Romans 5 (BOGWICC)
1 Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. 2 Iyeyo ndiye amene anatsekulira njira mwachikhulupiriro yolowera mʼchisomo mʼmene takhazikikamo. Ndipo tikukondwerera chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. 3 Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. 4 Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo. 5 Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake. 6 Pakuti pa nthawi yake, tikanali ochimwa, Khristu anatifera anthu osapembedzafe. 7 Sizichitika kawirikawiri kuti munthu wina afere munthu wolungama, ngakhale kuti chifukwa cha munthu wabwino wina atha kulimba mtima kumufera. 8 Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera. 9 Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu. 10 Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye? 11 Sikuti izi zili chomwechi chabe, koma timakondweranso mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Kudzera mwa Iye, ife tsopano tayanjanitsidwa ndi Mulungu. 12 Choncho monga momwe tchimo linalowa mʼdziko lapansi kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mu tchimo, mʼnjirayi imfa inafika kwa anthu onse pakuti onse anachimwa. 13 Pakuti Malamulo asanaperekedwe, tchimo linali mʼdziko lapansi. Koma pamene palibe Malamulo, tchimo silitengedwa kukhala tchimo. 14 Komabe, imfa inalamulira kuyambira nthawi ya Adamu mpaka nthawi ya Mose. Inalamulira ngakhalenso pa iwo amene sanachimwe posamvera Malamulo monga anachitira Adamu. Adamuyo amene anali chifaniziro cha wina amene ankabwera. 15 Koma sitingafananitse mphatso yaulereyo ndi kuchimwa kwa anthu. Pakuti ngati anthu ambiri anafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga chisomo cha Mulungu ndi mphatso zomwe zinabwera ndi chisomo cha munthu mmodzi, Yesu Khristu, ndi kusefukira kwa ambiri! 16 Ndiponso, mphatso ya Mulungu sifanana ndi zotsatira za kuchimwa kwa munthu mmodzi. Chiweruzo chinatsatira tchimo la munthu mmodzi ndi kubweretsa kutsutsidwa koma mphatso inatsatira zolakwa zambiri ndi kubweretsa kulungamitsidwa. 17 Pakuti ngati, chifukwa cha kulakwa kwa munthu mmodziyo, imfa inalamulira kudzera mwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga kwa iwo amene adzalandira chisomo chochuluka ndi mphatso yachilungamo, adzalamulira mʼmoyo kudzera mwa munthu mmodzi, Yesu Khristu. 18 Choncho monga tchimo limodzi linabweretsa kutsutsika pa anthu onse, chimodzimodzinso ntchito imodzi yolungama inabweretsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuwapatsa moyo. 19 Pakuti kusamvera kwa munthu mmodzi kunasandutsa anthu ambiri kukhala ochimwa, chimodzimodzinso anthu ambiri adzasanduka olungama kudzera mwa munthu mmodzinso. 20 Malamulo a Mulungu anaperekedwa ndi cholinga chakuti anthu onse azindikire kuchuluka kwa machimo awo. Koma pamene machimo anachuluka, chisomo chinachuluka koposa. 21 Choncho monga momwe tchimo linkalamulira anthu ndi kubweretsa imfa pa iwo, chomwecho kunali koyenera kuti chisomo chilamulire pobweretsa chilungamo kwa anthu, ndi kuwafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
In Other Versions
Romans 5 in the ANGEFD
Romans 5 in the ANTPNG2D
Romans 5 in the AS21
Romans 5 in the BAGH
Romans 5 in the BBPNG
Romans 5 in the BBT1E
Romans 5 in the BDS
Romans 5 in the BEV
Romans 5 in the BHAD
Romans 5 in the BIB
Romans 5 in the BLPT
Romans 5 in the BNT
Romans 5 in the BNTABOOT
Romans 5 in the BNTLV
Romans 5 in the BOATCB
Romans 5 in the BOATCB2
Romans 5 in the BOBCV
Romans 5 in the BOCNT
Romans 5 in the BOECS
Romans 5 in the BOHCB
Romans 5 in the BOHCV
Romans 5 in the BOHLNT
Romans 5 in the BOHNTLTAL
Romans 5 in the BOICB
Romans 5 in the BOILNTAP
Romans 5 in the BOITCV
Romans 5 in the BOKCV
Romans 5 in the BOKCV2
Romans 5 in the BOKHWOG
Romans 5 in the BOKSSV
Romans 5 in the BOLCB
Romans 5 in the BOLCB2
Romans 5 in the BOMCV
Romans 5 in the BONAV
Romans 5 in the BONCB
Romans 5 in the BONLT
Romans 5 in the BONUT2
Romans 5 in the BOPLNT
Romans 5 in the BOSCB
Romans 5 in the BOSNC
Romans 5 in the BOTLNT
Romans 5 in the BOVCB
Romans 5 in the BOYCB
Romans 5 in the BPBB
Romans 5 in the BPH
Romans 5 in the BSB
Romans 5 in the CCB
Romans 5 in the CUV
Romans 5 in the CUVS
Romans 5 in the DBT
Romans 5 in the DGDNT
Romans 5 in the DHNT
Romans 5 in the DNT
Romans 5 in the ELBE
Romans 5 in the EMTV
Romans 5 in the ESV
Romans 5 in the FBV
Romans 5 in the FEB
Romans 5 in the GGMNT
Romans 5 in the GNT
Romans 5 in the HARY
Romans 5 in the HNT
Romans 5 in the IRVA
Romans 5 in the IRVB
Romans 5 in the IRVG
Romans 5 in the IRVH
Romans 5 in the IRVK
Romans 5 in the IRVM
Romans 5 in the IRVM2
Romans 5 in the IRVO
Romans 5 in the IRVP
Romans 5 in the IRVT
Romans 5 in the IRVT2
Romans 5 in the IRVU
Romans 5 in the ISVN
Romans 5 in the JSNT
Romans 5 in the KAPI
Romans 5 in the KBT1ETNIK
Romans 5 in the KBV
Romans 5 in the KJV
Romans 5 in the KNFD
Romans 5 in the LBA
Romans 5 in the LBLA
Romans 5 in the LNT
Romans 5 in the LSV
Romans 5 in the MAAL
Romans 5 in the MBV
Romans 5 in the MBV2
Romans 5 in the MHNT
Romans 5 in the MKNFD
Romans 5 in the MNG
Romans 5 in the MNT
Romans 5 in the MNT2
Romans 5 in the MRS1T
Romans 5 in the NAA
Romans 5 in the NASB
Romans 5 in the NBLA
Romans 5 in the NBS
Romans 5 in the NBVTP
Romans 5 in the NET2
Romans 5 in the NIV11
Romans 5 in the NNT
Romans 5 in the NNT2
Romans 5 in the NNT3
Romans 5 in the PDDPT
Romans 5 in the PFNT
Romans 5 in the RMNT
Romans 5 in the SBIAS
Romans 5 in the SBIBS
Romans 5 in the SBIBS2
Romans 5 in the SBICS
Romans 5 in the SBIDS
Romans 5 in the SBIGS
Romans 5 in the SBIHS
Romans 5 in the SBIIS
Romans 5 in the SBIIS2
Romans 5 in the SBIIS3
Romans 5 in the SBIKS
Romans 5 in the SBIKS2
Romans 5 in the SBIMS
Romans 5 in the SBIOS
Romans 5 in the SBIPS
Romans 5 in the SBISS
Romans 5 in the SBITS
Romans 5 in the SBITS2
Romans 5 in the SBITS3
Romans 5 in the SBITS4
Romans 5 in the SBIUS
Romans 5 in the SBIVS
Romans 5 in the SBT
Romans 5 in the SBT1E
Romans 5 in the SCHL
Romans 5 in the SNT
Romans 5 in the SUSU
Romans 5 in the SUSU2
Romans 5 in the SYNO
Romans 5 in the TBIAOTANT
Romans 5 in the TBT1E
Romans 5 in the TBT1E2
Romans 5 in the TFTIP
Romans 5 in the TFTU
Romans 5 in the TGNTATF3T
Romans 5 in the THAI
Romans 5 in the TNFD
Romans 5 in the TNT
Romans 5 in the TNTIK
Romans 5 in the TNTIL
Romans 5 in the TNTIN
Romans 5 in the TNTIP
Romans 5 in the TNTIZ
Romans 5 in the TOMA
Romans 5 in the TTENT
Romans 5 in the UBG
Romans 5 in the UGV
Romans 5 in the UGV2
Romans 5 in the UGV3
Romans 5 in the VBL
Romans 5 in the VDCC
Romans 5 in the YALU
Romans 5 in the YAPE
Romans 5 in the YBVTP
Romans 5 in the ZBP