Psalms 125 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya. 2 Monga mapiri azungulira Yerusalemu,momwemonso Yehova azungulira anthu akekuyambira tsopano mpaka muyaya. 3 Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhalapa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,kuti anthu olungamawoangachite nawonso zoyipa. 4 Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,amene ndi olungama mtima 5 Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa. Mtendere ukhale pa Israeli.