Deuteronomy 29 (BOGWICC)

1 Awa ndiwo mawu a mʼpangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi Aisraeli ku Mowabu, powonjezera pa pangano limene anapangana nawo ku Horebu. 2 Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati kwa iwo: Inu munaona zonse zimene Yehova anachita kwa Farao, nduna zake ndi dziko lake lonse ku Igupto. 3 Ndi maso anu munaona mayesero onse aja, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zazikulu zija. 4 Koma mpaka lero Yehova sanakupatseni mtima wozindikira kapena maso openya kapena makutu akumva. 5 Mʼzaka makumi anayi zimene ndinakutsogolerani mʼchipululu, zovala zanu ndiponso nsapato za ku mapazi anu sizinangʼambike. 6 Inu simunadye buledi ndi kumwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa. Ndinachita izi kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 7 Pamene munafika malo ano, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni ndi Ogi mfumu ya ku Basani anabwera kudzamenyana nafe koma tinawagonjetsa iwo. 8 Tinatenga dziko lawo ndi kulipereka ngati cholowa cha fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase. 9 Tsatirani mosamalitsa mawu a mʼpangano ili kuti zinthu zizikuyenderani bwino pa zochitika zanu zonse. 10 Lero lino nonse mukuyima pamaso pa Yehova Mulungu wanu, atsogoleri a mafuko anu, akuluakulu ndi nduna zanu, ndi amuna ena onse a mu Israeli, 11 pamodzi ndi ana ndi akazi anu, kudzanso alendo amene akukhala pakati panu omwe amakuwazirani nkhuni ndi kukutungirani madzi. 12 Mukuyimirira pano kuti mulowe mʼpangano ndi Yehova Mulungu wanu, pangano limene Yehova akuchita ndi inu lero ndi kulisindikiza ndi malumbiro, 13 kukukhazikitsani lero lino ngati anthu ake, ndi kuti Iye akhale Mulungu wanu monga anakulonjezani inu ndiponso monga analumbira kwa makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 14 Ndikupanga pangano ili ndi malumbiro ake osati kwa inu nokha, 15 amene muli pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu, koma ndi iwonso amene sali pano lero. 16 Inu nomwe mukudziwa mmene tinkakhalira ku Igupto ndi mmene tinadutsira mayiko pa ulendo wobwera kuno. 17 Ife tinaona pakati pawo mafanizo ndi mafano awo onyansa, amtengo ndi amiyala, asiliva ndi agolide. 18 Onetsetsani kuti pasapezeke mwamuna kapena mkazi, banja kapena fuko pakati panu lero amene mtima wawo udzapandukira Yehova Mulungu wanu ndi kupita kukapembedza milungu ya mitundu iyo. Onetsetsani kuti pasapezeke muzu pakati panu wotulutsa mankhwala akupha otere. 19 Munthu wotere akamva mawu a lumbiro ili, asadzidalitse yekha mʼmaganizo mwake namati, “Ine ndidzapulumuka ngakhale nditapitiriza kuyenda njira yanga.” Zoterezi zidzadzetsa masautso pa nthaka ya chinyontho ndi yowuma yomwe. 20 Yehova sadzamukhululukira. Mkwiyo ndi nsanje ya Yehova zidzamuyakira munthuyo. Matemberero onse wolembedwa mʼbukuli adzamugwera iye ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pa dziko lapansi. 21 Yehova adzasankha pakati pa Aisraeli anthu oyenera masautso monga mwa matemberero onse a mʼpangano olembedwa Mʼbuku la Malamulo. 22 Ana anu a mibado yakutsogolo ndi alendo amene adzachokera kutali adzaona matsoka amene adzakugwerani mʼdziko muno ndiponso matenda amene Yehova adzabweretsa pa dzikoli. 23 Dziko lonse lidzasanduka nthaka ya mchere ndi ya sulufule. Simudzadzalamo kanthu, simudzakhala chomera chilichonse, ndi mbewu yomera mʼmenemo. Dziko lanu lidzakhala lowonongeka ngati Sodomu ndi Gomora, Adima ndi Zeboimu, mizinda imene Yehova anayiwononga ndi mkwiyo wake waukulu. 24 Mitundu yonse ya anthu idzafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani Yehova anachita zotere mʼdziko lake? Kodi chifukwa chiyani anaonetsa mkwiyo woopsa wotere?” 25 Ndipo yankho la mafunso amenewa lidzakhala lakuti, “Chifukwa chakuti anthu awa aphwanya pangano la Yehova Mulungu wa makolo awo, pangano limene Iye anapangana nawo pamene anawatulutsa ku Igupto. 26 Iwo anachoka ndi kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, milungu imene sanayidziwe, milungu imene sanawapatse. 27 Choncho Yehova anakwiyira dziko lino, kotero anabweretsa matemberero onse amene analembedwa mʼbuku lino. 28 Ndi mkwiyo komanso ukali wake woopsa Yehova anawazula mʼdziko lawo ndi kuwaponyera mʼdziko lina, monga mmene zilili lero lino.” 29 Zinsinsi ndi za Yehova Mulungu wathu koma zinthu zimene zaululidwa ndi zathu ndi ana athu kwamuyaya, kuti titsatire mawu onse a mʼmalamulowa.

In Other Versions

Deuteronomy 29 in the ANGEFD

Deuteronomy 29 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 29 in the AS21

Deuteronomy 29 in the BAGH

Deuteronomy 29 in the BBPNG

Deuteronomy 29 in the BBT1E

Deuteronomy 29 in the BDS

Deuteronomy 29 in the BEV

Deuteronomy 29 in the BHAD

Deuteronomy 29 in the BIB

Deuteronomy 29 in the BLPT

Deuteronomy 29 in the BNT

Deuteronomy 29 in the BNTABOOT

Deuteronomy 29 in the BNTLV

Deuteronomy 29 in the BOATCB

Deuteronomy 29 in the BOATCB2

Deuteronomy 29 in the BOBCV

Deuteronomy 29 in the BOCNT

Deuteronomy 29 in the BOECS

Deuteronomy 29 in the BOHCB

Deuteronomy 29 in the BOHCV

Deuteronomy 29 in the BOHLNT

Deuteronomy 29 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 29 in the BOICB

Deuteronomy 29 in the BOILNTAP

Deuteronomy 29 in the BOITCV

Deuteronomy 29 in the BOKCV

Deuteronomy 29 in the BOKCV2

Deuteronomy 29 in the BOKHWOG

Deuteronomy 29 in the BOKSSV

Deuteronomy 29 in the BOLCB

Deuteronomy 29 in the BOLCB2

Deuteronomy 29 in the BOMCV

Deuteronomy 29 in the BONAV

Deuteronomy 29 in the BONCB

Deuteronomy 29 in the BONLT

Deuteronomy 29 in the BONUT2

Deuteronomy 29 in the BOPLNT

Deuteronomy 29 in the BOSCB

Deuteronomy 29 in the BOSNC

Deuteronomy 29 in the BOTLNT

Deuteronomy 29 in the BOVCB

Deuteronomy 29 in the BOYCB

Deuteronomy 29 in the BPBB

Deuteronomy 29 in the BPH

Deuteronomy 29 in the BSB

Deuteronomy 29 in the CCB

Deuteronomy 29 in the CUV

Deuteronomy 29 in the CUVS

Deuteronomy 29 in the DBT

Deuteronomy 29 in the DGDNT

Deuteronomy 29 in the DHNT

Deuteronomy 29 in the DNT

Deuteronomy 29 in the ELBE

Deuteronomy 29 in the EMTV

Deuteronomy 29 in the ESV

Deuteronomy 29 in the FBV

Deuteronomy 29 in the FEB

Deuteronomy 29 in the GGMNT

Deuteronomy 29 in the GNT

Deuteronomy 29 in the HARY

Deuteronomy 29 in the HNT

Deuteronomy 29 in the IRVA

Deuteronomy 29 in the IRVB

Deuteronomy 29 in the IRVG

Deuteronomy 29 in the IRVH

Deuteronomy 29 in the IRVK

Deuteronomy 29 in the IRVM

Deuteronomy 29 in the IRVM2

Deuteronomy 29 in the IRVO

Deuteronomy 29 in the IRVP

Deuteronomy 29 in the IRVT

Deuteronomy 29 in the IRVT2

Deuteronomy 29 in the IRVU

Deuteronomy 29 in the ISVN

Deuteronomy 29 in the JSNT

Deuteronomy 29 in the KAPI

Deuteronomy 29 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 29 in the KBV

Deuteronomy 29 in the KJV

Deuteronomy 29 in the KNFD

Deuteronomy 29 in the LBA

Deuteronomy 29 in the LBLA

Deuteronomy 29 in the LNT

Deuteronomy 29 in the LSV

Deuteronomy 29 in the MAAL

Deuteronomy 29 in the MBV

Deuteronomy 29 in the MBV2

Deuteronomy 29 in the MHNT

Deuteronomy 29 in the MKNFD

Deuteronomy 29 in the MNG

Deuteronomy 29 in the MNT

Deuteronomy 29 in the MNT2

Deuteronomy 29 in the MRS1T

Deuteronomy 29 in the NAA

Deuteronomy 29 in the NASB

Deuteronomy 29 in the NBLA

Deuteronomy 29 in the NBS

Deuteronomy 29 in the NBVTP

Deuteronomy 29 in the NET2

Deuteronomy 29 in the NIV11

Deuteronomy 29 in the NNT

Deuteronomy 29 in the NNT2

Deuteronomy 29 in the NNT3

Deuteronomy 29 in the PDDPT

Deuteronomy 29 in the PFNT

Deuteronomy 29 in the RMNT

Deuteronomy 29 in the SBIAS

Deuteronomy 29 in the SBIBS

Deuteronomy 29 in the SBIBS2

Deuteronomy 29 in the SBICS

Deuteronomy 29 in the SBIDS

Deuteronomy 29 in the SBIGS

Deuteronomy 29 in the SBIHS

Deuteronomy 29 in the SBIIS

Deuteronomy 29 in the SBIIS2

Deuteronomy 29 in the SBIIS3

Deuteronomy 29 in the SBIKS

Deuteronomy 29 in the SBIKS2

Deuteronomy 29 in the SBIMS

Deuteronomy 29 in the SBIOS

Deuteronomy 29 in the SBIPS

Deuteronomy 29 in the SBISS

Deuteronomy 29 in the SBITS

Deuteronomy 29 in the SBITS2

Deuteronomy 29 in the SBITS3

Deuteronomy 29 in the SBITS4

Deuteronomy 29 in the SBIUS

Deuteronomy 29 in the SBIVS

Deuteronomy 29 in the SBT

Deuteronomy 29 in the SBT1E

Deuteronomy 29 in the SCHL

Deuteronomy 29 in the SNT

Deuteronomy 29 in the SUSU

Deuteronomy 29 in the SUSU2

Deuteronomy 29 in the SYNO

Deuteronomy 29 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 29 in the TBT1E

Deuteronomy 29 in the TBT1E2

Deuteronomy 29 in the TFTIP

Deuteronomy 29 in the TFTU

Deuteronomy 29 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 29 in the THAI

Deuteronomy 29 in the TNFD

Deuteronomy 29 in the TNT

Deuteronomy 29 in the TNTIK

Deuteronomy 29 in the TNTIL

Deuteronomy 29 in the TNTIN

Deuteronomy 29 in the TNTIP

Deuteronomy 29 in the TNTIZ

Deuteronomy 29 in the TOMA

Deuteronomy 29 in the TTENT

Deuteronomy 29 in the UBG

Deuteronomy 29 in the UGV

Deuteronomy 29 in the UGV2

Deuteronomy 29 in the UGV3

Deuteronomy 29 in the VBL

Deuteronomy 29 in the VDCC

Deuteronomy 29 in the YALU

Deuteronomy 29 in the YAPE

Deuteronomy 29 in the YBVTP

Deuteronomy 29 in the ZBP