Psalms 22 (BOGWICC)

undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide. 1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya?Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe?Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga? 2 Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha,usikunso, ndipo sindikhala chete. 3 Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu;ndinu matamando a Israeli. 4 Pa inu makolo athu anadalira;iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa. 5 Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa.Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse. 6 Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse. 7 Onse amene amandiona amandiseka;amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti 8 “Iyeyu amadalira Yehova,musiyeni Yehovayo amulanditse.Musiyeni Yehova amupulumutsepopeza amakondwera mwa Yehovayo.” 9 Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.Munachititsa kuti ndizikudaliraningakhale pa nthawi imene ndinkayamwa. 10 Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga. 11 Musakhale kutali ndi ine,pakuti mavuto ali pafupindipo palibe wina wondipulumutsa. 12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira;ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga. 13 Mikango yobangula pokadzula nyama,yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane. 14 Ine ndatayika pansi ngati madzindipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake.Mtima wanga wasanduka phula;wasungunuka mʼkati mwanga. 15 Mphamvu zanga zauma ngati phale,ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada;mwandigoneka mʼfumbi la imfa. 16 Agalu andizungulira;gulu la anthu oyipa landizinga.Alasa manja ndi mapazi anga. 17 Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse;anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma. 18 Iwo agawana zovala zanga pakati pawondi kuchita maere pa zovala zangazo. 19 Koma Inu Yehova, musakhale kutali;Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize. 20 Pulumutsani moyo wanga ku lupanga,moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu. 21 Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango;pulumutseni ku nyanga za njati. 22 Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga;ndidzakutamandani mu msonkhano. 23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli! 24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyozakuvutika kwa wosautsidwayo;Iye sanabise nkhope yake kwa iye.Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo. 25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu. 26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta;iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya! 27 Malekezero onse a dziko lapansiadzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,ndipo mabanja a mitundu ya anthuadzawerama pamaso pake, 28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehovandipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse. 29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo. 30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye. 31 Iwo adzalengeza za chilungamo chakekwa anthu amene pano sanabadwepakuti Iye wachita zimenezi.

In Other Versions

Psalms 22 in the ANGEFD

Psalms 22 in the ANTPNG2D

Psalms 22 in the AS21

Psalms 22 in the BAGH

Psalms 22 in the BBPNG

Psalms 22 in the BBT1E

Psalms 22 in the BDS

Psalms 22 in the BEV

Psalms 22 in the BHAD

Psalms 22 in the BIB

Psalms 22 in the BLPT

Psalms 22 in the BNT

Psalms 22 in the BNTABOOT

Psalms 22 in the BNTLV

Psalms 22 in the BOATCB

Psalms 22 in the BOATCB2

Psalms 22 in the BOBCV

Psalms 22 in the BOCNT

Psalms 22 in the BOECS

Psalms 22 in the BOHCB

Psalms 22 in the BOHCV

Psalms 22 in the BOHLNT

Psalms 22 in the BOHNTLTAL

Psalms 22 in the BOICB

Psalms 22 in the BOILNTAP

Psalms 22 in the BOITCV

Psalms 22 in the BOKCV

Psalms 22 in the BOKCV2

Psalms 22 in the BOKHWOG

Psalms 22 in the BOKSSV

Psalms 22 in the BOLCB

Psalms 22 in the BOLCB2

Psalms 22 in the BOMCV

Psalms 22 in the BONAV

Psalms 22 in the BONCB

Psalms 22 in the BONLT

Psalms 22 in the BONUT2

Psalms 22 in the BOPLNT

Psalms 22 in the BOSCB

Psalms 22 in the BOSNC

Psalms 22 in the BOTLNT

Psalms 22 in the BOVCB

Psalms 22 in the BOYCB

Psalms 22 in the BPBB

Psalms 22 in the BPH

Psalms 22 in the BSB

Psalms 22 in the CCB

Psalms 22 in the CUV

Psalms 22 in the CUVS

Psalms 22 in the DBT

Psalms 22 in the DGDNT

Psalms 22 in the DHNT

Psalms 22 in the DNT

Psalms 22 in the ELBE

Psalms 22 in the EMTV

Psalms 22 in the ESV

Psalms 22 in the FBV

Psalms 22 in the FEB

Psalms 22 in the GGMNT

Psalms 22 in the GNT

Psalms 22 in the HARY

Psalms 22 in the HNT

Psalms 22 in the IRVA

Psalms 22 in the IRVB

Psalms 22 in the IRVG

Psalms 22 in the IRVH

Psalms 22 in the IRVK

Psalms 22 in the IRVM

Psalms 22 in the IRVM2

Psalms 22 in the IRVO

Psalms 22 in the IRVP

Psalms 22 in the IRVT

Psalms 22 in the IRVT2

Psalms 22 in the IRVU

Psalms 22 in the ISVN

Psalms 22 in the JSNT

Psalms 22 in the KAPI

Psalms 22 in the KBT1ETNIK

Psalms 22 in the KBV

Psalms 22 in the KJV

Psalms 22 in the KNFD

Psalms 22 in the LBA

Psalms 22 in the LBLA

Psalms 22 in the LNT

Psalms 22 in the LSV

Psalms 22 in the MAAL

Psalms 22 in the MBV

Psalms 22 in the MBV2

Psalms 22 in the MHNT

Psalms 22 in the MKNFD

Psalms 22 in the MNG

Psalms 22 in the MNT

Psalms 22 in the MNT2

Psalms 22 in the MRS1T

Psalms 22 in the NAA

Psalms 22 in the NASB

Psalms 22 in the NBLA

Psalms 22 in the NBS

Psalms 22 in the NBVTP

Psalms 22 in the NET2

Psalms 22 in the NIV11

Psalms 22 in the NNT

Psalms 22 in the NNT2

Psalms 22 in the NNT3

Psalms 22 in the PDDPT

Psalms 22 in the PFNT

Psalms 22 in the RMNT

Psalms 22 in the SBIAS

Psalms 22 in the SBIBS

Psalms 22 in the SBIBS2

Psalms 22 in the SBICS

Psalms 22 in the SBIDS

Psalms 22 in the SBIGS

Psalms 22 in the SBIHS

Psalms 22 in the SBIIS

Psalms 22 in the SBIIS2

Psalms 22 in the SBIIS3

Psalms 22 in the SBIKS

Psalms 22 in the SBIKS2

Psalms 22 in the SBIMS

Psalms 22 in the SBIOS

Psalms 22 in the SBIPS

Psalms 22 in the SBISS

Psalms 22 in the SBITS

Psalms 22 in the SBITS2

Psalms 22 in the SBITS3

Psalms 22 in the SBITS4

Psalms 22 in the SBIUS

Psalms 22 in the SBIVS

Psalms 22 in the SBT

Psalms 22 in the SBT1E

Psalms 22 in the SCHL

Psalms 22 in the SNT

Psalms 22 in the SUSU

Psalms 22 in the SUSU2

Psalms 22 in the SYNO

Psalms 22 in the TBIAOTANT

Psalms 22 in the TBT1E

Psalms 22 in the TBT1E2

Psalms 22 in the TFTIP

Psalms 22 in the TFTU

Psalms 22 in the TGNTATF3T

Psalms 22 in the THAI

Psalms 22 in the TNFD

Psalms 22 in the TNT

Psalms 22 in the TNTIK

Psalms 22 in the TNTIL

Psalms 22 in the TNTIN

Psalms 22 in the TNTIP

Psalms 22 in the TNTIZ

Psalms 22 in the TOMA

Psalms 22 in the TTENT

Psalms 22 in the UBG

Psalms 22 in the UGV

Psalms 22 in the UGV2

Psalms 22 in the UGV3

Psalms 22 in the VBL

Psalms 22 in the VDCC

Psalms 22 in the YALU

Psalms 22 in the YAPE

Psalms 22 in the YBVTP

Psalms 22 in the ZBP