1 Chronicles 16 (BOGWICC)

1 Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu. 2 Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova. 3 Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma. 4 Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli. 5 Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga, 6 ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu. 7 Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova: 8 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu. 9 Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa. 10 Nyadirani dzina lake loyera;ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova. 11 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;funafunani nkhope yake nthawi zonse. 12 Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita,zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake, 13 inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake,inu ana a Yakobo, osankhidwa ake. 14 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi. 15 Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse,mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda, 16 pangano limene anachita ndi Abrahamu,lonjezo limene analumbira kwa Isake. 17 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo,kwa Israeli monga pangano lamuyaya. 18 “Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaanimonga cholowa chimene udzachilandira.” 19 Ali anthu owerengeka,ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo, 20 iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,ku ufumu wina kupita ku ufumu wina. 21 Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze;chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu: 22 “Musakhudze odzozedwa anga;musawachitire choyipa aneneri anga.” 23 Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi;lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. 24 Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse,ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse. 25 Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda;Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse. 26 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake,koma Yehova analenga kumwamba. 27 Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake;mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye. 28 Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina,perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu, 29 perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake.Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake;pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake. 30 Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi!Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe. 31 Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere;anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!” 32 Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo! 33 Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba,idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova,pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi. 34 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino;chikondi chake chikhala mpaka muyaya. 35 Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina,kuti tiyamike dzina lanu loyera,kuti tikutamandeni.” 36 Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli,kuyambira muyaya mpaka muyaya.Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.” 37 Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse. 38 Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata. 39 Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni 40 kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli. 41 Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.” 42 Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata. 43 Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.

In Other Versions

1 Chronicles 16 in the ANGEFD

1 Chronicles 16 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 16 in the AS21

1 Chronicles 16 in the BAGH

1 Chronicles 16 in the BBPNG

1 Chronicles 16 in the BBT1E

1 Chronicles 16 in the BDS

1 Chronicles 16 in the BEV

1 Chronicles 16 in the BHAD

1 Chronicles 16 in the BIB

1 Chronicles 16 in the BLPT

1 Chronicles 16 in the BNT

1 Chronicles 16 in the BNTABOOT

1 Chronicles 16 in the BNTLV

1 Chronicles 16 in the BOATCB

1 Chronicles 16 in the BOATCB2

1 Chronicles 16 in the BOBCV

1 Chronicles 16 in the BOCNT

1 Chronicles 16 in the BOECS

1 Chronicles 16 in the BOHCB

1 Chronicles 16 in the BOHCV

1 Chronicles 16 in the BOHLNT

1 Chronicles 16 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 16 in the BOICB

1 Chronicles 16 in the BOILNTAP

1 Chronicles 16 in the BOITCV

1 Chronicles 16 in the BOKCV

1 Chronicles 16 in the BOKCV2

1 Chronicles 16 in the BOKHWOG

1 Chronicles 16 in the BOKSSV

1 Chronicles 16 in the BOLCB

1 Chronicles 16 in the BOLCB2

1 Chronicles 16 in the BOMCV

1 Chronicles 16 in the BONAV

1 Chronicles 16 in the BONCB

1 Chronicles 16 in the BONLT

1 Chronicles 16 in the BONUT2

1 Chronicles 16 in the BOPLNT

1 Chronicles 16 in the BOSCB

1 Chronicles 16 in the BOSNC

1 Chronicles 16 in the BOTLNT

1 Chronicles 16 in the BOVCB

1 Chronicles 16 in the BOYCB

1 Chronicles 16 in the BPBB

1 Chronicles 16 in the BPH

1 Chronicles 16 in the BSB

1 Chronicles 16 in the CCB

1 Chronicles 16 in the CUV

1 Chronicles 16 in the CUVS

1 Chronicles 16 in the DBT

1 Chronicles 16 in the DGDNT

1 Chronicles 16 in the DHNT

1 Chronicles 16 in the DNT

1 Chronicles 16 in the ELBE

1 Chronicles 16 in the EMTV

1 Chronicles 16 in the ESV

1 Chronicles 16 in the FBV

1 Chronicles 16 in the FEB

1 Chronicles 16 in the GGMNT

1 Chronicles 16 in the GNT

1 Chronicles 16 in the HARY

1 Chronicles 16 in the HNT

1 Chronicles 16 in the IRVA

1 Chronicles 16 in the IRVB

1 Chronicles 16 in the IRVG

1 Chronicles 16 in the IRVH

1 Chronicles 16 in the IRVK

1 Chronicles 16 in the IRVM

1 Chronicles 16 in the IRVM2

1 Chronicles 16 in the IRVO

1 Chronicles 16 in the IRVP

1 Chronicles 16 in the IRVT

1 Chronicles 16 in the IRVT2

1 Chronicles 16 in the IRVU

1 Chronicles 16 in the ISVN

1 Chronicles 16 in the JSNT

1 Chronicles 16 in the KAPI

1 Chronicles 16 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 16 in the KBV

1 Chronicles 16 in the KJV

1 Chronicles 16 in the KNFD

1 Chronicles 16 in the LBA

1 Chronicles 16 in the LBLA

1 Chronicles 16 in the LNT

1 Chronicles 16 in the LSV

1 Chronicles 16 in the MAAL

1 Chronicles 16 in the MBV

1 Chronicles 16 in the MBV2

1 Chronicles 16 in the MHNT

1 Chronicles 16 in the MKNFD

1 Chronicles 16 in the MNG

1 Chronicles 16 in the MNT

1 Chronicles 16 in the MNT2

1 Chronicles 16 in the MRS1T

1 Chronicles 16 in the NAA

1 Chronicles 16 in the NASB

1 Chronicles 16 in the NBLA

1 Chronicles 16 in the NBS

1 Chronicles 16 in the NBVTP

1 Chronicles 16 in the NET2

1 Chronicles 16 in the NIV11

1 Chronicles 16 in the NNT

1 Chronicles 16 in the NNT2

1 Chronicles 16 in the NNT3

1 Chronicles 16 in the PDDPT

1 Chronicles 16 in the PFNT

1 Chronicles 16 in the RMNT

1 Chronicles 16 in the SBIAS

1 Chronicles 16 in the SBIBS

1 Chronicles 16 in the SBIBS2

1 Chronicles 16 in the SBICS

1 Chronicles 16 in the SBIDS

1 Chronicles 16 in the SBIGS

1 Chronicles 16 in the SBIHS

1 Chronicles 16 in the SBIIS

1 Chronicles 16 in the SBIIS2

1 Chronicles 16 in the SBIIS3

1 Chronicles 16 in the SBIKS

1 Chronicles 16 in the SBIKS2

1 Chronicles 16 in the SBIMS

1 Chronicles 16 in the SBIOS

1 Chronicles 16 in the SBIPS

1 Chronicles 16 in the SBISS

1 Chronicles 16 in the SBITS

1 Chronicles 16 in the SBITS2

1 Chronicles 16 in the SBITS3

1 Chronicles 16 in the SBITS4

1 Chronicles 16 in the SBIUS

1 Chronicles 16 in the SBIVS

1 Chronicles 16 in the SBT

1 Chronicles 16 in the SBT1E

1 Chronicles 16 in the SCHL

1 Chronicles 16 in the SNT

1 Chronicles 16 in the SUSU

1 Chronicles 16 in the SUSU2

1 Chronicles 16 in the SYNO

1 Chronicles 16 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 16 in the TBT1E

1 Chronicles 16 in the TBT1E2

1 Chronicles 16 in the TFTIP

1 Chronicles 16 in the TFTU

1 Chronicles 16 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 16 in the THAI

1 Chronicles 16 in the TNFD

1 Chronicles 16 in the TNT

1 Chronicles 16 in the TNTIK

1 Chronicles 16 in the TNTIL

1 Chronicles 16 in the TNTIN

1 Chronicles 16 in the TNTIP

1 Chronicles 16 in the TNTIZ

1 Chronicles 16 in the TOMA

1 Chronicles 16 in the TTENT

1 Chronicles 16 in the UBG

1 Chronicles 16 in the UGV

1 Chronicles 16 in the UGV2

1 Chronicles 16 in the UGV3

1 Chronicles 16 in the VBL

1 Chronicles 16 in the VDCC

1 Chronicles 16 in the YALU

1 Chronicles 16 in the YAPE

1 Chronicles 16 in the YBVTP

1 Chronicles 16 in the ZBP