Ruth 3 (BOGWICC)
1 Tsiku lina Naomi anafunsa mpongozi wake Rute kuti, “Mwana wanga, kodi si kwabwino kuti ndikupezere kokhala kuti zinthu zizikuyendera bwino? 2 Bowazi amene adzakazi ake wakhala nawo nthawi yonseyi, si wachibale wathu kodi? Usiku uno akhala akupeta barele ku malo opunthira. 3 Samba ndi kudzola mafuta onunkhira, ndipo uvale zovala zako zabwino kwambiri. Kenaka upite ku malo opunthirako tirigu ndi barele koma munthuyo asakakuzindikire kufikira atamaliza kudya ndi kumwa. 4 Akamakagona, iwe ukaonetsetse malo amene wagonawo. Kenaka upite ndi kuvundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona. Iyeyo akakuwuza zoti uchite.” 5 Rute anayankha kuti, “Ndichita zonse zimene mwanena.” 6 Choncho Rute anapita ku malo opunthirawo ndipo anachita monga momwe apongozi ake anamuwuza. 7 Atamaliza kudya ndi kumwa, Bowazi anakhala wosangalala, ndipo anakagona pa mbali pa mulu wa barele. Tsono Rute anapita mwa kachetechete, navundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona. 8 Tsono pakati pa usiku Bowazi anadzidzimuka, natembenuka, ndipo anangoona mkazi akugona ku mapazi ake. 9 Iye anafunsa kuti, “Ndiwe yani?” Ndipo anayankha kuti, “Ndine mdzakazi wanu Rute. Popeza ndinu wachibale amene muyenera kundiwombola, ndiye mundilowe chokolo.” 10 Ndipo Bowazi anati, “Mwana wanga, Yehova akudalitse popeza kukoma mtima kumene wasonyeza panoku kwaposa koyamba kaja. Iwe sunathamangire anyamata olemera kapena osauka. 11 Ndipo tsopano mwana wanga usaope. Ine ndidzakuchitira chilichonse udzapemphe popeza anzanga onse amʼmudzi muno akudziwa kuti ndiwe mkazi wa khalidwe labwino. 12 Ngakhale kuti ndinedi wachibale woyenera kukusamala, koma alipo wachibale weniweni kuposa ine. 13 Gona konkuno usiku uno mpaka mmawa. Tsono ngati iyeyu adzakulowa chokolo, chabwino alowe. Koma ngati safuna kutero, ine ndikulumbira pamaso pa Yehova Wamoyo kuti ndidzakulowa chokolo. Ugone kuno mpaka mmawa.” 14 Choncho Rute anagona ku mapazi ake mpaka mmawa, koma anadzuka mmamawa kusanayere chifukwa Bowazi anati, “Aliyense asadziwe kuti kopondera barele kunabwera mkazi.” 15 Bowazi anati kwa Rute, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho ndipo uchiyale pansi.” Ndipo atayala, Bowazi anathira makilogalamu makumi awiri a barele ndi kumusenzetsa Rute. Rute anapita nakalowa mu mzinda. 16 Rute atafika kwa apongozi ake anamufunsa kuti, “Zinayenda bwanji mwana wanga?” Kenaka iye anafotokoza zonse zimene Bowazi anamuchitira. 17 Ndipo anati, “Munthuyo anandipatsa makilogalamu makumi awiri awa a barele, nandiwuza kuti usapite kwa apongozi ako wopanda kanthu.” 18 Kenaka Naomi anati, “Mwana wanga, dikira mpaka titaona mmene zinthu zikhalire chifukwa munthuyu salekera pomwepo, mpaka zinthuzi zitakonzeka lero.”
In Other Versions
Ruth 3 in the ANGEFD
Ruth 3 in the ANTPNG2D
Ruth 3 in the AS21
Ruth 3 in the BAGH
Ruth 3 in the BBPNG
Ruth 3 in the BBT1E
Ruth 3 in the BDS
Ruth 3 in the BEV
Ruth 3 in the BHAD
Ruth 3 in the BIB
Ruth 3 in the BLPT
Ruth 3 in the BNT
Ruth 3 in the BNTABOOT
Ruth 3 in the BNTLV
Ruth 3 in the BOATCB
Ruth 3 in the BOATCB2
Ruth 3 in the BOBCV
Ruth 3 in the BOCNT
Ruth 3 in the BOECS
Ruth 3 in the BOHCB
Ruth 3 in the BOHCV
Ruth 3 in the BOHLNT
Ruth 3 in the BOHNTLTAL
Ruth 3 in the BOICB
Ruth 3 in the BOILNTAP
Ruth 3 in the BOITCV
Ruth 3 in the BOKCV
Ruth 3 in the BOKCV2
Ruth 3 in the BOKHWOG
Ruth 3 in the BOKSSV
Ruth 3 in the BOLCB
Ruth 3 in the BOLCB2
Ruth 3 in the BOMCV
Ruth 3 in the BONAV
Ruth 3 in the BONCB
Ruth 3 in the BONLT
Ruth 3 in the BONUT2
Ruth 3 in the BOPLNT
Ruth 3 in the BOSCB
Ruth 3 in the BOSNC
Ruth 3 in the BOTLNT
Ruth 3 in the BOVCB
Ruth 3 in the BOYCB
Ruth 3 in the BPBB
Ruth 3 in the BPH
Ruth 3 in the BSB
Ruth 3 in the CCB
Ruth 3 in the CUV
Ruth 3 in the CUVS
Ruth 3 in the DBT
Ruth 3 in the DGDNT
Ruth 3 in the DHNT
Ruth 3 in the DNT
Ruth 3 in the ELBE
Ruth 3 in the EMTV
Ruth 3 in the ESV
Ruth 3 in the FBV
Ruth 3 in the FEB
Ruth 3 in the GGMNT
Ruth 3 in the GNT
Ruth 3 in the HARY
Ruth 3 in the HNT
Ruth 3 in the IRVA
Ruth 3 in the IRVB
Ruth 3 in the IRVG
Ruth 3 in the IRVH
Ruth 3 in the IRVK
Ruth 3 in the IRVM
Ruth 3 in the IRVM2
Ruth 3 in the IRVO
Ruth 3 in the IRVP
Ruth 3 in the IRVT
Ruth 3 in the IRVT2
Ruth 3 in the IRVU
Ruth 3 in the ISVN
Ruth 3 in the JSNT
Ruth 3 in the KAPI
Ruth 3 in the KBT1ETNIK
Ruth 3 in the KBV
Ruth 3 in the KJV
Ruth 3 in the KNFD
Ruth 3 in the LBA
Ruth 3 in the LBLA
Ruth 3 in the LNT
Ruth 3 in the LSV
Ruth 3 in the MAAL
Ruth 3 in the MBV
Ruth 3 in the MBV2
Ruth 3 in the MHNT
Ruth 3 in the MKNFD
Ruth 3 in the MNG
Ruth 3 in the MNT
Ruth 3 in the MNT2
Ruth 3 in the MRS1T
Ruth 3 in the NAA
Ruth 3 in the NASB
Ruth 3 in the NBLA
Ruth 3 in the NBS
Ruth 3 in the NBVTP
Ruth 3 in the NET2
Ruth 3 in the NIV11
Ruth 3 in the NNT
Ruth 3 in the NNT2
Ruth 3 in the NNT3
Ruth 3 in the PDDPT
Ruth 3 in the PFNT
Ruth 3 in the RMNT
Ruth 3 in the SBIAS
Ruth 3 in the SBIBS
Ruth 3 in the SBIBS2
Ruth 3 in the SBICS
Ruth 3 in the SBIDS
Ruth 3 in the SBIGS
Ruth 3 in the SBIHS
Ruth 3 in the SBIIS
Ruth 3 in the SBIIS2
Ruth 3 in the SBIIS3
Ruth 3 in the SBIKS
Ruth 3 in the SBIKS2
Ruth 3 in the SBIMS
Ruth 3 in the SBIOS
Ruth 3 in the SBIPS
Ruth 3 in the SBISS
Ruth 3 in the SBITS
Ruth 3 in the SBITS2
Ruth 3 in the SBITS3
Ruth 3 in the SBITS4
Ruth 3 in the SBIUS
Ruth 3 in the SBIVS
Ruth 3 in the SBT
Ruth 3 in the SBT1E
Ruth 3 in the SCHL
Ruth 3 in the SNT
Ruth 3 in the SUSU
Ruth 3 in the SUSU2
Ruth 3 in the SYNO
Ruth 3 in the TBIAOTANT
Ruth 3 in the TBT1E
Ruth 3 in the TBT1E2
Ruth 3 in the TFTIP
Ruth 3 in the TFTU
Ruth 3 in the TGNTATF3T
Ruth 3 in the THAI
Ruth 3 in the TNFD
Ruth 3 in the TNT
Ruth 3 in the TNTIK
Ruth 3 in the TNTIL
Ruth 3 in the TNTIN
Ruth 3 in the TNTIP
Ruth 3 in the TNTIZ
Ruth 3 in the TOMA
Ruth 3 in the TTENT
Ruth 3 in the UBG
Ruth 3 in the UGV
Ruth 3 in the UGV2
Ruth 3 in the UGV3
Ruth 3 in the VBL
Ruth 3 in the VDCC
Ruth 3 in the YALU
Ruth 3 in the YAPE
Ruth 3 in the YBVTP
Ruth 3 in the ZBP