Romans 3 (BOGWICC)

1 Nanga kodi pali ubwino wotani pokhala Myuda, kapena muli ubwino wanjinso mu mdulidwe? 2 Ubwino wake ndi wambiri mʼnjira zonse! Choyambirira iwo anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti awasunge. 3 Nanga zili bwanji ngati ena analibe chikhulupiriro? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawo kukanalepheretsa kukhulupirika kwa Mulungu? 4 Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti,“Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhulandi kupambana pamene muweruza.” 5 Koma ngati kuyipa mtima kwathu kuonetsa poyera kuti Mulungu ndi wolungama, ife tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ndi wosalungama pamene aonetsa mkwiyo wake pa ife? (Ine ndikuyankhula monga mmene anthu ena amayankhulira). 6 Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ngati zikanakhala zotero, kodi Mulungu akanaweruza bwanji dziko lapansi? 7 Wina atanena kuti, “Ngati kunama kwanga kukuonetsa koposa kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemerero wake, nanga nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa kuti ndine wochimwa?” 8 Nʼchifukwa chiyani osanena kuti, monga ena amanena mosasamala kuti, “Tiyeni tichite zoyipa kuti zabwino zionekere?” Anthu onena zoterewa kulangidwa kwawo ndi koyenera. 9 Kodi timalize bwanji? Kodi Ayuda ndife oposa anthu ena? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ife tinanena kale kuti Ayuda ndi a mitundu ina omwe ndi ochimwa. 10 Monga kwalembedwa kuti,“Palibe munthu wolungama, inde palibe ndi mmodzi yemwe. 11 Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira,palibe amene amafunafuna Mulungu. 12 Onse apatukira kumbali,onse pamodzi asanduka opandapake.Palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita zabwino,palibe ngakhale mmodzi.” 13 “Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.”“Ululu wa mamba uli pa milomo yawo.” 14 “Mʼkamwa mwawo ndi modzaza ndi zotemberera ndi mawu owawa.” 15 “Mapazi awo afulumira kukakhetsa magazi. 16 Kusakaza ndi chisoni kumaonekera mʼnjira zawo, 17 ndipo njira ya mtendere sayidziwa.” 18 “Saopa Mulungu ndi pangʼono pomwe.” 19 Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu. 20 Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo. 21 Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni. 22 Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, 23 pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu 24 ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola. 25 Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale. 26 Iye anachita izi kuti aonetse chilungamo chake lero lino. Anthu azindikire kuti Iye ndi wolungama ndipo amalungamitsa aliyense amene akhulupirira Yesu. 27 Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Kunyadatu kwachotsedwa. Chifukwa cha Malamulo? Kodi Malamulo samafuna ntchito za munthu? Ayi, koma mwachikhulupiriro. 28 Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo. 29 Kodi Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si Mulungu wa a mitundu inanso? Inde wa a mitundu inanso, 30 popeza ndi Mulungu mmodzi yemweyo amene adzalungamitsa mwachikhulupiriro ochita mdulidwe ndi osachita mdulidwe kudzera mʼchikhulupiriro chomwecho. 31 Kodi tsono ife, tikutaya Malamulo pamene tikunena kuti pafunika chikhulupiriro? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Komatu ife tikukwaniritsadi Malamulo.

In Other Versions

Romans 3 in the ANGEFD

Romans 3 in the ANTPNG2D

Romans 3 in the AS21

Romans 3 in the BAGH

Romans 3 in the BBPNG

Romans 3 in the BBT1E

Romans 3 in the BDS

Romans 3 in the BEV

Romans 3 in the BHAD

Romans 3 in the BIB

Romans 3 in the BLPT

Romans 3 in the BNT

Romans 3 in the BNTABOOT

Romans 3 in the BNTLV

Romans 3 in the BOATCB

Romans 3 in the BOATCB2

Romans 3 in the BOBCV

Romans 3 in the BOCNT

Romans 3 in the BOECS

Romans 3 in the BOHCB

Romans 3 in the BOHCV

Romans 3 in the BOHLNT

Romans 3 in the BOHNTLTAL

Romans 3 in the BOICB

Romans 3 in the BOILNTAP

Romans 3 in the BOITCV

Romans 3 in the BOKCV

Romans 3 in the BOKCV2

Romans 3 in the BOKHWOG

Romans 3 in the BOKSSV

Romans 3 in the BOLCB

Romans 3 in the BOLCB2

Romans 3 in the BOMCV

Romans 3 in the BONAV

Romans 3 in the BONCB

Romans 3 in the BONLT

Romans 3 in the BONUT2

Romans 3 in the BOPLNT

Romans 3 in the BOSCB

Romans 3 in the BOSNC

Romans 3 in the BOTLNT

Romans 3 in the BOVCB

Romans 3 in the BOYCB

Romans 3 in the BPBB

Romans 3 in the BPH

Romans 3 in the BSB

Romans 3 in the CCB

Romans 3 in the CUV

Romans 3 in the CUVS

Romans 3 in the DBT

Romans 3 in the DGDNT

Romans 3 in the DHNT

Romans 3 in the DNT

Romans 3 in the ELBE

Romans 3 in the EMTV

Romans 3 in the ESV

Romans 3 in the FBV

Romans 3 in the FEB

Romans 3 in the GGMNT

Romans 3 in the GNT

Romans 3 in the HARY

Romans 3 in the HNT

Romans 3 in the IRVA

Romans 3 in the IRVB

Romans 3 in the IRVG

Romans 3 in the IRVH

Romans 3 in the IRVK

Romans 3 in the IRVM

Romans 3 in the IRVM2

Romans 3 in the IRVO

Romans 3 in the IRVP

Romans 3 in the IRVT

Romans 3 in the IRVT2

Romans 3 in the IRVU

Romans 3 in the ISVN

Romans 3 in the JSNT

Romans 3 in the KAPI

Romans 3 in the KBT1ETNIK

Romans 3 in the KBV

Romans 3 in the KJV

Romans 3 in the KNFD

Romans 3 in the LBA

Romans 3 in the LBLA

Romans 3 in the LNT

Romans 3 in the LSV

Romans 3 in the MAAL

Romans 3 in the MBV

Romans 3 in the MBV2

Romans 3 in the MHNT

Romans 3 in the MKNFD

Romans 3 in the MNG

Romans 3 in the MNT

Romans 3 in the MNT2

Romans 3 in the MRS1T

Romans 3 in the NAA

Romans 3 in the NASB

Romans 3 in the NBLA

Romans 3 in the NBS

Romans 3 in the NBVTP

Romans 3 in the NET2

Romans 3 in the NIV11

Romans 3 in the NNT

Romans 3 in the NNT2

Romans 3 in the NNT3

Romans 3 in the PDDPT

Romans 3 in the PFNT

Romans 3 in the RMNT

Romans 3 in the SBIAS

Romans 3 in the SBIBS

Romans 3 in the SBIBS2

Romans 3 in the SBICS

Romans 3 in the SBIDS

Romans 3 in the SBIGS

Romans 3 in the SBIHS

Romans 3 in the SBIIS

Romans 3 in the SBIIS2

Romans 3 in the SBIIS3

Romans 3 in the SBIKS

Romans 3 in the SBIKS2

Romans 3 in the SBIMS

Romans 3 in the SBIOS

Romans 3 in the SBIPS

Romans 3 in the SBISS

Romans 3 in the SBITS

Romans 3 in the SBITS2

Romans 3 in the SBITS3

Romans 3 in the SBITS4

Romans 3 in the SBIUS

Romans 3 in the SBIVS

Romans 3 in the SBT

Romans 3 in the SBT1E

Romans 3 in the SCHL

Romans 3 in the SNT

Romans 3 in the SUSU

Romans 3 in the SUSU2

Romans 3 in the SYNO

Romans 3 in the TBIAOTANT

Romans 3 in the TBT1E

Romans 3 in the TBT1E2

Romans 3 in the TFTIP

Romans 3 in the TFTU

Romans 3 in the TGNTATF3T

Romans 3 in the THAI

Romans 3 in the TNFD

Romans 3 in the TNT

Romans 3 in the TNTIK

Romans 3 in the TNTIL

Romans 3 in the TNTIN

Romans 3 in the TNTIP

Romans 3 in the TNTIZ

Romans 3 in the TOMA

Romans 3 in the TTENT

Romans 3 in the UBG

Romans 3 in the UGV

Romans 3 in the UGV2

Romans 3 in the UGV3

Romans 3 in the VBL

Romans 3 in the VDCC

Romans 3 in the YALU

Romans 3 in the YAPE

Romans 3 in the YBVTP

Romans 3 in the ZBP