Titus 1 (BOGWICC)
1 Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu 2 ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe. 3 Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu. 4 Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse:Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu. 5 Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira. 6 Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera. 7 Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo. 8 Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo. 9 Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho. 10 Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. 11 Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo. 12 Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.” 13 Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona, 14 kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi. 15 Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa. 16 Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.
In Other Versions
Titus 1 in the ANGEFD
Titus 1 in the ANTPNG2D
Titus 1 in the AS21
Titus 1 in the BAGH
Titus 1 in the BBPNG
Titus 1 in the BBT1E
Titus 1 in the BDS
Titus 1 in the BEV
Titus 1 in the BHAD
Titus 1 in the BIB
Titus 1 in the BLPT
Titus 1 in the BNT
Titus 1 in the BNTABOOT
Titus 1 in the BNTLV
Titus 1 in the BOATCB
Titus 1 in the BOATCB2
Titus 1 in the BOBCV
Titus 1 in the BOCNT
Titus 1 in the BOECS
Titus 1 in the BOHCB
Titus 1 in the BOHCV
Titus 1 in the BOHLNT
Titus 1 in the BOHNTLTAL
Titus 1 in the BOICB
Titus 1 in the BOILNTAP
Titus 1 in the BOITCV
Titus 1 in the BOKCV
Titus 1 in the BOKCV2
Titus 1 in the BOKHWOG
Titus 1 in the BOKSSV
Titus 1 in the BOLCB
Titus 1 in the BOLCB2
Titus 1 in the BOMCV
Titus 1 in the BONAV
Titus 1 in the BONCB
Titus 1 in the BONLT
Titus 1 in the BONUT2
Titus 1 in the BOPLNT
Titus 1 in the BOSCB
Titus 1 in the BOSNC
Titus 1 in the BOTLNT
Titus 1 in the BOVCB
Titus 1 in the BOYCB
Titus 1 in the BPBB
Titus 1 in the BPH
Titus 1 in the BSB
Titus 1 in the CCB
Titus 1 in the CUV
Titus 1 in the CUVS
Titus 1 in the DBT
Titus 1 in the DGDNT
Titus 1 in the DHNT
Titus 1 in the DNT
Titus 1 in the ELBE
Titus 1 in the EMTV
Titus 1 in the ESV
Titus 1 in the FBV
Titus 1 in the FEB
Titus 1 in the GGMNT
Titus 1 in the GNT
Titus 1 in the HARY
Titus 1 in the HNT
Titus 1 in the IRVA
Titus 1 in the IRVB
Titus 1 in the IRVG
Titus 1 in the IRVH
Titus 1 in the IRVK
Titus 1 in the IRVM
Titus 1 in the IRVM2
Titus 1 in the IRVO
Titus 1 in the IRVP
Titus 1 in the IRVT
Titus 1 in the IRVT2
Titus 1 in the IRVU
Titus 1 in the ISVN
Titus 1 in the JSNT
Titus 1 in the KAPI
Titus 1 in the KBT1ETNIK
Titus 1 in the KBV
Titus 1 in the KJV
Titus 1 in the KNFD
Titus 1 in the LBA
Titus 1 in the LBLA
Titus 1 in the LNT
Titus 1 in the LSV
Titus 1 in the MAAL
Titus 1 in the MBV
Titus 1 in the MBV2
Titus 1 in the MHNT
Titus 1 in the MKNFD
Titus 1 in the MNG
Titus 1 in the MNT
Titus 1 in the MNT2
Titus 1 in the MRS1T
Titus 1 in the NAA
Titus 1 in the NASB
Titus 1 in the NBLA
Titus 1 in the NBS
Titus 1 in the NBVTP
Titus 1 in the NET2
Titus 1 in the NIV11
Titus 1 in the NNT
Titus 1 in the NNT2
Titus 1 in the NNT3
Titus 1 in the PDDPT
Titus 1 in the PFNT
Titus 1 in the RMNT
Titus 1 in the SBIAS
Titus 1 in the SBIBS
Titus 1 in the SBIBS2
Titus 1 in the SBICS
Titus 1 in the SBIDS
Titus 1 in the SBIGS
Titus 1 in the SBIHS
Titus 1 in the SBIIS
Titus 1 in the SBIIS2
Titus 1 in the SBIIS3
Titus 1 in the SBIKS
Titus 1 in the SBIKS2
Titus 1 in the SBIMS
Titus 1 in the SBIOS
Titus 1 in the SBIPS
Titus 1 in the SBISS
Titus 1 in the SBITS
Titus 1 in the SBITS2
Titus 1 in the SBITS3
Titus 1 in the SBITS4
Titus 1 in the SBIUS
Titus 1 in the SBIVS
Titus 1 in the SBT
Titus 1 in the SBT1E
Titus 1 in the SCHL
Titus 1 in the SNT
Titus 1 in the SUSU
Titus 1 in the SUSU2
Titus 1 in the SYNO
Titus 1 in the TBIAOTANT
Titus 1 in the TBT1E
Titus 1 in the TBT1E2
Titus 1 in the TFTIP
Titus 1 in the TFTU
Titus 1 in the TGNTATF3T
Titus 1 in the THAI
Titus 1 in the TNFD
Titus 1 in the TNT
Titus 1 in the TNTIK
Titus 1 in the TNTIL
Titus 1 in the TNTIN
Titus 1 in the TNTIP
Titus 1 in the TNTIZ
Titus 1 in the TOMA
Titus 1 in the TTENT
Titus 1 in the UBG
Titus 1 in the UGV
Titus 1 in the UGV2
Titus 1 in the UGV3
Titus 1 in the VBL
Titus 1 in the VDCC
Titus 1 in the YALU
Titus 1 in the YAPE
Titus 1 in the YBVTP
Titus 1 in the ZBP