Psalms 13 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 1 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu? 2 Ndidzalimbana ndi maganizo angandi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?Mpaka liti adani anga adzandipambana? 3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.Walitsani maso anga kuti ndingafe; 4 mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa. 5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu. 6 Ine ndidzayimbira Yehovapakuti wandichitira zokoma.