Proverbs 19 (BOGWICC)

1 Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro,aposa munthu wopusa woyankhula zokhota. 2 Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru;ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira. 3 Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta,mtima wake umakwiyira Yehova. 4 Chuma chimachulukitsa abwenzi;koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa. 5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa;ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka. 6 Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima,ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense. 7 Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye,nanji abwenzi ake tsono!Iwo adzamuthawa kupita kutali.Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse. 8 Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake.Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino. 9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka. 10 Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado,nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga! 11 Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga;ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa. 12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango,koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu. 13 Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo akendipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi. 14 Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo;koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova. 15 Ulesi umagonetsa tulo tofa natondipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala. 16 Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake,koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa. 17 Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova,ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere. 18 Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo;ngati sutero udzawononga moyo wake. 19 Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango;pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale. 20 Mvera uphungu ndipo landira malangizo;pa mapeto pake udzakhala wanzeru. 21 Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike. 22 Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha;nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza. 23 Kuopa Yehova kumabweretsa moyo;wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera. 24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale;koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake. 25 Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo;dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso. 26 Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa. 27 Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo,udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru. 28 Mboni yopanda pake imanyoza cholungama,ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa. 29 Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa,ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.

In Other Versions

Proverbs 19 in the ANGEFD

Proverbs 19 in the ANTPNG2D

Proverbs 19 in the AS21

Proverbs 19 in the BAGH

Proverbs 19 in the BBPNG

Proverbs 19 in the BBT1E

Proverbs 19 in the BDS

Proverbs 19 in the BEV

Proverbs 19 in the BHAD

Proverbs 19 in the BIB

Proverbs 19 in the BLPT

Proverbs 19 in the BNT

Proverbs 19 in the BNTABOOT

Proverbs 19 in the BNTLV

Proverbs 19 in the BOATCB

Proverbs 19 in the BOATCB2

Proverbs 19 in the BOBCV

Proverbs 19 in the BOCNT

Proverbs 19 in the BOECS

Proverbs 19 in the BOHCB

Proverbs 19 in the BOHCV

Proverbs 19 in the BOHLNT

Proverbs 19 in the BOHNTLTAL

Proverbs 19 in the BOICB

Proverbs 19 in the BOILNTAP

Proverbs 19 in the BOITCV

Proverbs 19 in the BOKCV

Proverbs 19 in the BOKCV2

Proverbs 19 in the BOKHWOG

Proverbs 19 in the BOKSSV

Proverbs 19 in the BOLCB

Proverbs 19 in the BOLCB2

Proverbs 19 in the BOMCV

Proverbs 19 in the BONAV

Proverbs 19 in the BONCB

Proverbs 19 in the BONLT

Proverbs 19 in the BONUT2

Proverbs 19 in the BOPLNT

Proverbs 19 in the BOSCB

Proverbs 19 in the BOSNC

Proverbs 19 in the BOTLNT

Proverbs 19 in the BOVCB

Proverbs 19 in the BOYCB

Proverbs 19 in the BPBB

Proverbs 19 in the BPH

Proverbs 19 in the BSB

Proverbs 19 in the CCB

Proverbs 19 in the CUV

Proverbs 19 in the CUVS

Proverbs 19 in the DBT

Proverbs 19 in the DGDNT

Proverbs 19 in the DHNT

Proverbs 19 in the DNT

Proverbs 19 in the ELBE

Proverbs 19 in the EMTV

Proverbs 19 in the ESV

Proverbs 19 in the FBV

Proverbs 19 in the FEB

Proverbs 19 in the GGMNT

Proverbs 19 in the GNT

Proverbs 19 in the HARY

Proverbs 19 in the HNT

Proverbs 19 in the IRVA

Proverbs 19 in the IRVB

Proverbs 19 in the IRVG

Proverbs 19 in the IRVH

Proverbs 19 in the IRVK

Proverbs 19 in the IRVM

Proverbs 19 in the IRVM2

Proverbs 19 in the IRVO

Proverbs 19 in the IRVP

Proverbs 19 in the IRVT

Proverbs 19 in the IRVT2

Proverbs 19 in the IRVU

Proverbs 19 in the ISVN

Proverbs 19 in the JSNT

Proverbs 19 in the KAPI

Proverbs 19 in the KBT1ETNIK

Proverbs 19 in the KBV

Proverbs 19 in the KJV

Proverbs 19 in the KNFD

Proverbs 19 in the LBA

Proverbs 19 in the LBLA

Proverbs 19 in the LNT

Proverbs 19 in the LSV

Proverbs 19 in the MAAL

Proverbs 19 in the MBV

Proverbs 19 in the MBV2

Proverbs 19 in the MHNT

Proverbs 19 in the MKNFD

Proverbs 19 in the MNG

Proverbs 19 in the MNT

Proverbs 19 in the MNT2

Proverbs 19 in the MRS1T

Proverbs 19 in the NAA

Proverbs 19 in the NASB

Proverbs 19 in the NBLA

Proverbs 19 in the NBS

Proverbs 19 in the NBVTP

Proverbs 19 in the NET2

Proverbs 19 in the NIV11

Proverbs 19 in the NNT

Proverbs 19 in the NNT2

Proverbs 19 in the NNT3

Proverbs 19 in the PDDPT

Proverbs 19 in the PFNT

Proverbs 19 in the RMNT

Proverbs 19 in the SBIAS

Proverbs 19 in the SBIBS

Proverbs 19 in the SBIBS2

Proverbs 19 in the SBICS

Proverbs 19 in the SBIDS

Proverbs 19 in the SBIGS

Proverbs 19 in the SBIHS

Proverbs 19 in the SBIIS

Proverbs 19 in the SBIIS2

Proverbs 19 in the SBIIS3

Proverbs 19 in the SBIKS

Proverbs 19 in the SBIKS2

Proverbs 19 in the SBIMS

Proverbs 19 in the SBIOS

Proverbs 19 in the SBIPS

Proverbs 19 in the SBISS

Proverbs 19 in the SBITS

Proverbs 19 in the SBITS2

Proverbs 19 in the SBITS3

Proverbs 19 in the SBITS4

Proverbs 19 in the SBIUS

Proverbs 19 in the SBIVS

Proverbs 19 in the SBT

Proverbs 19 in the SBT1E

Proverbs 19 in the SCHL

Proverbs 19 in the SNT

Proverbs 19 in the SUSU

Proverbs 19 in the SUSU2

Proverbs 19 in the SYNO

Proverbs 19 in the TBIAOTANT

Proverbs 19 in the TBT1E

Proverbs 19 in the TBT1E2

Proverbs 19 in the TFTIP

Proverbs 19 in the TFTU

Proverbs 19 in the TGNTATF3T

Proverbs 19 in the THAI

Proverbs 19 in the TNFD

Proverbs 19 in the TNT

Proverbs 19 in the TNTIK

Proverbs 19 in the TNTIL

Proverbs 19 in the TNTIN

Proverbs 19 in the TNTIP

Proverbs 19 in the TNTIZ

Proverbs 19 in the TOMA

Proverbs 19 in the TTENT

Proverbs 19 in the UBG

Proverbs 19 in the UGV

Proverbs 19 in the UGV2

Proverbs 19 in the UGV3

Proverbs 19 in the VBL

Proverbs 19 in the VDCC

Proverbs 19 in the YALU

Proverbs 19 in the YAPE

Proverbs 19 in the YBVTP

Proverbs 19 in the ZBP