Acts 28 (BOGWICC)

1 Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita. 2 Anthu a pa chilumbacho anatichitira zokoma zimene sizichitika kawirikawiri. Iwo anakoleza moto natilandira tonse chifukwa kumagwa mvula ndipo kumazizira. 3 Paulo anatola mtolo wankhuni, pamene amayika pa moto, munatulukamo njoka chifukwa cha kutentha, ndipo inamuluma pa dzanja. 4 Anthu a pa chilumbacho ataona njokayo ili lende pa dzanja lake, iwo anawuzana kuti, “Munthu uyu akuyenera kukhala munthu wopha anthu; pakuti ngakhale wapulumuka pa nyanja, chilungamo sichinamulore kuti akhale ndi moyo.” 5 Koma Paulo anayikutumulira pa moto njokayo, ndipo sanamve kupweteka. 6 Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu. 7 Pafupi ndi malowa panali munda wa Popliyo, mkulu wa boma la pa chilumbacho. Iye anatilandira natisamala bwino masiku atatu. 8 Abambo ake anali gone, chifukwa amadwala malungo ndi kamwazi. Paulo analowa mʼchipinda chake kukawaona, ndipo atapemphera, anasanjika manja ake pa iwo nawachiritsa. 9 Zitachitika zimenezi, anthu onse odwala a pa chilumbacho anabwera ndipo anachiritsidwa. 10 Anthuwo anatilemekeza ife mʼnjira zambiri ndipo pamene tinakonzeka kuti tiyambe ulendo, anatipatsa zonse zomwe tinazisowa. 11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pa sitima ina imene inakhala pa chilumbacho chifukwa cha kuzizira. Inali sitima ya ku Alekisandriya imene inali ndi chizindikiro cha milungu ya mapasa yotchedwa Kastro ndi Polikisi. 12 Tinakafika ku Surakusa ndipo kumeneko tinakhalako masiku atatu. 13 Kuchokera kumeneko tinayenda ndi kukafika ku Regio. Mmawa mwake mphepo yochokera kummwera inawomba, ndipo tsiku linalo tinakafika ku Potiyolo. 14 Kumeneko tinapezako abale amene anatiyitana kuti tikhale nawo sabata limodzi. Ndipo kenaka tinapita ku Roma. 15 Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa. 16 Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kukhala pa yekha ndi msilikali womulondera. 17 Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa pamodzi atsogoleri a Ayuda. Atasonkhana, Paulo anawawuza kuti, “Abale anga, ngakhale kuti ine sindinachite kanthu kalikonse kulakwira mtundu wathu kapena miyambo ya makolo athu, koma anandigwira mu Yerusalemu ndi kundipereka mʼmanja mwa Aroma. 18 Iwo anandifufuza ndipo anafuna kundimasula chifukwa sanandipeze wopalamula mlandu woyenera kuphedwa. 19 Koma Ayuda atakana, ine ndinakakamizidwa kupempha kuti ndikaonekere pamaso pa Kaisara, sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga. 20 Pa chifukwa ichi ndapempha kuti ndionane nanu ndi kuyankhula nanu. Pakuti nʼchifukwa cha chiyembekezo cha Israeli ndamangidwa unyolo uwu.” 21 Iwo anayankha kuti, “Ife sitinalandire kalata iliyonse yochokera ku Yudeya yonena za iwe, ndipo palibe mmodzi wa abale amene anachokera kumeneko anafotokoza kapena kunena kalikonse koyipa ka iwe. 22 Koma ife tikufuna kumva maganizo ako ndi otani, pakuti tikudziwa kuti ponseponse anthu akuyankhula zotsutsana ndi mpatuko umenewu.” 23 Iwo anakonza tsiku lina loti akumane ndi Paulo, ndipo anabwera anthu ambiri ku nyumba kumene amakhala. Kuyambira mmawa mpaka madzulo, Paulo anawafotokozera ndi kuwawuza za ufumu wa Mulungu ndipo anayesa kuwakopa kuti akhulupirire Yesu kuchokera mʼMalamulo a Mose ndiponso mʼmabuku a Aneneri. 24 Ena anakopeka ndi zimene Paulo ananena, koma enanso sanakhulupirire. 25 Ndipo anayamba kuchoka popeza sanagwirizane pakati pawo Paulo atanena mawu awa omaliza akuti, “Mzimu Woyera anayankhula zoona za makolo anu pamene Iye ananena kudzera mwa Mneneri Yesaya kuti, 26 “Pita kwa anthu awa ndi kuwawuza kuti,‘Kumva mudzamva, koma osamvetsetsa;kupenya mudzapenya, koma osaona kanthu.’ 27 Pakuti mtima wa anthu ndi wokanika;mʼmakutu mwawo ndi mogontha,ndipo atsinzina kuti asaone kanthu.Mwina angapenye ndi maso awo,angamve ndi makutu awo,angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,Ineyo nʼkuwachiritsa. 28 “Chifukwa chake ine ndikufuna mudziwe kuti chipulumutso cha Mulungu chatumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzamvera.” 29 Paulo atanena mawu amenewa, Ayuda aja anachoka akutsutsana kwambiri. 30 Paulo anakhala kumeneko zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yobwereka yomwe amalipira ndipo ankalandira aliyense amene amabwera kudzamuona. 31 Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.

In Other Versions

Acts 28 in the ANGEFD

Acts 28 in the ANTPNG2D

Acts 28 in the AS21

Acts 28 in the BAGH

Acts 28 in the BBPNG

Acts 28 in the BBT1E

Acts 28 in the BDS

Acts 28 in the BEV

Acts 28 in the BHAD

Acts 28 in the BIB

Acts 28 in the BLPT

Acts 28 in the BNT

Acts 28 in the BNTABOOT

Acts 28 in the BNTLV

Acts 28 in the BOATCB

Acts 28 in the BOATCB2

Acts 28 in the BOBCV

Acts 28 in the BOCNT

Acts 28 in the BOECS

Acts 28 in the BOHCB

Acts 28 in the BOHCV

Acts 28 in the BOHLNT

Acts 28 in the BOHNTLTAL

Acts 28 in the BOICB

Acts 28 in the BOILNTAP

Acts 28 in the BOITCV

Acts 28 in the BOKCV

Acts 28 in the BOKCV2

Acts 28 in the BOKHWOG

Acts 28 in the BOKSSV

Acts 28 in the BOLCB

Acts 28 in the BOLCB2

Acts 28 in the BOMCV

Acts 28 in the BONAV

Acts 28 in the BONCB

Acts 28 in the BONLT

Acts 28 in the BONUT2

Acts 28 in the BOPLNT

Acts 28 in the BOSCB

Acts 28 in the BOSNC

Acts 28 in the BOTLNT

Acts 28 in the BOVCB

Acts 28 in the BOYCB

Acts 28 in the BPBB

Acts 28 in the BPH

Acts 28 in the BSB

Acts 28 in the CCB

Acts 28 in the CUV

Acts 28 in the CUVS

Acts 28 in the DBT

Acts 28 in the DGDNT

Acts 28 in the DHNT

Acts 28 in the DNT

Acts 28 in the ELBE

Acts 28 in the EMTV

Acts 28 in the ESV

Acts 28 in the FBV

Acts 28 in the FEB

Acts 28 in the GGMNT

Acts 28 in the GNT

Acts 28 in the HARY

Acts 28 in the HNT

Acts 28 in the IRVA

Acts 28 in the IRVB

Acts 28 in the IRVG

Acts 28 in the IRVH

Acts 28 in the IRVK

Acts 28 in the IRVM

Acts 28 in the IRVM2

Acts 28 in the IRVO

Acts 28 in the IRVP

Acts 28 in the IRVT

Acts 28 in the IRVT2

Acts 28 in the IRVU

Acts 28 in the ISVN

Acts 28 in the JSNT

Acts 28 in the KAPI

Acts 28 in the KBT1ETNIK

Acts 28 in the KBV

Acts 28 in the KJV

Acts 28 in the KNFD

Acts 28 in the LBA

Acts 28 in the LBLA

Acts 28 in the LNT

Acts 28 in the LSV

Acts 28 in the MAAL

Acts 28 in the MBV

Acts 28 in the MBV2

Acts 28 in the MHNT

Acts 28 in the MKNFD

Acts 28 in the MNG

Acts 28 in the MNT

Acts 28 in the MNT2

Acts 28 in the MRS1T

Acts 28 in the NAA

Acts 28 in the NASB

Acts 28 in the NBLA

Acts 28 in the NBS

Acts 28 in the NBVTP

Acts 28 in the NET2

Acts 28 in the NIV11

Acts 28 in the NNT

Acts 28 in the NNT2

Acts 28 in the NNT3

Acts 28 in the PDDPT

Acts 28 in the PFNT

Acts 28 in the RMNT

Acts 28 in the SBIAS

Acts 28 in the SBIBS

Acts 28 in the SBIBS2

Acts 28 in the SBICS

Acts 28 in the SBIDS

Acts 28 in the SBIGS

Acts 28 in the SBIHS

Acts 28 in the SBIIS

Acts 28 in the SBIIS2

Acts 28 in the SBIIS3

Acts 28 in the SBIKS

Acts 28 in the SBIKS2

Acts 28 in the SBIMS

Acts 28 in the SBIOS

Acts 28 in the SBIPS

Acts 28 in the SBISS

Acts 28 in the SBITS

Acts 28 in the SBITS2

Acts 28 in the SBITS3

Acts 28 in the SBITS4

Acts 28 in the SBIUS

Acts 28 in the SBIVS

Acts 28 in the SBT

Acts 28 in the SBT1E

Acts 28 in the SCHL

Acts 28 in the SNT

Acts 28 in the SUSU

Acts 28 in the SUSU2

Acts 28 in the SYNO

Acts 28 in the TBIAOTANT

Acts 28 in the TBT1E

Acts 28 in the TBT1E2

Acts 28 in the TFTIP

Acts 28 in the TFTU

Acts 28 in the TGNTATF3T

Acts 28 in the THAI

Acts 28 in the TNFD

Acts 28 in the TNT

Acts 28 in the TNTIK

Acts 28 in the TNTIL

Acts 28 in the TNTIN

Acts 28 in the TNTIP

Acts 28 in the TNTIZ

Acts 28 in the TOMA

Acts 28 in the TTENT

Acts 28 in the UBG

Acts 28 in the UGV

Acts 28 in the UGV2

Acts 28 in the UGV3

Acts 28 in the VBL

Acts 28 in the VDCC

Acts 28 in the YALU

Acts 28 in the YAPE

Acts 28 in the YBVTP

Acts 28 in the ZBP