Philippians 4 (BOGWICC)

1 Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Ndinu chimwemwe changa ndi chipewa cha ulemerero wanga. Abwenzi okondedwa, chilimikani choncho mwa Ambuye. 2 Ndikudandaulira Euodiya ndi Suntuke kuti akhale ndi mtima umodzi mwa Ambuye. 3 Inde, ndikupempha iwe mnzanga pa ntchitoyi, thandiza amayiwa amene ndagwira nawo ntchito ya Uthenga Wabwino pamodzi ndi Klementonso ndi ena onse antchito anzanga amene mayina awo ali mʼbuku lamoyo. 4 Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa! 5 Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi. 6 Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. 7 Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu. 8 Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka. 9 Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu. 10 Ndikukondwa kwambiri mwa Ambuye kuti patapita nthawi tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizira. Zoonadi, mwakhala mukundikumbukira, koma munalibe mpata woti muonetsere zimenezi. 11 Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. 12 Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. 13 Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu. 14 Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. 15 Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu. 16 Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga. 17 Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. 18 Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. 19 Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu. 20 Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni. 21 Perekani moni kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akupereka moni wawo. 22 Oyera mtima onse akupereka moni, makamaka iwo a ku nyumba ya Kaisara. 23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Ameni.

In Other Versions

Philippians 4 in the ANGEFD

Philippians 4 in the ANTPNG2D

Philippians 4 in the AS21

Philippians 4 in the BAGH

Philippians 4 in the BBPNG

Philippians 4 in the BBT1E

Philippians 4 in the BDS

Philippians 4 in the BEV

Philippians 4 in the BHAD

Philippians 4 in the BIB

Philippians 4 in the BLPT

Philippians 4 in the BNT

Philippians 4 in the BNTABOOT

Philippians 4 in the BNTLV

Philippians 4 in the BOATCB

Philippians 4 in the BOATCB2

Philippians 4 in the BOBCV

Philippians 4 in the BOCNT

Philippians 4 in the BOECS

Philippians 4 in the BOHCB

Philippians 4 in the BOHCV

Philippians 4 in the BOHLNT

Philippians 4 in the BOHNTLTAL

Philippians 4 in the BOICB

Philippians 4 in the BOILNTAP

Philippians 4 in the BOITCV

Philippians 4 in the BOKCV

Philippians 4 in the BOKCV2

Philippians 4 in the BOKHWOG

Philippians 4 in the BOKSSV

Philippians 4 in the BOLCB

Philippians 4 in the BOLCB2

Philippians 4 in the BOMCV

Philippians 4 in the BONAV

Philippians 4 in the BONCB

Philippians 4 in the BONLT

Philippians 4 in the BONUT2

Philippians 4 in the BOPLNT

Philippians 4 in the BOSCB

Philippians 4 in the BOSNC

Philippians 4 in the BOTLNT

Philippians 4 in the BOVCB

Philippians 4 in the BOYCB

Philippians 4 in the BPBB

Philippians 4 in the BPH

Philippians 4 in the BSB

Philippians 4 in the CCB

Philippians 4 in the CUV

Philippians 4 in the CUVS

Philippians 4 in the DBT

Philippians 4 in the DGDNT

Philippians 4 in the DHNT

Philippians 4 in the DNT

Philippians 4 in the ELBE

Philippians 4 in the EMTV

Philippians 4 in the ESV

Philippians 4 in the FBV

Philippians 4 in the FEB

Philippians 4 in the GGMNT

Philippians 4 in the GNT

Philippians 4 in the HARY

Philippians 4 in the HNT

Philippians 4 in the IRVA

Philippians 4 in the IRVB

Philippians 4 in the IRVG

Philippians 4 in the IRVH

Philippians 4 in the IRVK

Philippians 4 in the IRVM

Philippians 4 in the IRVM2

Philippians 4 in the IRVO

Philippians 4 in the IRVP

Philippians 4 in the IRVT

Philippians 4 in the IRVT2

Philippians 4 in the IRVU

Philippians 4 in the ISVN

Philippians 4 in the JSNT

Philippians 4 in the KAPI

Philippians 4 in the KBT1ETNIK

Philippians 4 in the KBV

Philippians 4 in the KJV

Philippians 4 in the KNFD

Philippians 4 in the LBA

Philippians 4 in the LBLA

Philippians 4 in the LNT

Philippians 4 in the LSV

Philippians 4 in the MAAL

Philippians 4 in the MBV

Philippians 4 in the MBV2

Philippians 4 in the MHNT

Philippians 4 in the MKNFD

Philippians 4 in the MNG

Philippians 4 in the MNT

Philippians 4 in the MNT2

Philippians 4 in the MRS1T

Philippians 4 in the NAA

Philippians 4 in the NASB

Philippians 4 in the NBLA

Philippians 4 in the NBS

Philippians 4 in the NBVTP

Philippians 4 in the NET2

Philippians 4 in the NIV11

Philippians 4 in the NNT

Philippians 4 in the NNT2

Philippians 4 in the NNT3

Philippians 4 in the PDDPT

Philippians 4 in the PFNT

Philippians 4 in the RMNT

Philippians 4 in the SBIAS

Philippians 4 in the SBIBS

Philippians 4 in the SBIBS2

Philippians 4 in the SBICS

Philippians 4 in the SBIDS

Philippians 4 in the SBIGS

Philippians 4 in the SBIHS

Philippians 4 in the SBIIS

Philippians 4 in the SBIIS2

Philippians 4 in the SBIIS3

Philippians 4 in the SBIKS

Philippians 4 in the SBIKS2

Philippians 4 in the SBIMS

Philippians 4 in the SBIOS

Philippians 4 in the SBIPS

Philippians 4 in the SBISS

Philippians 4 in the SBITS

Philippians 4 in the SBITS2

Philippians 4 in the SBITS3

Philippians 4 in the SBITS4

Philippians 4 in the SBIUS

Philippians 4 in the SBIVS

Philippians 4 in the SBT

Philippians 4 in the SBT1E

Philippians 4 in the SCHL

Philippians 4 in the SNT

Philippians 4 in the SUSU

Philippians 4 in the SUSU2

Philippians 4 in the SYNO

Philippians 4 in the TBIAOTANT

Philippians 4 in the TBT1E

Philippians 4 in the TBT1E2

Philippians 4 in the TFTIP

Philippians 4 in the TFTU

Philippians 4 in the TGNTATF3T

Philippians 4 in the THAI

Philippians 4 in the TNFD

Philippians 4 in the TNT

Philippians 4 in the TNTIK

Philippians 4 in the TNTIL

Philippians 4 in the TNTIN

Philippians 4 in the TNTIP

Philippians 4 in the TNTIZ

Philippians 4 in the TOMA

Philippians 4 in the TTENT

Philippians 4 in the UBG

Philippians 4 in the UGV

Philippians 4 in the UGV2

Philippians 4 in the UGV3

Philippians 4 in the VBL

Philippians 4 in the VDCC

Philippians 4 in the YALU

Philippians 4 in the YAPE

Philippians 4 in the YBVTP

Philippians 4 in the ZBP