Ecclesiastes 7 (BOGWICC)

1 Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino,ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa. 2 Kuli bwino kupita ku nyumba yamalirokusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero:Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense;anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo. 3 Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka,pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima. 4 Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa,koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo. 5 Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzerukusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru. 6 Kuseka kwa zitsiru kuli ngatikuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika,izinso ndi zopandapake. 7 Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru,ndipo chiphuphu chimawononga mtima. 8 Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake,ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza. 9 Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako,pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru. 10 Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?”pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa. 11 Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwinondipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano. 12 Nzeru ndi chitetezo,monganso ndalama zili chitetezo,koma phindu la chidziwitso ndi ili:kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo. 13 Taganizirani zimene Mulungu wazichita:ndani angathe kuwongola chinthuchimene Iye anachipanga chokhota? 14 Pamene zinthu zili bwino, sangalala;koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino:Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo,ndiponso nthawi imene si yabwinoyo.Choncho munthu sangathe kuzindikirachilichonse cha mʼtsogolo mwake. 15 Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi:munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake,ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake. 16 Usakhale wolungama kwambirikapena wanzeru kwambiri,udziwonongerenji wekha? 17 Usakhale woyipa kwambiri,ndipo usakhale chitsiru,uferenji nthawi yako isanakwane? 18 Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi,ndipo usataye njira inayo.Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi. 19 Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzerukupambana olamulira khumi a mu mzinda. 20 Palibe munthu wolungama pa dziko lapansiamene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa. 21 Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula,mwina udzamva wantchito wako akukutukwana, 22 pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwakokuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena. 23 Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati,“Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,”koma nzeruyo inanditalikira. 24 Nzeru zimene zilipo,zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri,ndani angathe kuzidziwa? 25 Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe,ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalirandipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsirundiponso kupusa kwake kwa misala. 26 Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa,mkazi amene ali ngati khoka,amene mtima wake uli ngati khwekhwe,ndipo manja ake ali ngati maunyolo.Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo,koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa. 27 Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi:“Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira, 28 pamene ine ndinali kufufuzabekoma osapeza kanthu,ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000,koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama. 29 Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi:Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama,koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”

In Other Versions

Ecclesiastes 7 in the ANGEFD

Ecclesiastes 7 in the ANTPNG2D

Ecclesiastes 7 in the AS21

Ecclesiastes 7 in the BAGH

Ecclesiastes 7 in the BBPNG

Ecclesiastes 7 in the BBT1E

Ecclesiastes 7 in the BDS

Ecclesiastes 7 in the BEV

Ecclesiastes 7 in the BHAD

Ecclesiastes 7 in the BIB

Ecclesiastes 7 in the BLPT

Ecclesiastes 7 in the BNT

Ecclesiastes 7 in the BNTABOOT

Ecclesiastes 7 in the BNTLV

Ecclesiastes 7 in the BOATCB

Ecclesiastes 7 in the BOATCB2

Ecclesiastes 7 in the BOBCV

Ecclesiastes 7 in the BOCNT

Ecclesiastes 7 in the BOECS

Ecclesiastes 7 in the BOHCB

Ecclesiastes 7 in the BOHCV

Ecclesiastes 7 in the BOHLNT

Ecclesiastes 7 in the BOHNTLTAL

Ecclesiastes 7 in the BOICB

Ecclesiastes 7 in the BOILNTAP

Ecclesiastes 7 in the BOITCV

Ecclesiastes 7 in the BOKCV

Ecclesiastes 7 in the BOKCV2

Ecclesiastes 7 in the BOKHWOG

Ecclesiastes 7 in the BOKSSV

Ecclesiastes 7 in the BOLCB

Ecclesiastes 7 in the BOLCB2

Ecclesiastes 7 in the BOMCV

Ecclesiastes 7 in the BONAV

Ecclesiastes 7 in the BONCB

Ecclesiastes 7 in the BONLT

Ecclesiastes 7 in the BONUT2

Ecclesiastes 7 in the BOPLNT

Ecclesiastes 7 in the BOSCB

Ecclesiastes 7 in the BOSNC

Ecclesiastes 7 in the BOTLNT

Ecclesiastes 7 in the BOVCB

Ecclesiastes 7 in the BOYCB

Ecclesiastes 7 in the BPBB

Ecclesiastes 7 in the BPH

Ecclesiastes 7 in the BSB

Ecclesiastes 7 in the CCB

Ecclesiastes 7 in the CUV

Ecclesiastes 7 in the CUVS

Ecclesiastes 7 in the DBT

Ecclesiastes 7 in the DGDNT

Ecclesiastes 7 in the DHNT

Ecclesiastes 7 in the DNT

Ecclesiastes 7 in the ELBE

Ecclesiastes 7 in the EMTV

Ecclesiastes 7 in the ESV

Ecclesiastes 7 in the FBV

Ecclesiastes 7 in the FEB

Ecclesiastes 7 in the GGMNT

Ecclesiastes 7 in the GNT

Ecclesiastes 7 in the HARY

Ecclesiastes 7 in the HNT

Ecclesiastes 7 in the IRVA

Ecclesiastes 7 in the IRVB

Ecclesiastes 7 in the IRVG

Ecclesiastes 7 in the IRVH

Ecclesiastes 7 in the IRVK

Ecclesiastes 7 in the IRVM

Ecclesiastes 7 in the IRVM2

Ecclesiastes 7 in the IRVO

Ecclesiastes 7 in the IRVP

Ecclesiastes 7 in the IRVT

Ecclesiastes 7 in the IRVT2

Ecclesiastes 7 in the IRVU

Ecclesiastes 7 in the ISVN

Ecclesiastes 7 in the JSNT

Ecclesiastes 7 in the KAPI

Ecclesiastes 7 in the KBT1ETNIK

Ecclesiastes 7 in the KBV

Ecclesiastes 7 in the KJV

Ecclesiastes 7 in the KNFD

Ecclesiastes 7 in the LBA

Ecclesiastes 7 in the LBLA

Ecclesiastes 7 in the LNT

Ecclesiastes 7 in the LSV

Ecclesiastes 7 in the MAAL

Ecclesiastes 7 in the MBV

Ecclesiastes 7 in the MBV2

Ecclesiastes 7 in the MHNT

Ecclesiastes 7 in the MKNFD

Ecclesiastes 7 in the MNG

Ecclesiastes 7 in the MNT

Ecclesiastes 7 in the MNT2

Ecclesiastes 7 in the MRS1T

Ecclesiastes 7 in the NAA

Ecclesiastes 7 in the NASB

Ecclesiastes 7 in the NBLA

Ecclesiastes 7 in the NBS

Ecclesiastes 7 in the NBVTP

Ecclesiastes 7 in the NET2

Ecclesiastes 7 in the NIV11

Ecclesiastes 7 in the NNT

Ecclesiastes 7 in the NNT2

Ecclesiastes 7 in the NNT3

Ecclesiastes 7 in the PDDPT

Ecclesiastes 7 in the PFNT

Ecclesiastes 7 in the RMNT

Ecclesiastes 7 in the SBIAS

Ecclesiastes 7 in the SBIBS

Ecclesiastes 7 in the SBIBS2

Ecclesiastes 7 in the SBICS

Ecclesiastes 7 in the SBIDS

Ecclesiastes 7 in the SBIGS

Ecclesiastes 7 in the SBIHS

Ecclesiastes 7 in the SBIIS

Ecclesiastes 7 in the SBIIS2

Ecclesiastes 7 in the SBIIS3

Ecclesiastes 7 in the SBIKS

Ecclesiastes 7 in the SBIKS2

Ecclesiastes 7 in the SBIMS

Ecclesiastes 7 in the SBIOS

Ecclesiastes 7 in the SBIPS

Ecclesiastes 7 in the SBISS

Ecclesiastes 7 in the SBITS

Ecclesiastes 7 in the SBITS2

Ecclesiastes 7 in the SBITS3

Ecclesiastes 7 in the SBITS4

Ecclesiastes 7 in the SBIUS

Ecclesiastes 7 in the SBIVS

Ecclesiastes 7 in the SBT

Ecclesiastes 7 in the SBT1E

Ecclesiastes 7 in the SCHL

Ecclesiastes 7 in the SNT

Ecclesiastes 7 in the SUSU

Ecclesiastes 7 in the SUSU2

Ecclesiastes 7 in the SYNO

Ecclesiastes 7 in the TBIAOTANT

Ecclesiastes 7 in the TBT1E

Ecclesiastes 7 in the TBT1E2

Ecclesiastes 7 in the TFTIP

Ecclesiastes 7 in the TFTU

Ecclesiastes 7 in the TGNTATF3T

Ecclesiastes 7 in the THAI

Ecclesiastes 7 in the TNFD

Ecclesiastes 7 in the TNT

Ecclesiastes 7 in the TNTIK

Ecclesiastes 7 in the TNTIL

Ecclesiastes 7 in the TNTIN

Ecclesiastes 7 in the TNTIP

Ecclesiastes 7 in the TNTIZ

Ecclesiastes 7 in the TOMA

Ecclesiastes 7 in the TTENT

Ecclesiastes 7 in the UBG

Ecclesiastes 7 in the UGV

Ecclesiastes 7 in the UGV2

Ecclesiastes 7 in the UGV3

Ecclesiastes 7 in the VBL

Ecclesiastes 7 in the VDCC

Ecclesiastes 7 in the YALU

Ecclesiastes 7 in the YAPE

Ecclesiastes 7 in the YBVTP

Ecclesiastes 7 in the ZBP