Revelation 6 (BOGWICC)

1 Ndinaona pamene Mwana Wankhosa anatsekula chomatira choyamba cha zomatira zisanu ndi ziwiri zija. Ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chikunena liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!” 2 Nditayangʼana patsogolo pake ndinaona kavalo woyera! Wokwerapo wake anali ndi uta ndipo anapatsidwa chipewa chaufumu, ndipo anatuluka kupita kukagonjetsa anthu ena. 3 Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chija chikuti, “Bwera!” 4 Pamenepo kavalo wina wofiira anatulukira. Wokwerapo wake anapatsidwa mphamvu yochotsa mtendere pa dziko lapansi ndi kuchititsa anthu kuti aziphana wina ndi mnzake. Iyeyu anapatsidwa lupanga lalikulu. 5 Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wakuda! Wokwerapo wake anali ndi masikelo awiri mʼmanja mwake. 6 Ndinamva ngati liwu kuchokera pakati pa zamoyo zinayi zija likuti, “Kilogalamu imodzi ya tirigu mtengo ndi malipiro a tsiku limodzi ndipo makilogalamu atatu a barele mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi koma usawononge mafuta ndi vinyo!” 7 Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachinayi, ndinamva chamoyo chachinayi chija chikunena kuti, “Bwera!” 8 Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wotuwa! Wokwerapo wake dzina lake linali Imfa ndipo Hade inali kumutsatira pambuyo pake. Anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi kuti aphe ndi lupanga, njala, mliri, ndi zirombo zakuthengo za mʼdziko lapansi. 9 Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni. 10 Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?” 11 Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira. 12 Ndinayangʼanitsitsa pamene ankatsekula chomatira chachisanu ndi chimodzi. Ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Dzuwa linada ngati chiguduli chopanga ndi bweya wambuzi wakuda. Mwezi wonse unafiira ngati magazi, 13 ndipo nyenyezi zakuthambo zinagwa pa dziko lapansi ngati muja zimagwera nkhuyu zotsalira mu mtengo mphepo yamphamvu ikawomba. 14 Thambo linachoka ngati amayalulira mphasa ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa pa malo pake. 15 Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri. 16 Iwo anafuwulira mapiri ndi matanthwe kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira kuti asatione wokhala pa mpando waufumuyo ndi kupulumuka ku mkwiyo wa Mwana Wankhosa! 17 Pakuti tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika ndipo ndi ndani angathe kulimbapo?”

In Other Versions

Revelation 6 in the ANGEFD

Revelation 6 in the ANTPNG2D

Revelation 6 in the AS21

Revelation 6 in the BAGH

Revelation 6 in the BBPNG

Revelation 6 in the BBT1E

Revelation 6 in the BDS

Revelation 6 in the BEV

Revelation 6 in the BHAD

Revelation 6 in the BIB

Revelation 6 in the BLPT

Revelation 6 in the BNT

Revelation 6 in the BNTABOOT

Revelation 6 in the BNTLV

Revelation 6 in the BOATCB

Revelation 6 in the BOATCB2

Revelation 6 in the BOBCV

Revelation 6 in the BOCNT

Revelation 6 in the BOECS

Revelation 6 in the BOHCB

Revelation 6 in the BOHCV

Revelation 6 in the BOHLNT

Revelation 6 in the BOHNTLTAL

Revelation 6 in the BOICB

Revelation 6 in the BOILNTAP

Revelation 6 in the BOITCV

Revelation 6 in the BOKCV

Revelation 6 in the BOKCV2

Revelation 6 in the BOKHWOG

Revelation 6 in the BOKSSV

Revelation 6 in the BOLCB

Revelation 6 in the BOLCB2

Revelation 6 in the BOMCV

Revelation 6 in the BONAV

Revelation 6 in the BONCB

Revelation 6 in the BONLT

Revelation 6 in the BONUT2

Revelation 6 in the BOPLNT

Revelation 6 in the BOSCB

Revelation 6 in the BOSNC

Revelation 6 in the BOTLNT

Revelation 6 in the BOVCB

Revelation 6 in the BOYCB

Revelation 6 in the BPBB

Revelation 6 in the BPH

Revelation 6 in the BSB

Revelation 6 in the CCB

Revelation 6 in the CUV

Revelation 6 in the CUVS

Revelation 6 in the DBT

Revelation 6 in the DGDNT

Revelation 6 in the DHNT

Revelation 6 in the DNT

Revelation 6 in the ELBE

Revelation 6 in the EMTV

Revelation 6 in the ESV

Revelation 6 in the FBV

Revelation 6 in the FEB

Revelation 6 in the GGMNT

Revelation 6 in the GNT

Revelation 6 in the HARY

Revelation 6 in the HNT

Revelation 6 in the IRVA

Revelation 6 in the IRVB

Revelation 6 in the IRVG

Revelation 6 in the IRVH

Revelation 6 in the IRVK

Revelation 6 in the IRVM

Revelation 6 in the IRVM2

Revelation 6 in the IRVO

Revelation 6 in the IRVP

Revelation 6 in the IRVT

Revelation 6 in the IRVT2

Revelation 6 in the IRVU

Revelation 6 in the ISVN

Revelation 6 in the JSNT

Revelation 6 in the KAPI

Revelation 6 in the KBT1ETNIK

Revelation 6 in the KBV

Revelation 6 in the KJV

Revelation 6 in the KNFD

Revelation 6 in the LBA

Revelation 6 in the LBLA

Revelation 6 in the LNT

Revelation 6 in the LSV

Revelation 6 in the MAAL

Revelation 6 in the MBV

Revelation 6 in the MBV2

Revelation 6 in the MHNT

Revelation 6 in the MKNFD

Revelation 6 in the MNG

Revelation 6 in the MNT

Revelation 6 in the MNT2

Revelation 6 in the MRS1T

Revelation 6 in the NAA

Revelation 6 in the NASB

Revelation 6 in the NBLA

Revelation 6 in the NBS

Revelation 6 in the NBVTP

Revelation 6 in the NET2

Revelation 6 in the NIV11

Revelation 6 in the NNT

Revelation 6 in the NNT2

Revelation 6 in the NNT3

Revelation 6 in the PDDPT

Revelation 6 in the PFNT

Revelation 6 in the RMNT

Revelation 6 in the SBIAS

Revelation 6 in the SBIBS

Revelation 6 in the SBIBS2

Revelation 6 in the SBICS

Revelation 6 in the SBIDS

Revelation 6 in the SBIGS

Revelation 6 in the SBIHS

Revelation 6 in the SBIIS

Revelation 6 in the SBIIS2

Revelation 6 in the SBIIS3

Revelation 6 in the SBIKS

Revelation 6 in the SBIKS2

Revelation 6 in the SBIMS

Revelation 6 in the SBIOS

Revelation 6 in the SBIPS

Revelation 6 in the SBISS

Revelation 6 in the SBITS

Revelation 6 in the SBITS2

Revelation 6 in the SBITS3

Revelation 6 in the SBITS4

Revelation 6 in the SBIUS

Revelation 6 in the SBIVS

Revelation 6 in the SBT

Revelation 6 in the SBT1E

Revelation 6 in the SCHL

Revelation 6 in the SNT

Revelation 6 in the SUSU

Revelation 6 in the SUSU2

Revelation 6 in the SYNO

Revelation 6 in the TBIAOTANT

Revelation 6 in the TBT1E

Revelation 6 in the TBT1E2

Revelation 6 in the TFTIP

Revelation 6 in the TFTU

Revelation 6 in the TGNTATF3T

Revelation 6 in the THAI

Revelation 6 in the TNFD

Revelation 6 in the TNT

Revelation 6 in the TNTIK

Revelation 6 in the TNTIL

Revelation 6 in the TNTIN

Revelation 6 in the TNTIP

Revelation 6 in the TNTIZ

Revelation 6 in the TOMA

Revelation 6 in the TTENT

Revelation 6 in the UBG

Revelation 6 in the UGV

Revelation 6 in the UGV2

Revelation 6 in the UGV3

Revelation 6 in the VBL

Revelation 6 in the VDCC

Revelation 6 in the YALU

Revelation 6 in the YAPE

Revelation 6 in the YBVTP

Revelation 6 in the ZBP