1 Samuel 12 (BOGWICC)

1 Pambuyo pake Samueli anawuza Aisraeli onse kuti, “Ine ndamvera zonse zimene munandiwuza ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. 2 Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero. 3 Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.” 4 Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.” 5 Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.”Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.” 6 Samueli anawawuzanso kuti, “Yehova ndiye amene anasankha Mose ndi Aaroni kuti atulutse makolo anu mʼdziko la Igupto. 7 Nʼchifukwa chake tsopano imani pomwepa kuti ndikufotokozereni pamaso pa Yehova, za ntchito za chipulumutso zimene Yehova anachitira inu ndi makolo anu. 8 “Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano. 9 “Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu. 10 Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’ 11 Choncho Yehova anatumiza Yeru-Baala, Bedani, Yefita ndi Samueli ndipo anakulanditsani mʼmanja mwa adani anu amene anakuzungulirani, kotero munakhala mwamtendere. 12 “Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu. 13 Tsopano nayi mfumu imene mwayisankha, imene munayipempha. Onani, Yehova wakupatsani mfumu. 14 Ngati muziopa Yehova ndi kumamutumikira ndi kumamumvera, osamupandukira ndiponso ngati inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Yehova Mulungu wanu, ndiye zinthu zonse zidzakuyenderani bwino. 15 Koma mukapanda kumvera Yehova ndi kumupandukira, ndiye adzakulangani pamodzi ndi mfumu yanu yomwe. 16 “Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu! 17 Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.” 18 Choncho Samueli anapemphera, ndipo Yehova anatumiza mvula ya mabingu tsiku lomwelo. Apo anthu aja anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli. 19 Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.” 20 Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse. 21 Ndipo musatsate mafano achabechabe amene alibe phindu ndipo sangakupulumutseni popeza ndi achabechabe. 22 Yehova adzakana anthu ake kuopa kuti dzina lake lamphamvu linganyozeke, pakuti chinamukondweretsa Yehova kuti akusandutseni inu kukhala anthu ake. 23 Ndiponso kunena za ine, zisachitike kuti ndichimwire Yehova pakulephera kukupemphererani. Ndipo ine ndidzakuphunzitsani njira yabwino ndi yolungama kuti muziyendamo. 24 Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani. 25 Komabe mukapitirira kuchita zoyipa, ndiye kuti inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzachotsedwa.”

In Other Versions

1 Samuel 12 in the ANGEFD

1 Samuel 12 in the ANTPNG2D

1 Samuel 12 in the AS21

1 Samuel 12 in the BAGH

1 Samuel 12 in the BBPNG

1 Samuel 12 in the BBT1E

1 Samuel 12 in the BDS

1 Samuel 12 in the BEV

1 Samuel 12 in the BHAD

1 Samuel 12 in the BIB

1 Samuel 12 in the BLPT

1 Samuel 12 in the BNT

1 Samuel 12 in the BNTABOOT

1 Samuel 12 in the BNTLV

1 Samuel 12 in the BOATCB

1 Samuel 12 in the BOATCB2

1 Samuel 12 in the BOBCV

1 Samuel 12 in the BOCNT

1 Samuel 12 in the BOECS

1 Samuel 12 in the BOHCB

1 Samuel 12 in the BOHCV

1 Samuel 12 in the BOHLNT

1 Samuel 12 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 12 in the BOICB

1 Samuel 12 in the BOILNTAP

1 Samuel 12 in the BOITCV

1 Samuel 12 in the BOKCV

1 Samuel 12 in the BOKCV2

1 Samuel 12 in the BOKHWOG

1 Samuel 12 in the BOKSSV

1 Samuel 12 in the BOLCB

1 Samuel 12 in the BOLCB2

1 Samuel 12 in the BOMCV

1 Samuel 12 in the BONAV

1 Samuel 12 in the BONCB

1 Samuel 12 in the BONLT

1 Samuel 12 in the BONUT2

1 Samuel 12 in the BOPLNT

1 Samuel 12 in the BOSCB

1 Samuel 12 in the BOSNC

1 Samuel 12 in the BOTLNT

1 Samuel 12 in the BOVCB

1 Samuel 12 in the BOYCB

1 Samuel 12 in the BPBB

1 Samuel 12 in the BPH

1 Samuel 12 in the BSB

1 Samuel 12 in the CCB

1 Samuel 12 in the CUV

1 Samuel 12 in the CUVS

1 Samuel 12 in the DBT

1 Samuel 12 in the DGDNT

1 Samuel 12 in the DHNT

1 Samuel 12 in the DNT

1 Samuel 12 in the ELBE

1 Samuel 12 in the EMTV

1 Samuel 12 in the ESV

1 Samuel 12 in the FBV

1 Samuel 12 in the FEB

1 Samuel 12 in the GGMNT

1 Samuel 12 in the GNT

1 Samuel 12 in the HARY

1 Samuel 12 in the HNT

1 Samuel 12 in the IRVA

1 Samuel 12 in the IRVB

1 Samuel 12 in the IRVG

1 Samuel 12 in the IRVH

1 Samuel 12 in the IRVK

1 Samuel 12 in the IRVM

1 Samuel 12 in the IRVM2

1 Samuel 12 in the IRVO

1 Samuel 12 in the IRVP

1 Samuel 12 in the IRVT

1 Samuel 12 in the IRVT2

1 Samuel 12 in the IRVU

1 Samuel 12 in the ISVN

1 Samuel 12 in the JSNT

1 Samuel 12 in the KAPI

1 Samuel 12 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 12 in the KBV

1 Samuel 12 in the KJV

1 Samuel 12 in the KNFD

1 Samuel 12 in the LBA

1 Samuel 12 in the LBLA

1 Samuel 12 in the LNT

1 Samuel 12 in the LSV

1 Samuel 12 in the MAAL

1 Samuel 12 in the MBV

1 Samuel 12 in the MBV2

1 Samuel 12 in the MHNT

1 Samuel 12 in the MKNFD

1 Samuel 12 in the MNG

1 Samuel 12 in the MNT

1 Samuel 12 in the MNT2

1 Samuel 12 in the MRS1T

1 Samuel 12 in the NAA

1 Samuel 12 in the NASB

1 Samuel 12 in the NBLA

1 Samuel 12 in the NBS

1 Samuel 12 in the NBVTP

1 Samuel 12 in the NET2

1 Samuel 12 in the NIV11

1 Samuel 12 in the NNT

1 Samuel 12 in the NNT2

1 Samuel 12 in the NNT3

1 Samuel 12 in the PDDPT

1 Samuel 12 in the PFNT

1 Samuel 12 in the RMNT

1 Samuel 12 in the SBIAS

1 Samuel 12 in the SBIBS

1 Samuel 12 in the SBIBS2

1 Samuel 12 in the SBICS

1 Samuel 12 in the SBIDS

1 Samuel 12 in the SBIGS

1 Samuel 12 in the SBIHS

1 Samuel 12 in the SBIIS

1 Samuel 12 in the SBIIS2

1 Samuel 12 in the SBIIS3

1 Samuel 12 in the SBIKS

1 Samuel 12 in the SBIKS2

1 Samuel 12 in the SBIMS

1 Samuel 12 in the SBIOS

1 Samuel 12 in the SBIPS

1 Samuel 12 in the SBISS

1 Samuel 12 in the SBITS

1 Samuel 12 in the SBITS2

1 Samuel 12 in the SBITS3

1 Samuel 12 in the SBITS4

1 Samuel 12 in the SBIUS

1 Samuel 12 in the SBIVS

1 Samuel 12 in the SBT

1 Samuel 12 in the SBT1E

1 Samuel 12 in the SCHL

1 Samuel 12 in the SNT

1 Samuel 12 in the SUSU

1 Samuel 12 in the SUSU2

1 Samuel 12 in the SYNO

1 Samuel 12 in the TBIAOTANT

1 Samuel 12 in the TBT1E

1 Samuel 12 in the TBT1E2

1 Samuel 12 in the TFTIP

1 Samuel 12 in the TFTU

1 Samuel 12 in the TGNTATF3T

1 Samuel 12 in the THAI

1 Samuel 12 in the TNFD

1 Samuel 12 in the TNT

1 Samuel 12 in the TNTIK

1 Samuel 12 in the TNTIL

1 Samuel 12 in the TNTIN

1 Samuel 12 in the TNTIP

1 Samuel 12 in the TNTIZ

1 Samuel 12 in the TOMA

1 Samuel 12 in the TTENT

1 Samuel 12 in the UBG

1 Samuel 12 in the UGV

1 Samuel 12 in the UGV2

1 Samuel 12 in the UGV3

1 Samuel 12 in the VBL

1 Samuel 12 in the VDCC

1 Samuel 12 in the YALU

1 Samuel 12 in the YAPE

1 Samuel 12 in the YBVTP

1 Samuel 12 in the ZBP