Acts 15 (BOGWICC)

1 Anthu ena ochokera ku Yudeya anafika ku Antiokeya ndipo amaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuchita mdulidwe potsata mwambo wa Mose, simungapulumuke.” 2 Zimenezi zinachititsa Paulo ndi Barnaba kuti atsutsane nawo kwambiri. Kotero Paulo ndi Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi abale ena kuti apite ku Yerusalemu kukaonana ndi atumwi ndi akulu ampingo kukakambirana za nkhaniyi. 3 Mpingo unawaperekeza, ndipo pamene amadutsa ku Foinike ndi Samariya, iwo anafotokoza momwe a mitundu ina anatembenukira mtima. Nkhani imeneyi inakondweretsa kwambiri abale onse. 4 Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo. 5 Kenaka, okhulupirira ena amene kale anali a gulu la Afarisi anayimirira ndipo anati, “Anthu a mitundu ina ayenera kuchita mdulidwe ndi kusunga malamulo a Mose.” 6 Atumwi ndi akulu ampingo anasonkhana kuti akambirane za nkhaniyi. 7 Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira. 8 Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse pakati pa ife ndi iwo, pakuti anayeretsa mitima yawo mwachikhulupiriro. 10 Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza? 11 Osatero! Ife tikukhulupirira kuti tinapulumutsidwa mwachisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, monga iwonso anachitira.” 12 Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo. 13 Iwo atatha kuyankhula, Yakobo anayankhula nati: “Abale, tandimverani. 14 Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake. 15 Mawu a aneneri akuvomereza zimenezi, monga kwalembedwa kuti, 16 “ ‘Zitatha izi Ine ndidzabwererandipo ndidzamanganso nyumba ya Davide imene inagwa.Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,ndi kuyimanganso, 17 kuti anthu otsalawo afunefune Ambuye,ndi anthu onse a mitundu ina amene atchedwa ndi dzina langa,akutero Ambuye, amene amachita zinthu zimenezi 18 zinaululidwa kuyambira kalekale.’ 19 “Chifukwa chake, ine ndikuweruza kuti tisamavute anthu a mitundu ina amene atembenuka mtima kutsata Mulungu. 20 Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi. 21 Pakuti malamulo a Mose akhala akulalikidwa mu mzinda uliwonse, kuyambira kalekale ndipo amawerengedwa mʼMasunagoge tsiku la Sabata.” 22 Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale, 23 kuti akapereke kalata yonena kuti,Kuchokera kwa atumwi ndi akulu ampingo, abale anu,Kwa anthu a mitundu ina okhulupirira a ku Antiokeya, Siriya ndi Kilikiya:Tikupereka moni. 24 Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani. 25 Tsono ife tagwirizana kuti, tisankhe anthu ena ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa Paulo ndi Barnaba, 26 anthu amene anapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye athu Yesu Khristu. 27 Nʼchifukwa chake, tikutumiza Yudasi ndi Sila kuti adzachitire umboni ndi mawu a pakamwa pawo za zimene ife talemba. 28 Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi: 29 Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi. Tsalani bwino. 30 Anthu aja anatumidwa ndipo anafika ku Antiokeya, kumene anasonkhanitsa mpingo pamodzi napereka kalatayo. 31 Anthuwo anawerenga kalatayo ndipo abalewo anakondwa chifukwa cha mawu ake achirimbikitso. 32 Yudasi ndi Sila amene analinso aneneri, ananena zambiri zowalimbikitsa ndi kuwapatsa mphamvu abalewo. 33 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abale aja anatsanzikana nawo mwamtendere kuti abwerere kwa amene anawatuma. 34 Koma Sila anasankha kuti akhale komweko. 35 Koma Paulo ndi Barnaba anatsalira ku Antiokeya kumene iwo pamodzi ndi ena ambiri anaphunzitsa ndi kulalikira Mawu a Ambuye. 36 Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.” 37 Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo. 38 Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito. 39 Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 40 Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka. 41 Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.

In Other Versions

Acts 15 in the ANGEFD

Acts 15 in the ANTPNG2D

Acts 15 in the AS21

Acts 15 in the BAGH

Acts 15 in the BBPNG

Acts 15 in the BBT1E

Acts 15 in the BDS

Acts 15 in the BEV

Acts 15 in the BHAD

Acts 15 in the BIB

Acts 15 in the BLPT

Acts 15 in the BNT

Acts 15 in the BNTABOOT

Acts 15 in the BNTLV

Acts 15 in the BOATCB

Acts 15 in the BOATCB2

Acts 15 in the BOBCV

Acts 15 in the BOCNT

Acts 15 in the BOECS

Acts 15 in the BOHCB

Acts 15 in the BOHCV

Acts 15 in the BOHLNT

Acts 15 in the BOHNTLTAL

Acts 15 in the BOICB

Acts 15 in the BOILNTAP

Acts 15 in the BOITCV

Acts 15 in the BOKCV

Acts 15 in the BOKCV2

Acts 15 in the BOKHWOG

Acts 15 in the BOKSSV

Acts 15 in the BOLCB

Acts 15 in the BOLCB2

Acts 15 in the BOMCV

Acts 15 in the BONAV

Acts 15 in the BONCB

Acts 15 in the BONLT

Acts 15 in the BONUT2

Acts 15 in the BOPLNT

Acts 15 in the BOSCB

Acts 15 in the BOSNC

Acts 15 in the BOTLNT

Acts 15 in the BOVCB

Acts 15 in the BOYCB

Acts 15 in the BPBB

Acts 15 in the BPH

Acts 15 in the BSB

Acts 15 in the CCB

Acts 15 in the CUV

Acts 15 in the CUVS

Acts 15 in the DBT

Acts 15 in the DGDNT

Acts 15 in the DHNT

Acts 15 in the DNT

Acts 15 in the ELBE

Acts 15 in the EMTV

Acts 15 in the ESV

Acts 15 in the FBV

Acts 15 in the FEB

Acts 15 in the GGMNT

Acts 15 in the GNT

Acts 15 in the HARY

Acts 15 in the HNT

Acts 15 in the IRVA

Acts 15 in the IRVB

Acts 15 in the IRVG

Acts 15 in the IRVH

Acts 15 in the IRVK

Acts 15 in the IRVM

Acts 15 in the IRVM2

Acts 15 in the IRVO

Acts 15 in the IRVP

Acts 15 in the IRVT

Acts 15 in the IRVT2

Acts 15 in the IRVU

Acts 15 in the ISVN

Acts 15 in the JSNT

Acts 15 in the KAPI

Acts 15 in the KBT1ETNIK

Acts 15 in the KBV

Acts 15 in the KJV

Acts 15 in the KNFD

Acts 15 in the LBA

Acts 15 in the LBLA

Acts 15 in the LNT

Acts 15 in the LSV

Acts 15 in the MAAL

Acts 15 in the MBV

Acts 15 in the MBV2

Acts 15 in the MHNT

Acts 15 in the MKNFD

Acts 15 in the MNG

Acts 15 in the MNT

Acts 15 in the MNT2

Acts 15 in the MRS1T

Acts 15 in the NAA

Acts 15 in the NASB

Acts 15 in the NBLA

Acts 15 in the NBS

Acts 15 in the NBVTP

Acts 15 in the NET2

Acts 15 in the NIV11

Acts 15 in the NNT

Acts 15 in the NNT2

Acts 15 in the NNT3

Acts 15 in the PDDPT

Acts 15 in the PFNT

Acts 15 in the RMNT

Acts 15 in the SBIAS

Acts 15 in the SBIBS

Acts 15 in the SBIBS2

Acts 15 in the SBICS

Acts 15 in the SBIDS

Acts 15 in the SBIGS

Acts 15 in the SBIHS

Acts 15 in the SBIIS

Acts 15 in the SBIIS2

Acts 15 in the SBIIS3

Acts 15 in the SBIKS

Acts 15 in the SBIKS2

Acts 15 in the SBIMS

Acts 15 in the SBIOS

Acts 15 in the SBIPS

Acts 15 in the SBISS

Acts 15 in the SBITS

Acts 15 in the SBITS2

Acts 15 in the SBITS3

Acts 15 in the SBITS4

Acts 15 in the SBIUS

Acts 15 in the SBIVS

Acts 15 in the SBT

Acts 15 in the SBT1E

Acts 15 in the SCHL

Acts 15 in the SNT

Acts 15 in the SUSU

Acts 15 in the SUSU2

Acts 15 in the SYNO

Acts 15 in the TBIAOTANT

Acts 15 in the TBT1E

Acts 15 in the TBT1E2

Acts 15 in the TFTIP

Acts 15 in the TFTU

Acts 15 in the TGNTATF3T

Acts 15 in the THAI

Acts 15 in the TNFD

Acts 15 in the TNT

Acts 15 in the TNTIK

Acts 15 in the TNTIL

Acts 15 in the TNTIN

Acts 15 in the TNTIP

Acts 15 in the TNTIZ

Acts 15 in the TOMA

Acts 15 in the TTENT

Acts 15 in the UBG

Acts 15 in the UGV

Acts 15 in the UGV2

Acts 15 in the UGV3

Acts 15 in the VBL

Acts 15 in the VDCC

Acts 15 in the YALU

Acts 15 in the YAPE

Acts 15 in the YBVTP

Acts 15 in the ZBP