Psalms 126 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,tinali ngati amene akulota. 2 Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,“Yehova wawachitira zinthu zazikulu.” 3 Yehova watichitira zinthu zazikulu,ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe. 4 Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,monga mitsinje ya ku Negevi. 5 Iwo amene amafesa akulira,adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe. 6 Iye amene amayendayenda nalira,atanyamula mbewu yokafesa,adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,atanyamula mitolo yake.