1 Peter 4 (BOGWICC)
1 Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo. 2 Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. 3 Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. 4 Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe. 5 Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. 6 Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu. 7 Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera. 8 Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri. 9 Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika. 10 Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu. 11 Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni. 12 Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. 13 Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. 14 Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu. 15 Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena, 16 koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo. 17 Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani? 18 Monga Malemba akuti,“Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke,nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?” 19 Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.
In Other Versions
1 Peter 4 in the ANGEFD
1 Peter 4 in the ANTPNG2D
1 Peter 4 in the AS21
1 Peter 4 in the BAGH
1 Peter 4 in the BBPNG
1 Peter 4 in the BBT1E
1 Peter 4 in the BDS
1 Peter 4 in the BEV
1 Peter 4 in the BHAD
1 Peter 4 in the BIB
1 Peter 4 in the BLPT
1 Peter 4 in the BNT
1 Peter 4 in the BNTABOOT
1 Peter 4 in the BNTLV
1 Peter 4 in the BOATCB
1 Peter 4 in the BOATCB2
1 Peter 4 in the BOBCV
1 Peter 4 in the BOCNT
1 Peter 4 in the BOECS
1 Peter 4 in the BOHCB
1 Peter 4 in the BOHCV
1 Peter 4 in the BOHLNT
1 Peter 4 in the BOHNTLTAL
1 Peter 4 in the BOICB
1 Peter 4 in the BOILNTAP
1 Peter 4 in the BOITCV
1 Peter 4 in the BOKCV
1 Peter 4 in the BOKCV2
1 Peter 4 in the BOKHWOG
1 Peter 4 in the BOKSSV
1 Peter 4 in the BOLCB
1 Peter 4 in the BOLCB2
1 Peter 4 in the BOMCV
1 Peter 4 in the BONAV
1 Peter 4 in the BONCB
1 Peter 4 in the BONLT
1 Peter 4 in the BONUT2
1 Peter 4 in the BOPLNT
1 Peter 4 in the BOSCB
1 Peter 4 in the BOSNC
1 Peter 4 in the BOTLNT
1 Peter 4 in the BOVCB
1 Peter 4 in the BOYCB
1 Peter 4 in the BPBB
1 Peter 4 in the BPH
1 Peter 4 in the BSB
1 Peter 4 in the CCB
1 Peter 4 in the CUV
1 Peter 4 in the CUVS
1 Peter 4 in the DBT
1 Peter 4 in the DGDNT
1 Peter 4 in the DHNT
1 Peter 4 in the DNT
1 Peter 4 in the ELBE
1 Peter 4 in the EMTV
1 Peter 4 in the ESV
1 Peter 4 in the FBV
1 Peter 4 in the FEB
1 Peter 4 in the GGMNT
1 Peter 4 in the GNT
1 Peter 4 in the HARY
1 Peter 4 in the HNT
1 Peter 4 in the IRVA
1 Peter 4 in the IRVB
1 Peter 4 in the IRVG
1 Peter 4 in the IRVH
1 Peter 4 in the IRVK
1 Peter 4 in the IRVM
1 Peter 4 in the IRVM2
1 Peter 4 in the IRVO
1 Peter 4 in the IRVP
1 Peter 4 in the IRVT
1 Peter 4 in the IRVT2
1 Peter 4 in the IRVU
1 Peter 4 in the ISVN
1 Peter 4 in the JSNT
1 Peter 4 in the KAPI
1 Peter 4 in the KBT1ETNIK
1 Peter 4 in the KBV
1 Peter 4 in the KJV
1 Peter 4 in the KNFD
1 Peter 4 in the LBA
1 Peter 4 in the LBLA
1 Peter 4 in the LNT
1 Peter 4 in the LSV
1 Peter 4 in the MAAL
1 Peter 4 in the MBV
1 Peter 4 in the MBV2
1 Peter 4 in the MHNT
1 Peter 4 in the MKNFD
1 Peter 4 in the MNG
1 Peter 4 in the MNT
1 Peter 4 in the MNT2
1 Peter 4 in the MRS1T
1 Peter 4 in the NAA
1 Peter 4 in the NASB
1 Peter 4 in the NBLA
1 Peter 4 in the NBS
1 Peter 4 in the NBVTP
1 Peter 4 in the NET2
1 Peter 4 in the NIV11
1 Peter 4 in the NNT
1 Peter 4 in the NNT2
1 Peter 4 in the NNT3
1 Peter 4 in the PDDPT
1 Peter 4 in the PFNT
1 Peter 4 in the RMNT
1 Peter 4 in the SBIAS
1 Peter 4 in the SBIBS
1 Peter 4 in the SBIBS2
1 Peter 4 in the SBICS
1 Peter 4 in the SBIDS
1 Peter 4 in the SBIGS
1 Peter 4 in the SBIHS
1 Peter 4 in the SBIIS
1 Peter 4 in the SBIIS2
1 Peter 4 in the SBIIS3
1 Peter 4 in the SBIKS
1 Peter 4 in the SBIKS2
1 Peter 4 in the SBIMS
1 Peter 4 in the SBIOS
1 Peter 4 in the SBIPS
1 Peter 4 in the SBISS
1 Peter 4 in the SBITS
1 Peter 4 in the SBITS2
1 Peter 4 in the SBITS3
1 Peter 4 in the SBITS4
1 Peter 4 in the SBIUS
1 Peter 4 in the SBIVS
1 Peter 4 in the SBT
1 Peter 4 in the SBT1E
1 Peter 4 in the SCHL
1 Peter 4 in the SNT
1 Peter 4 in the SUSU
1 Peter 4 in the SUSU2
1 Peter 4 in the SYNO
1 Peter 4 in the TBIAOTANT
1 Peter 4 in the TBT1E
1 Peter 4 in the TBT1E2
1 Peter 4 in the TFTIP
1 Peter 4 in the TFTU
1 Peter 4 in the TGNTATF3T
1 Peter 4 in the THAI
1 Peter 4 in the TNFD
1 Peter 4 in the TNT
1 Peter 4 in the TNTIK
1 Peter 4 in the TNTIL
1 Peter 4 in the TNTIN
1 Peter 4 in the TNTIP
1 Peter 4 in the TNTIZ
1 Peter 4 in the TOMA
1 Peter 4 in the TTENT
1 Peter 4 in the UBG
1 Peter 4 in the UGV
1 Peter 4 in the UGV2
1 Peter 4 in the UGV3
1 Peter 4 in the VBL
1 Peter 4 in the VDCC
1 Peter 4 in the YALU
1 Peter 4 in the YAPE
1 Peter 4 in the YBVTP
1 Peter 4 in the ZBP