Philippians 3 (BOGWICC)
1 Abale anga, ndikupitiriza kunena kuti, kondwani mwa Ambuye! Sizondivuta kuti ndilembenso mawu omwewo, ndipo zimenezi nʼzokuthandizani inuyo. 2 Chenjerani ndi agalu amenewa, anthu ochita zoyipa, anthu amene amadula thupi lawo. 3 Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi 4 ngakhale kuti ineyo ndili ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupizo.Ngati pali winanso amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupi, ineyo ndili ndi zifukwa zoposa pamenepo. 5 Ndinachita mdulidwe pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditangobadwa. Ndine wa mtundu wa Israeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, kunena za malamulo, ndinali Mfarisi. 6 Kunena za changu changa, ndinkazunza mpingo. Kunena za chilungamo chopezeka chifukwa chotsata malamulo, ineyo ndinali wopanda cholakwa. 7 Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. 8 Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu 9 ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro. 10 Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake 11 kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa. 12 Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiyitanira. 13 Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. 14 Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu. 15 Choncho ife tonse amene tili okhwima pa moyo wauzimu, tikhale ndi maganizo omwewa. Ndipo ngati pena ndi pena muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa, pameneponso Mulungu adzakuwunikirani. 16 Tiyeni ife tizikhala mogwirizana ndi zimene tinapeza kale basi. 17 Abale, nonsenu pamodzi mudzinditsanzira ine, ndipo monga inu muli ndi chitsanzo, phunzirani kwa amene akukhala moyo motsatira momwe timakhalira. 18 Pakuti monga ndakhala ndikukuwuzani kawirikawiri mʼmbuyomu, ndipo tsopano ndikunenanso ndi misozi kuti, anthu ambiri akukhala monga adani a mtanda wa Khristu. 19 Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo. Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi. 20 Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. 21 Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.
In Other Versions
Philippians 3 in the ANGEFD
Philippians 3 in the ANTPNG2D
Philippians 3 in the AS21
Philippians 3 in the BAGH
Philippians 3 in the BBPNG
Philippians 3 in the BBT1E
Philippians 3 in the BDS
Philippians 3 in the BEV
Philippians 3 in the BHAD
Philippians 3 in the BIB
Philippians 3 in the BLPT
Philippians 3 in the BNT
Philippians 3 in the BNTABOOT
Philippians 3 in the BNTLV
Philippians 3 in the BOATCB
Philippians 3 in the BOATCB2
Philippians 3 in the BOBCV
Philippians 3 in the BOCNT
Philippians 3 in the BOECS
Philippians 3 in the BOHCB
Philippians 3 in the BOHCV
Philippians 3 in the BOHLNT
Philippians 3 in the BOHNTLTAL
Philippians 3 in the BOICB
Philippians 3 in the BOILNTAP
Philippians 3 in the BOITCV
Philippians 3 in the BOKCV
Philippians 3 in the BOKCV2
Philippians 3 in the BOKHWOG
Philippians 3 in the BOKSSV
Philippians 3 in the BOLCB
Philippians 3 in the BOLCB2
Philippians 3 in the BOMCV
Philippians 3 in the BONAV
Philippians 3 in the BONCB
Philippians 3 in the BONLT
Philippians 3 in the BONUT2
Philippians 3 in the BOPLNT
Philippians 3 in the BOSCB
Philippians 3 in the BOSNC
Philippians 3 in the BOTLNT
Philippians 3 in the BOVCB
Philippians 3 in the BOYCB
Philippians 3 in the BPBB
Philippians 3 in the BPH
Philippians 3 in the BSB
Philippians 3 in the CCB
Philippians 3 in the CUV
Philippians 3 in the CUVS
Philippians 3 in the DBT
Philippians 3 in the DGDNT
Philippians 3 in the DHNT
Philippians 3 in the DNT
Philippians 3 in the ELBE
Philippians 3 in the EMTV
Philippians 3 in the ESV
Philippians 3 in the FBV
Philippians 3 in the FEB
Philippians 3 in the GGMNT
Philippians 3 in the GNT
Philippians 3 in the HARY
Philippians 3 in the HNT
Philippians 3 in the IRVA
Philippians 3 in the IRVB
Philippians 3 in the IRVG
Philippians 3 in the IRVH
Philippians 3 in the IRVK
Philippians 3 in the IRVM
Philippians 3 in the IRVM2
Philippians 3 in the IRVO
Philippians 3 in the IRVP
Philippians 3 in the IRVT
Philippians 3 in the IRVT2
Philippians 3 in the IRVU
Philippians 3 in the ISVN
Philippians 3 in the JSNT
Philippians 3 in the KAPI
Philippians 3 in the KBT1ETNIK
Philippians 3 in the KBV
Philippians 3 in the KJV
Philippians 3 in the KNFD
Philippians 3 in the LBA
Philippians 3 in the LBLA
Philippians 3 in the LNT
Philippians 3 in the LSV
Philippians 3 in the MAAL
Philippians 3 in the MBV
Philippians 3 in the MBV2
Philippians 3 in the MHNT
Philippians 3 in the MKNFD
Philippians 3 in the MNG
Philippians 3 in the MNT
Philippians 3 in the MNT2
Philippians 3 in the MRS1T
Philippians 3 in the NAA
Philippians 3 in the NASB
Philippians 3 in the NBLA
Philippians 3 in the NBS
Philippians 3 in the NBVTP
Philippians 3 in the NET2
Philippians 3 in the NIV11
Philippians 3 in the NNT
Philippians 3 in the NNT2
Philippians 3 in the NNT3
Philippians 3 in the PDDPT
Philippians 3 in the PFNT
Philippians 3 in the RMNT
Philippians 3 in the SBIAS
Philippians 3 in the SBIBS
Philippians 3 in the SBIBS2
Philippians 3 in the SBICS
Philippians 3 in the SBIDS
Philippians 3 in the SBIGS
Philippians 3 in the SBIHS
Philippians 3 in the SBIIS
Philippians 3 in the SBIIS2
Philippians 3 in the SBIIS3
Philippians 3 in the SBIKS
Philippians 3 in the SBIKS2
Philippians 3 in the SBIMS
Philippians 3 in the SBIOS
Philippians 3 in the SBIPS
Philippians 3 in the SBISS
Philippians 3 in the SBITS
Philippians 3 in the SBITS2
Philippians 3 in the SBITS3
Philippians 3 in the SBITS4
Philippians 3 in the SBIUS
Philippians 3 in the SBIVS
Philippians 3 in the SBT
Philippians 3 in the SBT1E
Philippians 3 in the SCHL
Philippians 3 in the SNT
Philippians 3 in the SUSU
Philippians 3 in the SUSU2
Philippians 3 in the SYNO
Philippians 3 in the TBIAOTANT
Philippians 3 in the TBT1E
Philippians 3 in the TBT1E2
Philippians 3 in the TFTIP
Philippians 3 in the TFTU
Philippians 3 in the TGNTATF3T
Philippians 3 in the THAI
Philippians 3 in the TNFD
Philippians 3 in the TNT
Philippians 3 in the TNTIK
Philippians 3 in the TNTIL
Philippians 3 in the TNTIN
Philippians 3 in the TNTIP
Philippians 3 in the TNTIZ
Philippians 3 in the TOMA
Philippians 3 in the TTENT
Philippians 3 in the UBG
Philippians 3 in the UGV
Philippians 3 in the UGV2
Philippians 3 in the UGV3
Philippians 3 in the VBL
Philippians 3 in the VDCC
Philippians 3 in the YALU
Philippians 3 in the YAPE
Philippians 3 in the YBVTP
Philippians 3 in the ZBP