pokhala munthu chonchoanadzichepetsa yekhandipo anamvera mpaka imfa yake,imfa yake ya pamtanda! 9 Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse 10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko, 11 ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuyekuchitira ulemu Mulungu Atate. 12 Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera, 13 pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo. 14 Muzichita zonse mosawiringula kapena mosatsutsapo, 15 kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba 16 powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe. 17 Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse. 18 Chomwechonso, inu khalani okondwa ndi osangalala nane pamodzi. 19 Ngati Ambuye Yesu alola, ndikukhulupirira kuti ndidzamutuma Timoteyo msanga kwanuko, kuti mwina ndingadzasangalale ndikadzamva za moyo wanu. 20 Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu. 21 Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu. 22 Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake. 23 Choncho ndikuyembekezera kumutuma msanga ndikangodziwa mmene zinthu zanga ziyendere. 24 Ndipo ndikukhulupirira kuti Ambuye akalola ine mwini ndidzafikanso kwanuko posachedwapa. 25 Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga. 26 Pakuti akukulakalakani nonsenu ndipo akusauka mu mtima chifukwa munamva kuti akudwala. 27 Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke. 28 Choncho khumbo langa lofulumiza kumutumiza lakula, kuti pamene mumuonenso musangalale komanso kuti nkhawa yanga ichepe. 29 Mulandireni mwa Ambuye ndi chimwemwe chachikulu, ndipo anthu onga iyeyu muziwachitira ulemu. 30 Iyeyu anatsala pangʼono kufa chifukwa cha ntchito ya Khristu, anayika moyo pa chiswe kuti akwaniritse thandizo limene inu simukanatha.
In Other Versions
Philippians 2 in the ANGEFD
Philippians 2 in the ANTPNG2D
Philippians 2 in the AS21
Philippians 2 in the BAGH
Philippians 2 in the BBPNG
Philippians 2 in the BBT1E
Philippians 2 in the BDS
Philippians 2 in the BEV
Philippians 2 in the BHAD
Philippians 2 in the BIB
Philippians 2 in the BLPT
Philippians 2 in the BNT
Philippians 2 in the BNTABOOT
Philippians 2 in the BNTLV
Philippians 2 in the BOATCB
Philippians 2 in the BOATCB2
Philippians 2 in the BOBCV
Philippians 2 in the BOCNT
Philippians 2 in the BOECS
Philippians 2 in the BOHCB
Philippians 2 in the BOHCV
Philippians 2 in the BOHLNT
Philippians 2 in the BOHNTLTAL
Philippians 2 in the BOICB
Philippians 2 in the BOILNTAP
Philippians 2 in the BOITCV
Philippians 2 in the BOKCV
Philippians 2 in the BOKCV2
Philippians 2 in the BOKHWOG
Philippians 2 in the BOKSSV
Philippians 2 in the BOLCB
Philippians 2 in the BOLCB2
Philippians 2 in the BOMCV
Philippians 2 in the BONAV
Philippians 2 in the BONCB
Philippians 2 in the BONLT
Philippians 2 in the BONUT2
Philippians 2 in the BOPLNT
Philippians 2 in the BOSCB
Philippians 2 in the BOSNC
Philippians 2 in the BOTLNT
Philippians 2 in the BOVCB
Philippians 2 in the BOYCB
Philippians 2 in the BPBB
Philippians 2 in the BPH
Philippians 2 in the BSB
Philippians 2 in the CCB
Philippians 2 in the CUV
Philippians 2 in the CUVS
Philippians 2 in the DBT
Philippians 2 in the DGDNT
Philippians 2 in the DHNT
Philippians 2 in the DNT
Philippians 2 in the ELBE
Philippians 2 in the EMTV
Philippians 2 in the ESV
Philippians 2 in the FBV
Philippians 2 in the FEB
Philippians 2 in the GGMNT
Philippians 2 in the GNT
Philippians 2 in the HARY
Philippians 2 in the HNT
Philippians 2 in the IRVA
Philippians 2 in the IRVB
Philippians 2 in the IRVG
Philippians 2 in the IRVH
Philippians 2 in the IRVK
Philippians 2 in the IRVM
Philippians 2 in the IRVM2
Philippians 2 in the IRVO
Philippians 2 in the IRVP
Philippians 2 in the IRVT
Philippians 2 in the IRVT2
Philippians 2 in the IRVU
Philippians 2 in the ISVN
Philippians 2 in the JSNT
Philippians 2 in the KAPI
Philippians 2 in the KBT1ETNIK
Philippians 2 in the KBV
Philippians 2 in the KJV
Philippians 2 in the KNFD
Philippians 2 in the LBA
Philippians 2 in the LBLA
Philippians 2 in the LNT
Philippians 2 in the LSV
Philippians 2 in the MAAL
Philippians 2 in the MBV
Philippians 2 in the MBV2
Philippians 2 in the MHNT
Philippians 2 in the MKNFD
Philippians 2 in the MNG
Philippians 2 in the MNT
Philippians 2 in the MNT2
Philippians 2 in the MRS1T
Philippians 2 in the NAA
Philippians 2 in the NASB
Philippians 2 in the NBLA
Philippians 2 in the NBS
Philippians 2 in the NBVTP
Philippians 2 in the NET2
Philippians 2 in the NIV11
Philippians 2 in the NNT
Philippians 2 in the NNT2
Philippians 2 in the NNT3
Philippians 2 in the PDDPT
Philippians 2 in the PFNT
Philippians 2 in the RMNT
Philippians 2 in the SBIAS
Philippians 2 in the SBIBS
Philippians 2 in the SBIBS2
Philippians 2 in the SBICS
Philippians 2 in the SBIDS
Philippians 2 in the SBIGS
Philippians 2 in the SBIHS
Philippians 2 in the SBIIS
Philippians 2 in the SBIIS2
Philippians 2 in the SBIIS3
Philippians 2 in the SBIKS
Philippians 2 in the SBIKS2
Philippians 2 in the SBIMS
Philippians 2 in the SBIOS
Philippians 2 in the SBIPS
Philippians 2 in the SBISS
Philippians 2 in the SBITS
Philippians 2 in the SBITS2
Philippians 2 in the SBITS3
Philippians 2 in the SBITS4
Philippians 2 in the SBIUS
Philippians 2 in the SBIVS
Philippians 2 in the SBT
Philippians 2 in the SBT1E
Philippians 2 in the SCHL
Philippians 2 in the SNT
Philippians 2 in the SUSU
Philippians 2 in the SUSU2
Philippians 2 in the SYNO
Philippians 2 in the TBIAOTANT
Philippians 2 in the TBT1E
Philippians 2 in the TBT1E2
Philippians 2 in the TFTIP
Philippians 2 in the TFTU
Philippians 2 in the TGNTATF3T
Philippians 2 in the THAI
Philippians 2 in the TNFD
Philippians 2 in the TNT
Philippians 2 in the TNTIK
Philippians 2 in the TNTIL
Philippians 2 in the TNTIN
Philippians 2 in the TNTIP
Philippians 2 in the TNTIZ
Philippians 2 in the TOMA
Philippians 2 in the TTENT
Philippians 2 in the UBG
Philippians 2 in the UGV
Philippians 2 in the UGV2
Philippians 2 in the UGV3
Philippians 2 in the VBL
Philippians 2 in the VDCC
Philippians 2 in the YALU
Philippians 2 in the YAPE
Philippians 2 in the YBVTP
Philippians 2 in the ZBP