Psalms 69 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.” 1 Pulumutseni Inu Mulungu,pakuti madzi afika mʼkhosi 2 Ine ndikumira mʼthope lozamamʼmene mulibe popondapo.Ndalowa mʼmadzi ozama;mafunde andimiza. 3 Ndafowoka ndikupempha chithandizo;kummero kwanga kwawuma gwaa,mʼmaso mwanga mwadakuyembekezera Mulungu wanga. 4 Iwo amene amadana nane popanda chifukwandi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,iwo amene akufunafuna kundiwononga.Ndikukakamizidwa kubwezerazomwe sindinabe. 5 Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu. 6 Iwo amene amadalira Inuasanyozedwe chifukwa cha ine,Inu Ambuye Wamphamvuzonse.Iwo amene amafunafuna Inuasachititsidwe manyazi chifukwa cha ine,Inu Mulungu wa Israeli. 7 Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu,ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga. 8 Ndine mlendo kwa abale anga,munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga; 9 pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsandipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera. 10 Pamene ndikulira ndi kusala kudya,ndiyenera kupirira kunyozedwa; 11 pomwe ndavala chiguduli,anthu amandiseweretsa. 12 Iwo amene amakhala pa chipata amandinena,ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa. 13 Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye,pa nthawi yanu yondikomera mtima;mwa chikondi chanu chachikuluInu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa. 14 Mundilanditse kuchoka mʼmatope,musalole kuti ndimire,pulumutseni ine kwa iwoamene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama. 15 Musalole kuti chigumula chindimeze,kuya kusandimezendipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza. 16 Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu;mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine. 17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu,ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto. 18 Bwerani pafupi ndi kundilanditsa;ndiwomboleni chifukwa cha adani anga. 19 Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera,kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu. 20 Mnyozo waswa mtima wangandipo wandisiya wopanda thandizo lililonse;ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni,koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe. 21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changandi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu. 22 Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha;chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe. 23 Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonensondipo misana yawo ipindike mpaka kalekale. 24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo;mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu. 25 Malo awo akhale wopanda anthupasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo. 26 Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulazandi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka. 27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu. 28 Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyondipo asalembedwe pamodzi ndi olungama. 29 Ndikumva zowawa ndi kuzunzika;lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze. 30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko. 31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake. 32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo! 33 Yehova amamvera anthu osowandipo sanyoza anthu ake omangidwa. 34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo, 35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyonindi kumanganso mizinda ya Yuda,anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo; 36 ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.