Acts 6 (BOGWICC)

1 Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku. 2 Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya. 3 Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira. 4 Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.” 5 Mawu amenewa anakondweretsa gulu lonse la anthu. Iwo anasankha, Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso Mzimu Woyera; anasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanora, Timo, Parmena ndi Nikolao amene anatembenuka mtima ndi kulowa Chiyuda kuchokera kwa Antiokeya. 6 Iwo anapereka anthuwa kwa atumwi amene anawapempherera ndi kuwasanjika manja. 7 Ndipo Mawu a Mulungu anapitirira kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira mu Yerusalemu chinakula mofulumira ndipo ansembe ochuluka anakhulupirira. 8 Stefano, munthu wodzazidwa ndi chisomo cha Mulungu ndi mphamvu anachita zodabwitsa ndiponso zizindikiro zazikulu pakati pa anthu. 9 Panauka mtsutso kuchokera kwa anthu a ku Kurene ndi a ku Alekisandriya komanso a ku dera la Silisiya ndi Asiya, otchedwa a Sunagoge ya Mfulu. Anthu amenewa anayamba kutsutsana ndi Stefano. 10 Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa. 11 Iwo ananyengerera anthu ena mwamseri kuti anene kuti, “Ife tinamva Stefano akuchitira chipongwe Mose ndiponso Mulungu.” 12 Motero anawutsa mitima ya anthu, akulu ndi aphunzitsi amalamulo. Anamugwira Stefano ndi kumubweretsa ku Bwalo Lalikulu. 13 Iwo anabweretsa mboni zonama zimene zinati, “Munthu uyu akupitirirabe kuyankhula mawu onyoza malo oyera ndi malamulo. 14 Pakuti tinamumva akunena kuti Yesu uja wa ku Nazareti adzawononga malo ano ndiponso kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.” 15 Onse amene anakhala pansi Mʼbwalo Lalikulu anamuyangʼanitsitsa Stefano, ndipo anaona kuti nkhope yake ikuwala ngati ya mngelo.

In Other Versions

Acts 6 in the ANGEFD

Acts 6 in the ANTPNG2D

Acts 6 in the AS21

Acts 6 in the BAGH

Acts 6 in the BBPNG

Acts 6 in the BBT1E

Acts 6 in the BDS

Acts 6 in the BEV

Acts 6 in the BHAD

Acts 6 in the BIB

Acts 6 in the BLPT

Acts 6 in the BNT

Acts 6 in the BNTABOOT

Acts 6 in the BNTLV

Acts 6 in the BOATCB

Acts 6 in the BOATCB2

Acts 6 in the BOBCV

Acts 6 in the BOCNT

Acts 6 in the BOECS

Acts 6 in the BOHCB

Acts 6 in the BOHCV

Acts 6 in the BOHLNT

Acts 6 in the BOHNTLTAL

Acts 6 in the BOICB

Acts 6 in the BOILNTAP

Acts 6 in the BOITCV

Acts 6 in the BOKCV

Acts 6 in the BOKCV2

Acts 6 in the BOKHWOG

Acts 6 in the BOKSSV

Acts 6 in the BOLCB

Acts 6 in the BOLCB2

Acts 6 in the BOMCV

Acts 6 in the BONAV

Acts 6 in the BONCB

Acts 6 in the BONLT

Acts 6 in the BONUT2

Acts 6 in the BOPLNT

Acts 6 in the BOSCB

Acts 6 in the BOSNC

Acts 6 in the BOTLNT

Acts 6 in the BOVCB

Acts 6 in the BOYCB

Acts 6 in the BPBB

Acts 6 in the BPH

Acts 6 in the BSB

Acts 6 in the CCB

Acts 6 in the CUV

Acts 6 in the CUVS

Acts 6 in the DBT

Acts 6 in the DGDNT

Acts 6 in the DHNT

Acts 6 in the DNT

Acts 6 in the ELBE

Acts 6 in the EMTV

Acts 6 in the ESV

Acts 6 in the FBV

Acts 6 in the FEB

Acts 6 in the GGMNT

Acts 6 in the GNT

Acts 6 in the HARY

Acts 6 in the HNT

Acts 6 in the IRVA

Acts 6 in the IRVB

Acts 6 in the IRVG

Acts 6 in the IRVH

Acts 6 in the IRVK

Acts 6 in the IRVM

Acts 6 in the IRVM2

Acts 6 in the IRVO

Acts 6 in the IRVP

Acts 6 in the IRVT

Acts 6 in the IRVT2

Acts 6 in the IRVU

Acts 6 in the ISVN

Acts 6 in the JSNT

Acts 6 in the KAPI

Acts 6 in the KBT1ETNIK

Acts 6 in the KBV

Acts 6 in the KJV

Acts 6 in the KNFD

Acts 6 in the LBA

Acts 6 in the LBLA

Acts 6 in the LNT

Acts 6 in the LSV

Acts 6 in the MAAL

Acts 6 in the MBV

Acts 6 in the MBV2

Acts 6 in the MHNT

Acts 6 in the MKNFD

Acts 6 in the MNG

Acts 6 in the MNT

Acts 6 in the MNT2

Acts 6 in the MRS1T

Acts 6 in the NAA

Acts 6 in the NASB

Acts 6 in the NBLA

Acts 6 in the NBS

Acts 6 in the NBVTP

Acts 6 in the NET2

Acts 6 in the NIV11

Acts 6 in the NNT

Acts 6 in the NNT2

Acts 6 in the NNT3

Acts 6 in the PDDPT

Acts 6 in the PFNT

Acts 6 in the RMNT

Acts 6 in the SBIAS

Acts 6 in the SBIBS

Acts 6 in the SBIBS2

Acts 6 in the SBICS

Acts 6 in the SBIDS

Acts 6 in the SBIGS

Acts 6 in the SBIHS

Acts 6 in the SBIIS

Acts 6 in the SBIIS2

Acts 6 in the SBIIS3

Acts 6 in the SBIKS

Acts 6 in the SBIKS2

Acts 6 in the SBIMS

Acts 6 in the SBIOS

Acts 6 in the SBIPS

Acts 6 in the SBISS

Acts 6 in the SBITS

Acts 6 in the SBITS2

Acts 6 in the SBITS3

Acts 6 in the SBITS4

Acts 6 in the SBIUS

Acts 6 in the SBIVS

Acts 6 in the SBT

Acts 6 in the SBT1E

Acts 6 in the SCHL

Acts 6 in the SNT

Acts 6 in the SUSU

Acts 6 in the SUSU2

Acts 6 in the SYNO

Acts 6 in the TBIAOTANT

Acts 6 in the TBT1E

Acts 6 in the TBT1E2

Acts 6 in the TFTIP

Acts 6 in the TFTU

Acts 6 in the TGNTATF3T

Acts 6 in the THAI

Acts 6 in the TNFD

Acts 6 in the TNT

Acts 6 in the TNTIK

Acts 6 in the TNTIL

Acts 6 in the TNTIN

Acts 6 in the TNTIP

Acts 6 in the TNTIZ

Acts 6 in the TOMA

Acts 6 in the TTENT

Acts 6 in the UBG

Acts 6 in the UGV

Acts 6 in the UGV2

Acts 6 in the UGV3

Acts 6 in the VBL

Acts 6 in the VDCC

Acts 6 in the YALU

Acts 6 in the YAPE

Acts 6 in the YBVTP

Acts 6 in the ZBP