Psalms 129 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,”anene tsono Israeli; 2 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,koma sanandipambane. 3 Anthu otipula analima pa msana pangandipo anapangapo mizere yayitali: 4 Koma Yehova ndi wolungama;Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.” 5 Onse amene amadana ndi Ziyoniabwezedwe pambuyo mwamanyazi. 6 Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,umene umafota usanakule; 7 sungadzaze manja a owumwetakapena manja a omanga mitolo. 8 Odutsa pafupi asanene kuti,“Dalitso la Yehova lili pa inu;tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”